You are on page 1of 61

1

TANTHAUZO LA SURAT AL FATIHAH


Wolemba:
Muhammad Abdul Karim Duncan
Malawi Ummah


2







__________________________
TANTHAUZO LA SURAT AL FATIHAH





Wolemba:
Muhammad Abdul Karim Duncan


3






Chitetezo cha bukuli
Gawo lirilonse la bukuli silikuloredwa kusindikizidwa
kachiwiri popanda chilorezo cholembedwa
kuchokera kwa mlembi kapena
msindikizi.
karim@malawiummah.com
info@malawiummah.com
MALAWI UMMAH
www.malawiummah.com



4
ZA NKATIMU
Mawu oyamba...................5
Surat Al Fatihah......10
Ndime 1.........13
Bismillah.............15
Al Rahman Al Rahim..........17
Ndime 2.............22
Al Hamdulillah........22
Rabbil alamin........26
Ndime 3.........30
Al Rahman Al Rahim.........30
Ndime 4.................31
Yawmiddin......................34
Din..........40
Ndime 5.....44
Iyyaka nabudu............................45
Wa iyyaka nastain..........46
Ndime 6.....49
Ihdinas siraatal mustaqim.49
Ndime 7.....53
Siraatalladhina anamta alayhim..........53
Ghayril magh-dhubi alayhim.........57
Waladh-dhaallin......58
Ameen.......59


5

>


M'dzina la Mulungu Wachifundo Chambiri, Wachisoni.
MAWU OYAMBA
Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, amene adabvumbulutsa
Buku lolemekezeka la Quran, lomwe likufotokoza za chinthu
china chirichonse mwatsatanetsatane. Mtendere ndi madalitso
zipite kwa Mtumiki womaliza Muhammad (SAW) pamodzi ndi
omutsatira ake onse kufikira pa tsiku lachiweruzo.
Mulungu adabvumbulutsa Quran kuti imutsogolere munthu
muchowonadi, imupezetse madalitso ndi mtendere,
iwachenjeze anthu ochimwa za moto wa Jahannam, komanso
nkhani yosangalatsa ya Jannah kwa ochita zabwino.

>

) 89 (
Ndiponso takuvumbulutsira Buku ili lomwe likufotokoza za
chinthu chirichonse lomwenso ndi chiongoko ndi mtendere
ndiponso ndi nkhani yosangalatsa kwa ogonjera (Mulungu).
Kuyangana chabe mawu a mu Quran kumabweretsa madalitso,
sitikufunikira kulekera pomwepo, koma tiyeneranso
kuyiwerenga chifukwa kuwerenga Quran kumabweretsa
madalitso komanso malipiro abwino pa chilembo chirichonse


6
chimene munthu akuwerenga. Tisangowerenga chabe koma
tikufunikanso kuphunzira matanthauzo, tikadziwa matanthauzo
tisayimire pomwepo koma kugwiritsa ntchito zimene tamva.
Pomaliza tiyenera kuchedwa ndi kulingalira mau a Mulunguwa
ndime ndi ndime, liwu ndi liwu, mukuchita zimenezi
tidzazindikira kuti Quraniyi yafotokozadi za chinthu china
chirichonse. Tidzapeza kuti moyo wathu wonse wa tsiku ndi
tsiku uli mu Quran, zinthu zonse zamakono (Science) za
mitundu yonse tizipeza zili mu Quran. Koma zonsezi kuti
tizipeze mu Quran tiyenera kulingalira ndi kuganiza mozama za
matanthauzo a Quran, zimenezo ndizomwenso Mulungu
akutilamulira mu Surah 38 (Saad) ndime 29:

) 29 (
(Ili), ndibuku lochuluka madalitso lomwe talivumbulutsa kwa
iwe kuti (anthu) azame kwambiri pomvetsetsa ndime zake; ndi
kuti apeze nalo phunziro eni nzeru.
Tikulamulidwa kuti tizame pomvetsetsa matanthauza a Quran,
mukutero tiphunzira zinthu zambiri.
Mwachitsanzo, tikamafuna kuyeza kutalika kwa chinthu
chachingono timagwiritsa ntchito ma Millimetre (mm),
chokulirapo timagwiritsa ntchito ma Centimetre (cm).
Chachitali kwambiri timagwiritsa ntchito ma Metre (m). Mtunda
ukatalika kwambiri timagwiritsa ntchito ma Kilometre kapena
ma Mile.


7
Zonse tatchulazi zikugwiritsidwa ntchito poyeza mtunda
wochoka malo kufika malo ena. Tikamawerenga ma buku omwe
amakamba za mlengalenga, amatiuza kuti mtunda wochoka
Galaxy (gulu la nyenyezi) kukafika Galaxy ina ndiwautali
kwambiri, choncho mmalo mogwiritsa ntchito zoyezera mtunda
timagwiritsa ntchito chimodzi mwa zoyezera nthawi chomwe
chiri chaka, chimatchedwa kuti Light Year
1
. Izi zili choncho
chifukwa mtunda wautali kwambiri umayezedwa pogwiritsa
ntchito nthawi.
Tikawerenga Surah 3 (Aali Imran) ndime 30, tikupeza kuti
Quran ndi imene idayambilira kugwiritsa ntchito nthawi poyeza
mtunda anthu a Science asadazitulukire:

) 30 (
"Tsiku lomwe mzimu uliwonse udzapeza zabwino zomwe
udachita zitabweretsedwa, ndiponso zoipa zomwe udachita;
udzalakalaka kuti pakadakhala mtunda wautali pakati pa
machimo ake ndi iye. Ndipo Mulungu Mwini akukuchenjezani za
chilango Chake. Ndipo Mulungu ndiwoleza kwa akapolo Ake.

1
Light Year ndi mtunda womwe kuwala (Light) kumayenda pa chaka chimodzi.
Timamva kuti kuwala kumatha mtunda wokwana pafupifupi 300,000km mu second
imodzi, ndiye kuti pa chaka chimodzi kuwala kumatha mtunda wokwana pafupifupi
9,460,800,000,000km. Kuchoka pa Galaxy yathu kufika pa Galaxy yomwe
yayandikana nayo kwambiri pali mtunda wokwana 180,000 Light Year. Kuti tiyike
mma Kilometres itipatsa nambala yaitali kwambiri, choncho tagwiritsa ntchito nthawi
poyeza mtunda.


8
Titenge mawu oti: Udzalakalaka (mzimu) kuti pakadakhala
mtunda wautali pakati pa machimo ake ndi iye.
Mawu oti:

amadan baidan ndi amene akutathauza


kuti mtunda wautali. Tanthauzo lenileni la mawu amenewa
mchichewa ndi Nthawi yaitali koma otanthauzira akutiwuza
kuti Mtunda wautali. Quran yagwiritsa ntchito nthawi poyeza
mtunda.
Quran yagwiritsa ntchito nthawi ponena zamtunda umene
munthu akalakelake kuti atalikane ndi machimo ake, chifukwa
chakuti mtunda wake ndiwautali kwambiri siwungayezedwe ndi
ma metre kapena ma kilometre.
Choncho amene awerenge chabe tanthauzo la ndimeyi adziwa
kuti ndi mtunda wautali, koma amene awerenge ndikulingalira
tanthauzolo mozama adziwa kuti mtundawu ndiwautali koposa,
ndipo akhala woopa kuti ngati munthu akalakelake kuti
atalikane ndi machimo ake mtunda ngati umenewo ndiye kuti
machimowo adzakhala oipa kwambiri choncho adzakhala
wopewa machimo ndi woopa Mulungu. Ndichifukwa chake
timapeza ndime 28 mu Surah 35 (Faatir) ikutiuza kuti:

... ) 28 (
Ndithu odziwa ndi amene amamuopa Mulungu mwa akapolo
Ake.


9
Chifukwa chakuti odziwawo akudziwa zomwe zili mkati mwa
ndime zimenezi choncho amakhala oopa.
Choncho ndikofunikira kuti tidzilingalira ndi kuzama
pomvetsetsa mawu a mu Quran.
Chifukwa chakuti Surat Al Fatihah ndi Surah yoyamba komanso
ndi imene pafupifupi aliyense amawerenga pa Salat, ndidaona
kuti ndichanzeru kuyamba kulemba ndikufotokoza matanthauzo
ake. Bukuli lomwe ndidayamba kulemba pa 1 Muharram 1435
Hijri, pomwe padali pa 5 November 2013, likutchedwa kuti:
Ndime7 kutengera nambala ya ndime za Surayi.
Ndikuthokoza mwapadera anthu awa amene ndimathandizana
nawo kuti buku limeneri litheke: Sheikh Hassam Dullah,
Jamila Jafar ndi Ramadhan Issah. Tikupempha Mulungu kuti
ationjezere kuzindikira ndi nzeru ndikuti uthenga umenewu
ukhale wothandiza ndi wa phindu pa dziko pano komanso moyo
uli nkudza, Ameen.
____________________________
Muhammad Abdul Karim Duncan
Al Azhar University





10

>



SURAT AL FATIHAH
Surat Al Fatihah ndi Surah yachisanu (5) kutsika
(kubvumbulutsidwa) kwa Mtumiki Muhammad (SAW)
1
, koma
ndi Surah yoyamba mundondomeko ya Buku la Quran. Surayi
ili ndi ndime (Ayah) zokwana zisanu ndi ziwiri (7). Mu Salah
zonse zisanu patsiku, munthu amawerenga Surayi kokwana
khumi ndi kasanu ndi kawiri (17) patsiku. Surat Al Fatihah
idatsikira ku Makkah, ena amati idatsikira ku Madinah Mtumiki
(SAW) atasamuka kuchoka ku Makkah, koma zoona ndi zoti
Surayi idatsikira ku Makkah Mtumiki (SAW) asadasamuke
kupita ku Madinah. Umboni wake ndi Surah 15 (Al Hijr) ndime
87 imene ikunena kuti:

) 87 (
Ndipo ndithu, takupatsa (Aya izi) zisanu ndi ziwiri
zomawerenga kawirikawiri, (Surat Fatihah), ndi Qur'an
yolemekezeka.

1
Zimanenedwa kuti Surah imeneyi idatsika pa nthawi imene Mtumiki (SAW) amamva
kuitana kuti: E! Muhammad. Mtumiki (SAW) amati akamva mau oyitanawa
amachoka pa malopo mofulumira. Munthu wina wotchedwa Warqah adamuwuza
Mtumiki (SAW) kuti akamvanso kuitanako akhale tchelu kuti amve zimene oyitanayo
akufuna kunena. Pamene adamvanso kuyitanako Mtumiki (SAW) adayankha kuti:
Labbayka! Kenako mauwo adati: Nena kuti: Ash-hadu an laa ilaaha illallaahu wa
anna Muhammadan rasulullaah. (Ndikuyikira umboni kuti palibe Mulungu wina
wachoona koma Allah, ndipo ndithu, Muhammad ndi Mtenga Wake.) Kenako adati:
Nena: [Alhamdulillahi rabbil aalamin. Al rahmanir rahim.Maliki
yawmiddin.]mpaka adamaliza Surat Al Fatiha.


11
Ayah zisanu ndi ziwiri (7) zimenezi ndi za mu Surat Al Fatihah.
Surat Al Hijr imene ikukamba za Surat Al Fatihayi idatsikira ku
Makkah, choncho ndizosamveka kuti Surat Al Hijr ikambe za
Surah yoti sidatsike.
Surat Al Fatihah ili ndi mayina ambiri, ena mwa iwo omwe ali
odziwika bwino ndi:-Fatihatul Kitab, Ummul Quran ndi
Assabul Mathani.
Fatihatul Kitab: Yotsegulira Buku (la Quran),
imatchedwa chonchi chifukwa ndiyoyambilira mu Buku
la Quran.
Assabul Mathani: (Ndime) zisanu ndi ziwiri (7)
zobwerezedwa, imatchedwa chonchi chifukwa ndi ndime
zisanu ndi ziwiri zokhazo zomwe zimabwerezedwa
ndikuwerengedwa kawirikawiri pa Salah.
Ummul Quran: Kholo la Quran, imatchedwa chonchi
pazifukwa zatchulidwa mmwambazo.
Surayi imatchedwanso kuti Surat Al Hamdu (Yotamanda
Mulungu), Surat Ash-Shifaa (yochiza matenda), Surat As-
Salah (chifukwa chakuti Salah simalandiridwa popanda
kuwerenga Surayi) Mtumiki (SAW) akunena kuti:
Amene wapemphera Salah ndipo sadawerenge Kholo la Quran
(Al Fatihah) Salatiyo ndiyosakwana
Mulungu mu Hadith Qudsi akunena kuti:
Ndayigawa Salah pakati pa Ine ndi kapolo Wanga mmatheka
awiri, ndipo kapolo Wanga apeza zimene apemphe. Kapolo
akanena kuti Alhamdulillahi rabbil alamin (Kutamandidwa


12
konse ndi kwa Mulungu Mbuye Wa zolengedwa zonse),
Mulungu amanena kuti: Wandiyamika kapolo Wanga.
(Kapolo) akanena kuti: Al rahmanir rahim (Wachifundo
chambiri Wachisoni chosatha). Mulungu amanena kuti:
Wanditamanda kapolo Wanga. Akanena kuti: Maaliki
yuwmiddin (Mwini tsiku la chiweruzo). Mulungu amati:
Wandikweza kapolo Wanga. Akanena kuti: Iyyaka nabudu
wa iyyaka nastain (Inu nokha tikukupembedzani ndiponso Inu
nokha tikukupemphani chithandizo). Mulungu amati: Izi ndi
za pakati pa Ine ndi kapolo Wanga ndipo kapolo Wanga apeza
zimene apemphe. Akanena kuti: Ihdinas siraatal mustaqim,
siraatalladhina anamta alayhim, ghayril magh-dhubi
alayhim waladh-dhaallin (Tiongolereni ku njira yoongoka.
Njira ya omwe mudawapatsa chisomo, osati ya amene
adakwiyiridwa (ndi Inu) osatinso ya omwe adasokera).
Mulungu amanena kuti: Izi ndi za kapolo Wanga ndipo kapolo
Wanga apatsidwa zimene wapempha.
Tikaonetsetsa bwino mu Hadithiyi Mulungu akuti: Ndayigawa
Salahkoma imene tamva ikugawidwa ndi Surat Al Fatihah,
chifukwa choti Surayi ndi kholo la Salah, Salah simalandiridwa
popanda kuwerenga Al Fatihah.



13
NDIME 1
(Ndime Yoyamba)

>

) 1 (
Bismillahir Rahmanir Rahim
(1) M'dzina la Mulungu Wachifundo Chambiri, Wachisoni.
Mukatsekula Buku la Quran mupeza kuti kumayambiliro kwa
Surah iliyonse kuli mau amenewa oti:

>


Bismillahir Rahmanir Rahim kupatula Surat At-Tawbah. Umo
ndi momwe Quran idabvumbulutsidwira.Choncho munthu
ayenera kuyamba ndi mawuwa asadayambe kuwerenga kapena
kulemba ndimeza Buku la Quran.
Mbiri ya Mtumiki Muhammad (SAW) imafotokoza kuti:
M'ngelo Jibril (AS) adawonekera kwa Mtumiki Muhammad
(SAW) panthawi imene iye adali ku phanga lotchedwa Hiraa.
Jibril (a) adati kwa Mtumiki Muhammad (saw): ''Werenga!''
pokhala munthu oti sadaphunzire kulemba kapena kuwerenga,
iye adati ''Ine sinditha kuwerenga.'' Koma pofuna kukwaniritsa
zomwe watumidwa ndi Mulungu, Jibril adamukakamiza
Mtumiki (SAW) kuti awerenge nati: Werenga. Munthu
ukawuzidwa kuti Werenga ndiye kuti zowerengazo mwina zili
mmutu udaloweza kapena zalembedwa penapake kuti uzionera
ndikumawerenga. Mulimonsemo, Mtumiki (SAW) zidamuvuta
kuti awerenge chifukwa adalibe zimene adaloweza komanso


14
ngakhale zikadalembedwa penapake sakadatha kuwerenga
chifukwa iye sadaphunzire kuwerenga, choncho iye Mtumiki
(SAW) adamuwuzanso Jibril (AS) kuti: Ine sinditha
kuwerenga. Koma Jibril (AS) atamva kuti iye samatha
kuwerenga adakakamirabe kumuwuza Mtumiki (SAW) kuti:
Werenga Ndichifukwa chiyani Jibril (AS) atamva kuti
Mtumiki (SAW) samatha kuwerenga adalimbikirabe kumuwuza
kuti: Werenga? Chifukwa chakuti Jibril (AS) amamudziwa
Mulungu kuti ndi Wakutha kupanga chirichonse, choncho
kudali kumuwuza Mtumiki (SAW) kuti iwe Muhammad!
(SAW) ngakhale uli wosatha kuwerenga, koma ngati uwerenge
mdzina la Mulungu, ukwanitsa kuwerenga. Choncho Jibril
(AS) adamuwuza Mtumiki (SAW) kuti awerenge mdzina la
Mulungu, adati:

) 1 (
Werenga!Mdzina la Mbuye Wako yemwe adalenga
(zolengedwa zonse).[Quran 96:1] mpaka kufikira ndime
yachisanu mu Surayi.
Mau akuti

>

Bismillahir rahmanir rahim


Kumayambiliro kwa Surat Al Fatiha ali ndi nambala (1) pamene
kumayambiliro kwa surah zina zonse mauwaalibe nambala. Izi
zili choncho chifukwa mauwa mu Surah Al Fatiha ndi ndime
yoyamba. Pamene mma Surah ena onse mauwa samatengedwa
kuti ndi Ndime (Ayah) kupatula Bismillah amene akupezeka mu
Surah 27 (An Naml) ndime 30:


15

>

) 30 (
Yachokera kwa Sulaiman, ndipo mawu ake ndi awa: M'dzina
la Mulungu, Wachifundo Chambiri, Wachisoni.
Ena amati Bismillah mu Surat Al Fatihah sindime yoyamba
ndipo ndime yoyamba mu Surayi ndi Alhamdulillahi rabbil
aalamin. Kutengera mu Surat Al Hijr kuti ndime 87:Ndipo
ndithu, takupatsa (Aya izi) zisanu ndi ziwiri zomawerenga
kawirikawiri, (Surat Fatihah), ndi Qur'an yolemekezeka.Surayi
ndime zake ndi 7, ndipo amene amati Bismillah sindime mu
Surayi amagawa ndime yomaliza mu Surayi pawiri motere:-

) 6 (
6-Njira ya omwe mudawapatsa chisomo.

) 7 (
7-Osati ya amene adakwiyiridwa (ndi Inu) osatinso ya omwe
adasokera.
Choncho amakwana ma Ayah asanu ndi awiri (7).
Bismillah
Mdzina la Mulungu
Bismillah ndi chiganizo chomwe chili ndi mau atatu m'kati
mwake.Mau ake ali motere: Bi-Ismi-Allah. Akaphatikizidwa,
I wa kumayambiliro kwa Ismi, pamodzi ndi A wa
kumayambiliro kwa Allah amachotsedwa ndipo mawu onse
pamodzi amalembedwa motere: Bi-smi-llah (Bismillah)
kutanthauza kuti Mdzina la Mulungu


16
Dzina loti: Allah ndi la Iye Yekha Wapamwambamwamba,
ndipo sikoloredwa kumutcha wina aliyense kapena china
chirichonse ndi dzina loti: Allah.
Cholinga choyamba kunena kuti Bismillah Mdzina la
Mulungu pochita zinthu ndichani?
Kunena kuti Mdzina la Mulungu zimatanthauza kuti
chirichonse chimene tikufuna kupangacho tikuchiyamba
mdzina la Mulungu. Mwachitsanzo: Ndikuyamba kuwerenga
Quraniyi mdzina la Mulungu, Ndikuyamba kulemba mdzina la
Mulungu, Ndikuyamba kudya mdzina la Mulungu, Ndikutsekula
chitsekochi mdzina la Mulungu, Ndikuyamba kulankhula
mdzina la Mulungu, ndi zina zotero.
Cholinga choyamba kuwerenga Quran kapena kuchita chinthu
chirichonse ndi dzina la Mulungu chimakhala kupempha
madalitso kwa Mulungu, chitetezo ndi chithandizo, kuti
Mulungu achitheketse ngati chili chosatheka, achifewetse
kapena kuchiphweketsa ngati chili cholimba kapena chovuta.
Mwachitsanzo ngati tikuwerenga Quran timayamba ndi
Bismillah kuti Mulungu atidalitse poyipanga Quraniyo kuti
ikhazikike mmitima mwathu, itiwongolere ndikuti ikhale
mankhwala ndi mchizo wa matenda a mumtima komanso
matenda ena aliwonse. Mu Surah 17 (Al Israa) ndime 82,
Mulungu akuti:

>

) 82 (


17
Ndipo tikuitumiza Qur'an yomwe imachiritsa (matenda a
mmitima) ndiponso ndi chifundo kwa okhulupirira...
Ngati chili chakudya, kuti Mulungu achidalitse, chigwire ntchito
yake moyenelera mthupi ndi kuti ngati chakudyacho chili ndi
zoipa monga tizilombo toyambitsa matenda kapena mankhwala
monga Poisoni, kuti Mulungu atiteteze ku zoipazo. Ngati ili
ntchito kuti Mulungu aipange kukhala yofewa komanso
yaphindu ndi zina zotero. Kuwerenga Bismillah kumakhalanso
kupempha chitetezo kwa Mulungu kuti atiteteze ku Shaytan
(Satana) ndi ma Jini oipa komanso anthu ochita zaufiti
(matsenga) ndi ochita nsanje kapena zoipa zina zilizonse.
Mtumiki (SAW) adati:
Ntchito iliyonse yomwe sidayambe ndi Bismillahir rahmanir
rahim ndiyopanda madalitso.
Pomaliza, munthu akazolowera kuyamba chirichonse ndi
Bismillah, amakhala woopa kupanga chinthu popanda kuyamba
ndi Bismillah, choncho sangapange chinthu choipa chifukwa
choipa sangayambe ndi Bismillah.
Dzina loti Allah sililoredwa kumutcha wina aliyense koma
Mulungu yekha.
Al Rahman Al Rahim
Wachifundo chambiri, Wachisoni (chosatha).
Al Rahman ndi Al Rahim ndi maina awiri mmaina 99 a
Mulungu.
Mawu oti Al Rahman ndi Al Rahim amachokera ku liwu loti
Rahmah kutanthauza kuti Chifundo. Wachifundo


18
amatchedwa kuti Raahim, wachifundo chambiri kapena
wachifundo kwambiri amatchedwa kuti Rahmaan kapena kuti
Rahiim amene ali Mulungu Yekha. Kufikira pamenepa
tadziwa kuti Al Rahman ndi Al Rahim mawu onse awiri
amatanthauza kuti Wachifundo kwambiri, chambiri kapena
choposa, chatsala ndichoti tidziwe kusiyana kwa mawu awiriwa.
Ena amati Al Rahman ndiko kuti Mulungu ndi Wachifundo
chambiri pa Iye Yekha ngakhale patapanda kupezeka owachitira
chifundocho, Iye Mbiri Yake ndiyoti: Wachifundo Chambiri
Adali Wachifundo wochitiridwa chifundowo asadalengedwe,
ndipo ndi Wachifundo komanso adzakhala Wachifundo mpaka
muyaya. Kuti zimveke bwino tipereke chitsanzo cha munthu
amene wamaliza maphunziro ake a udokotala, yemwe
sadayambe kugwira ntchito yake ya udokotala. Ngakhale
sadagwireko ntchito ya udokotala, komanso sadachiritseko
odwala, timamutchabe kuti Dokotala. Panthawi imeneyi
tikumutcha kuti Dokotala chifukwa chakuti ali ndi luso la
udokotala, osati chifukwa chakuti amagwira ntchito imeneyi
kapena kuti adachiritsako odwala. Chimodzimodzi Mulungu
adali Wachifundo asadalenge chirichonse. Choncho nthawi
zambiri mu Quran timapeza kuti mau oti Al Rahman
amatchulidwa pamene Iye (Allah) akufotokoza za Ulemelero
Wake, osati pamene akunena zowachitira zabwino akapolo Ake.
Mu Surah 20 (Taha) Allah akufotokoza za Ulemelero Wake
kuyambira ndime ya 4:

) 4 (

>

) 5 (

) 6 (


19
Chivumbulutso chochokera kwa Yemwe adalenga nthaka ndi
thambo lotukuka. (Al Rahman) Wachifundo, pampando
wachifumu adakhazikika. Zonse za kumwamba ndi za pansi ndi
zapakati pake ndi za pansi panthaka ndi za Iye.
Mpaka kufikira ndime ya 8 Mulungu akufotokoza za ulemelero
Wake. Mwachidule mau oti Al Rahman mu Quran
sadatchulidwe molumikizana ndikuwachitira zabwino akapolo
ake kapena zolengedwa zake.
Pamene Al Rahim, malo ambiri adatchulidwa motsatizana ndi
kuwachitira akapolo ake zabwino. Timubweretsenso dokotala
uja, pano wayamba ntchito yake ya udokotala ndipo wachiritsa
odwala angapo, nthawi ino timutcha kuti ndi Dokotala osati
chifukwa ali ndi luso la udotolo lokha ayi, koma chifukwa
amachiritsanso odwala
1
. Chimodzimodzi Al Rahim ndi
Wachifundo chifukwa amachitira zabwino akapolo ake ndi
zolengedwa zake zonse. Ndime zambiri zimene muli mau oti Al
Rahim zimatsatizana ndikuchitira zabwino akapolo ake.

) 143 (
Pakuti Mulungu ndi Woleza kwabasi kwa anthu, (Rahim) ndi
Wachifundo chambiri. [Quran 2:143].
Mu Surah 16 (An Nahl) ndime 5 mpaka 8, Mulungu
akufotokoza za chifundo chake pa anthu, mu ndime ya 7
akunena za zabwino zimene adatichitira podzichepetsa

1
Timakhulupilira kuti amene amachiritsa ndi Mulungu ndipo dokotala komanso
mankhwala ndinjira imene Mulungu amachiritsira odwala.


20
mphamvu ziweto kuti tithe kudzigwiritsa ntchito mosavuta,
ndipo akuti:

) 7 (
Ndipo zimasenza mitolo yanu (yolemera) kukafika nayo ku
midzi yakutali komwe simumatha kukafikako popanda kuvutika
kwambiri. Ndithu Mbuye wanu ndiwodekha kwambiri, (Rahim)
ndiwachisoni.
Ndime ngati zimenezi ndi zambiri mu Quran, mwachidule, Al
Rahman ndi Wachifundo pa Iye Yekha mu Ulumelero Wake,
pamene Al Rahim ndi Wachifundo powachitira zabwino akapolo
kapena zolengedwa zake zonse.
Ena amati Al Rahman ndi Wachifundo ndipo chifundo chake
amachitira akapolo Ake onse okhulupilira ndi osakhulupilira
omwe mu umoyo uno. Mulungu amadyetsa wina aliyense,
amagwetsa mvula kwa wina aliyense amachita zabwino zambiri
kwa wina aliyense posayangana kuti ndiokhulupilira kapena
osakhulupilira chifukwa onse ndi zolengedwa zake ndipo Iye
yekha ndi amene ali ndi udindo woziyanganira. Iye Mulungu
ndi Mlengi, Mbuye wa aliyense choncho chifundo chake
amapereka kwa wina aliyense.
Pemene Al Rahim ndi Wachifundo kwa okhulupilira okha mu
umoyo umene uli nkudza, chifukwa osakhulupilira
ndiothamangitsidwa mchifundo cha Allah mu umoyo umene uli
nkudza ndipo malo awo ndi ku moto. Tikumati Al Rahman ndi
Wachifundo chambiri chifukwa chifundo chake ndi chambiri


21
chimampeza aliyense, Al Rahim Wachisoni chosatha chifukwa
chifundo Chake ngakhale chidzakhale kwa anthu ochepa
(okhulupilira okha) koma chidzakhala chosatha mpaka muyaya.
Choncho ma Sheikh ena amamasulira kuti: Wachifundo
chambiri, Wachisoni chosatha.
Pomaliza, Al Rahmanir Rahim Iye ndi Wachifundo pa Iye
Yekha, chifundo Chake mu umoyo uno chimamupeza wina
aliyense wokhulupilira ndi wosakhulupilira yemwe, ndipo
umoyo uli nkudza chidzakhala kwa okhulupilira okha.
*******


22
NDIME 2
(Ndime Yachiwiri)

) 2 (
Alhamdulillahi rabbil aalamin
(2) Kutamandidwa konse ndi kwa Mulungu, Mbuye Wa
zolengedwa zonse.
Pambuyo poti Mulungu watiphunzitsa kuti tidziyamba zinthu za
umoyo wathu wa tsiku ndi tsiku ndi Bismillah, akupitiriza
kutiphunzitsanso mmene tingamutamandire. Mulungu
akadangoti Mutamandeni Mbuye wanu zikadativuta kuti
tibweretse mau abwino ndi oyenera kumutamandira Iye,
aliyense akadabweretsa mawu ake molingana ndi nzeru zake.
Koma Mulungu adatichitira chifundo potiphunzitsa kuti
tidzimutamanda Iye ponena kuti: Alhamdulillah rabbil
alamin.
Tanthauzo la: Alhamdulillahi rabbil alamin
Alhamdu: Kutamandidwa (konse), Lillahi: Ndi kwa Mulungu,
Rabbi: Mbuye (wa), Al alamin: Zolengedwa zonse.
Alhamdulillah
Mau akuti Alhamdulillah amatanthauza kuti: "Kutamandidwa
konse ndi kwa Mulungu." Mauwa amatanthauzanso kuti:
"Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu."Kusiyana kwa
Kutamanda ndi Kuyamika kuli motere:-


23
Kutamanda kumakhala mkulankhula, umamutamanda
munthu ndi mawu osati ndi zichitochito, pamene
Kuyamika (kumatchedwanso kuti Kuthokoza),
kumatheka ndi mawu komanso ndi zichitochito.
Ukamuona munthu wa mphamvu umamutamanda
polankhula kuti: Amene uja ndi wamphamvu. Pamene
yemwe wakupatsa malaya, umamuyamika polankhula
kuti: Zikomo kwambiri komanso umaonetsa kuyamika
powagwiritsa ntchito malayawo.
Timamutamanda Mulungu chifukwa cha Ulemelero
umene ali nawo komanso chifukwa cha zimene
amatichitira. Pamene Kuyamika, timamuyamika Iye
(Mulungu) chifukwa cha zimene amatichitira osati
chifukwa cha Ulemelero Wake.
Ngakhale mawu awiriwa akumveka kuti ndiosiyana,
sizolakwika kutanthauzira Alhamdulillah kuti: Kuyamikidwa
konse ndi kwa Mulungu, chifukwa mau oti: Alhamdu
tikamakamba za Mulungu amatanthauza zonse ziwiri
(Matamando komanso Mayamiko), koma mau amene ali
oyandikira kwambiri ndi Kutamandidwa. Pamene
Kuyamika/Kuthokoza mu Chiarabu ndi Shukr. Choncho
tikaonetsetsa mu Quran tipeza kuti mau oti: Alhamdulillah
agwiritsidwa ntchito pamene Mulungu akukamba za Ulemelero
Wake komanso pamene akukamba za zabwino zomwe
amawachitira akapolo Ake.
Zitsanzo za Alhamdu (kutamanda ndikuthokoza):


24
Kutamanda: Mu Surah 34 (Saba) ndime yoyamba,
Mulungu akufotokoza za Ulemelero Wake, zimene ali
nazo ndi zimene amachita, sakufotokoza zowachitira
akapolo Ake zabwino ndipo wagwiritsa ntchito mau oti:
Alhamdulillah:

) 1 (
Kuyamikidwa (Alhamdu) kwaulemu ndi kwa Mulungu
Yemwe zakumwamba ndi zapansi ndi zake.Ndipo
kutamandidwa konse kwaulemu pa tsiku lomaliza ndi
Kwake. ndiponso Iye ndiwanzeru zakuya, ndiwodziwa
chirichonse.
Kuyamika/Kuthokoza: Pamene Mneneri Ibrahim (AS)
adachitiridwa zabwino ndi Mulungu popatsidwa ana iye
ali wokalamba kwambiri adathokoza Mulungu, ndipo
Quran pa nkhaniyi yagwiritsa ntchito mau oti
Alhamdulillah kutathauza kuthokoza:

.
) 39 (
Kuyamikidwa (Alhamdu) konse ndi kwa Mulungu
Yemwe wandipatsa ine kuukulu Ismail ndi Isihaka.
Ndithu, Mbuye wanga ndiwakumva pempho (la kapolo
Wake).[Quran 14 (Ibrahim) ndime 39]
Pamene mau oti Shukr amatanthauza Kuthokoza kokha
pachimene wachitiridwa ndipo adagwiritsidwa ntchito mu
Quran malo okhawo amene Mulungu amakamba zowachitira


25
zabwino akapolo Ake. Mu Surah 40 (Ghaafir) ndime 61
Mulungu akuti:

) 61 (
Mulungu ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti mupumule
mmenemo, ndi usana kukhala wounika (kuti muthe kuchita
ntchito zanu). Ndithu, Mulungu ndi Mwini kupereka ufulu kwa
anthu. Koma anthu ambiri sathokoza.
Ayah zonga izi zilipo zambiri mu Quran. Choncho Alhamdu ndi
kutamanda komanso kuthokoza, pomwe Al shukr ndi kuthokoza
kokha. Tiyenera kumuthokoza Mulungu Yemwe wakupanga
kumuthokoza Iye mmawu ochepa oti: Alhamdulillah ndipo
kwa Iye mau amenewa amakwana. Alhamdulillah!
Zikunenedwa kuti kutamandidwa/kuyamikidwa "konse" ndi
kwa Iye Allah, chifukwa pamene tikumutamanda munthu
chifukwa champhamvu zake, kumakhala kumutamandanso
amene adapereka mphamvuzo Yemwe ndi Mulungu.
Tikamayamikira kukoma kwa chakudya, mayamikowo amapita
kwa amene waphikachakudyacho komanso kwa amene
adapereka luso lophika Yemwe ndi Mulungu. Palibe chimene
munthu angachite pokhapokha chimene Mulungu waloleza kuti
achite, matamando onse ndi mayamiko kothera kwake ndi kwa
Iye Allah. Choncho, Kutamandidwa ndi Kuyamikidwa kooonse!
ndi kwa Mulungu, Mbuye Wa zolengedwa zonse.
Rabbil alamin


26
Mbuye Wa zolengedwa zonse
Tikaiwonetsetsa kwambiri ndime imeneyi tipeza luntha ndi
kuzama kwa mawu a Mulungu. Mau ena aliwonse mu Quran ali
pa malo pake poyenelera komanso mochititsa chidwi. Mulungu
adafuna kuti Surat Al Fatihah ikhale kumayambiliro kwa Quran
chifukwa cha zomwe Surayi yatenga. Mabuku ambiri timapeza
MAU OYAMBAkomanso ZA MKATIMU timapeza kuti
mwalembedwa zokhudza mwini buku mwachidule kwambiri,
mbiri zake, maphuziro ake ndi zina zotero. Ena amalembanso
pemphero kuti cholinga cha bukulo chikwaniritsidwe, komanso
amalemba mwachidule zomwe zikupezeka m'kati mwa bukulo.
Quran idayambanso chimodzimodzi, pambuyo pa matamando,
ikufotokoza mwachidule za Mwini Bukuli (Quran) kuti Iye ndi:
Mbuye Wa zolengedwa zonse. Wachifundo chambiri,
Wachisoni.Mwini tsiku la chiweruzo.Ikupitiriza kunena kuti
Iye ndi Yemwe aliwoyenera kumupembedza komanso
kumupempha chithandizo: Inu nokha tikukupembedzani
ndiponso Inu nokha tikukupemphani chithandizo. Komanso
ikupitiriza ndi pemphero kuti cholinga cha Bukuli chomwe ndi
Chiwongoko chikwaniritsike: Tiongolereni ku njira yoongoka.
Njirayaomwe mudawapatsa chisomo; osati ya amene
adakwiyiridwa (ndi Inu) osatinso ya omwe adasokera.
Tikapitiriza kuwerenga Surah yotsatirayo, Surah 2 (Al Baqara)
ndime 2, yatibweretsera Za mkatimu za Buku limeneli: Ili
ndi Buku lopanda chipeneko mkati mwake; Ndi chiongoko cha
(anthu) oopa Mulungu. Ndizoloredwanso kuwerenga motere:


27
Ili ndi Buku lopanda chipeneko.Mkati mwake (muli) chiongoko
cha (anthu) oopa Mulungu.Za mkati mwa Buku limeneli ndi
chiongoko kwa oopa Mulungu.
Zikutanthauzanji Quran ikamati Mbuye Wa zolengedwa
zonse? Sindife oyamba kufunsa funso limeneli, Farawo
adafunsa Mneneri Musa (AS) funso longa lomweli, ife tikufunsa
ndicholinga chofuna kuphunzira, pamene Farawo kudali
kudzikweza kuti ndaninso mbuye wosakhala iye Farawo. Timve
kuchokera kwa Musa (AS), Surah 26 (Ash Shuaraa) ndime 23
ndi 24:

) 23 (

) 24 (
Farawo adati: Kodi ndani Mbuye wazolengedwayo? (Musa)
adati: Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati
muli ndi chitsimikizo.
Ndimeyi yafotokoza mwachimvekere kuti zolengedwa zonse ndi
kuyambira ntambo wakumwamba, dziko la pansi ndi zonse
zomwe zikupezeka m'menemo ndi pakati pa ziwirizi. Mbuye wa
zonsezi ndi Mulungu
Rabb(Mbuye) kuchokera pa Rabbil alamin,mau amenewa ali
ndi matanthauzo angapo ena mwa iwo ndi: Mwini, Mbuye,
Mleri ndi Bwana. Matanthuzo onsewa akusonkhana mmau oti:
Mbuye.
Rabb: Mbuye, Mwini ndi Mleri (amene amayanganira
zolengedwa zake zonse).


28
Al alamin Zolengedwa zonse. Chopezeka chirichonse,
kupatula Iye Mwini, (chimene chidapezekako, chikupezeka ndi
chimene chadzapezeka) ndicholengedwa cha Mulungu.
Kulingalira mozama m'zolengedwa za Mulungu kumabweretsa
Imaan ndi kuopa Mulungu (Taqwa). Zolengedwa za Mulungu
ndi zambiri kotero kuti tikulephera kuzisimba pogwiritsa ntchito
mawu kapena zilembo koma tingoti: Atamandike Mbuye wathu!
Yemwe adapatsa chinthu chilichonse chilengedwe chake
ndikuchiongolera!
Tikamati Mulungu amayanganira, kuyanganira Kwake sikuli
ngati momwe ife timayanganira zinthu zathu. Tikatembenukira
kumbali sitidziwa chomwe chikuchitika kumbuyo, timagona
osadziwa chomwe chikuchitika, pamene tikusamalira chinthu
chimodzi zina timakhala tazisiya kapena kuyiwala kumene,
pamene Mulungu nthawi zonse palibe chimene chimamudutsa,
amadziwa, amamva ndi kuona zonse nthawi zonse.
...

) 3 (
Sichingabisike kwa Iye cholemera ngati njere;
chakumwamba, chapansi ngakhale chochepa kuposa
chimenecho; ngakhale chokulirapo, koma (zonsezo) zili m'Buku
(Lake) losonyeza poyera (chirichonse). [Quran 34 (Saba)
ndime 3]
Tulo sitimamupeza ndipo samasinza, kuti Iye kumupeze
kusinza, kumwamba, pansi ndi zonse zomwe zili mkati mwa
ziwirizi ndi pakati pake zikhoza kuonongeka komanso kutha.

... ) 255 (


29
Mulungu palibe wopembedzedwa wina koma Iye, Wamoyo
Wamuyaya, Woimira ndi Woteteza chirichonse.Kusinza
sikumgwira ngakhale tulo.zonse zakumwamba ndi zapansi ndi
za Iye. [Quran 2 (Al Baqara) ndime 255]
Alemekezeke Mulungu! Mbuye wa zolengedwa zonse!
*******


30
NDIME 3
(Ndime Yachitatu)

>

) 3 (
Al Rahmanir Rahim
(3) Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha.
Mu ndime yathayi, Mulungu amatiuza za Mbiri Yake kuti Iye
ndi Mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo mu ndime ino
akupitiriza kutchula zina mwa mbiri Zake kuti Mulungu Amene
kutamandidwa konse ndi kwake, ndi Mbuye Wazolengedwa
zonse komanso ndi Wachifundo chambiri ndi chisoni
chosatha.Tafotokoza kale tanthauzo la Al Rahman Al Rahim
(Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha) mu ndime
yoyamba mu Surayi, choncho sitibwereza mu ndime imeneyi,
tipita ndime yotsatirayo yomwe Mulungu akupitirizabe kutiuza
Mbiri Zake.
*******



31
NDIME 4
(Ndime Yachinayi)

) 4 (
Maaliki yawmiddin.
(4) Mwini tsiku la chiweruzo.
Ndime imeneyi ili ndi kawerengedwe kosiyanasiyanamonga:

Maaliki yawmiddin komanso

Maliki
yawmiddin. Kusiyana kwake ndikoti kawerengedwe
koyambako timakoka mau oti Maalik, pamene kawerengedwe
kachiwiriko ndi Malik. Tikawerenga mokoka tanthauzo
limakhala: Mwini tsiku la chiweruzo, tikapanda kukoka
tanthauzo limakhala: Mfumu ya tsiku lachiweruzo, matanthauzo
onse awiri ndiolondola. Ena amawerenganso kuti

.Maliiki yawmiddin.
Mulungu mu ndime imeneyi akutiuza kuti Iye ndi Mfumu
komanso Mwini tsiku la chiweruzo. Ngati Allah ali Mwini
komanso Mfumu ya tsiku lachiweruzo, nanga masiku enawa
mwini komanso mfumu ndi ndani
Tsiku ndinthawi, Mulungu adalenga chirichonse
kuphatikizaponso nthawi, nthawi ndi cholengedwa cha
Mulungu, choncho masiku onse ndiolengedwa ndi Mulungu.


32
Mulungu ndi Mwini masiku onse. Ngati Iye ndiye Mwini
masiku onse, ndichifukwa chiyani wapatula tsiku limeneli kuti
ndi tsiku lake pamene masiku onse Mwini ndi Iye?
Munthu, pa dziko lapansi, adapatsidwa gawo la ufulu ndi
mphamvu zotha kuchita chimene akufuna.Akhoza kuyima,
kugona, kuyenda, kuthamanga ndi zina zambiri mmene iye
akufunira. Mulungu akamulamula kuti asadye nkhumba, iye
(munthu) alindi mphamvu zomwe adapatsidwa ndi Mulungu
zotha kusiya osadya nkhumbayo kapena kudya, akhoza
kulankhula kapena kukhala chete pamene wafuna.Aka ndi
kagawo kochepa ka ufulu ndi kudzilamulira kamene munthu
adapatsidwa mmasiku a umoyo uno. Pamene likadzafika tsiku
la chiweruzo, ufulu ndi mphamvu zimenezi zidzalandidwa ndipo
sadzatha kuchita chinthu chomwe iye akufuna ngati momwe
amachitira mmasiku a pa dziko. Umwini wotha kudzilamulira
udzatha ndipo udzatsala Umwini wa Mulungu. Choncho Mwini
Wachirichonse pa tsikuli ndi Mulungu.
Chimodzimodzi tikatanthauzira kuti Mfumu ya tsiku
lachiweruzo, Mulungu padziko lapansi amaperekanso gawo
lochepa la ufumu kwa anthu. Amapereka kwa aliyense yemwe
Iye wamufuna, okhulupilira kapena osakhulupilira, wabwino
kapena woipa. Mu Surah 3 (Ali Imran) ndime 26 Mulungu
akuti:

) 26 (


33
Nena "O! Mbuye wanga! Mwini Ufumu wonse. Mumapereka
ufumu kwa yemwe mwamufuna. Ndipo mumachotsa ufumu kwa
yemwe mwamufuna. mumapereka ulemelero kwa yemwe
mwamufuna, ndipo mumamsambula yemwenso mwamufuna.
Ubwino wonse uli m'manja mwanu.Ndithudi, Inu ndinu
Wokhoza chirichonse.
Choncho Mulungu amapereka ufumu pa dziko la pansi kwa
amene Iye wamufuna. Tikamati ufumu tikuyambira ufumu wa
mmudzi, utsogoleri wa gulu la anthu kapena bungwe,
utsogoleri wa dziko ndi utsogoleri wina uliwonse. Mfumu
kapena mtsogoleri amalamulira anthu ake ndipo chonena chake
chimachitika molingana ndi mphamvu zomwe wapatsidwa ndi
Mulungu, ndipo ulamuliro wake ukhoza kukhala wachilungamo
kapena wopondereza. Ufumu wonsewu ndi mmasiku a umoyo
uno. Pamene pa tsiku la chiweruzo ufumu wonse mwa anthu
udzakhala utalandidwa, ndipo udzatsala Ufumu wa Allah.

) 16 (
Tsiku lomwe iwo adzaonekera poyera (kwa Mulungu). Ndipo
palibe chirichonse chidzabisidwa kwa Mulungu (mzinthu zawo).
(Ndipo adzamva kufunsa koopsa ndi yankho loopsa):"Kodi
Ufumu ndiwayani lero? Ndi wa Mulungu mmodzi Yekha,
Wopambana, (woweruza mmene akufunira kwa anthu
Ake).[Quran 40 (Ghaafir) ndime 16]
Mu Surah 25 (Al Furqan) ndime 26 Mulungu akunenanso kuti:


34

>

) 26 (
Tsiku limenelo ufumu wachoonadi ndi wa (Mulungu)
Wachifundo chambiri. Ndipo lidzakhala tsiku lovuta kwa
osakhulupilira.
Mulungu ndi Mfumu ya masiku onse, ndipo masiku a umoyo
uno Mulungu amamupatsa amene wamufuna gawo lochepa
kwambiri la ufumu, koma pa tsiku la chiweruzo ma ufumu onse
adzatha udzatsala Ufumu wa Mulungu Yekha, Iye ndi Mwini
komanso Mfumu wa tsikuli.


Yawmiddin (Tsiku la chiweruzo)
Tsiku, mulingo wake ndiwosiyanasiyana, nthawi zina tikati
tsiku timatanthauza kuyambira kutuluka kwa dzuwa mpaka
kulowa kwa dzuwa, dzuwa likatuluka timati tsiku taliyamba
bwino, likamalowa timati talimaliza bwino. Nthawi zina tsiku
timatanthauza usana ndi usiku. Koma nthawi zambiri tsiku ndi
ma ola makumi awiri ndi anayi (24 hours). Ngakhale nthawi
zambiri tikati tsiku timatanthauza 24 hours koma mau oti
tsiku amagwiritsidwa ntchito potanthauza nthawi yokwana ma
ola 24, yochepera pamenepo kapena yoposera pamenepo.
Tikawerenga Hadith ya Dajjaal, imati Dajjaal adzakhala pa
dziko pano masiku makumi anayi (40) ndipo tsiku loyamba
lidzakhala lotalika ngati chaka chimodzi, tsiku lachiwiri
lidzakhala lotalika ngati mwezi, tsiku lachitatu


35
lidzakhalalotalika ngati sabata, ndipo masiku otsalawo
adzakhala otalika mofanana ndi masiku athu (ma ola 24), koma
onsewa akutchedwa kuti masiku ngakhale mulingo wake uli
wosiyana. Mulungu ndi Wakutha kupanga tsiku kukhala ma ola
24, kuchepera pamenepo kapena kuposera pamenepo. Mu Surah
22 (Al Hajj) ndime 47 Allah akunena kuti:

) 47 (
Ndipo akukufulumizitsa kuti udzetse chilango.Komatu
Mulungu sadzaswa lonjezo Lake.Ndipo ndithu, tsiku limodzi
kwa Mbuye wako lili ngati zaka chikwi (1000) chimodzi
mukawerengedwe kanu.
Mu ndimeyi Mulungu akutiwuza za tsiku lomwe kutalika kwake
ndikofanana ndi zaka 1000 za ife.
Mu Surah 70 (Al Maarij) ndime 4 akukamba za tsiku lina
lomwe kutalika kwake ndikokwana zaka 50 000 kuwerengera
zaka za ife:

>

) 4 (
Angelo ndi Jibril amakwera kwa Iye (Mulungu) m'tsiku lomwe
kutalika kwake kuli ngati zaka zikwi makumi asanu (50 000).
Choncho tsiku simaola 24 okha kapena usiku ndi usana wokha.
Zimanenedwa kuti tsiku la chiweruzo lidzatalika ngati zaka
50000, zomwe zili zodziwika bwino ndi zoti tsikuli likatalika


36
molingana ndi ntchito za munthu. Likakhala lalifupikwa anthu
ochita zabwino, aliyense molingana ndi ntchito zake, ndipo
likakhala lalitali kwa ochita zoipa aliyense molingananso ndi
ntchito zake. Mwina ndikumafunsa kuti ndizotheka bwanji tsiku
limodzi kukhala lalitali kwa wina ndi lalifupi kwa wina.
Choyamba, ngati ochititsa zimenezo ndi Mulungu ndiye kuti
ndizotheka, Iye ndiwakutha kupanga chirichonse. Izo ndiye
Mphamvu za Mulungu, akhonza kupanga tsiku limodzi kukhala
lalitali kwa ena ndi lalifupi kwa ena, akhonzanso kupanga
masiku osiyana mulingo kukhala otalika mofanana. Chitsanzo
chake ndi cha anthu a mmanda, amene adamwalira kale, amene
akumwalira tsopano ndi amene adzamwalire mtsogolo muno
onse mmanda nthawi yawo ndiyofanana palibe amakhala
mmanda nthawi yaitali kapena yaifupi kuposa nzake.
Ikadakhala nthawi yawo ndiyosiyana ndiye kuti chilango cha
mmanda kwaamene adamwalira kale chikadakhala chochuluka
kuposa amene adzamwalire Qiyama itatsala pangono, koma
sizili choncho, aliyense chilango chake ndicholingana ndi
ntchito zake. Umboni komanso chitsanzo chachikulu choti
Mulungu ndi wakutha kupanga tsiku limodzi kukhala lalitali
kwa ena ndi lalifupi kwa ena, komanso kupanga masiku ambiri
ndi ochepa kukhala otalika mofanana, tiwerenge ndime izi:
Surah 2 (Al Baqara) ndime 259 ndi ndime zingapo mu Surah 18
(Al Kahf).
Mu Surat Al Kahf, Mulungu akufotokozankhani ya anyamata
amene adathawira kuphanga ndipo Mulungu adawagonetsa tulo


37
kwa zaka zoposa ma zana atatu (300). Mndime ya 11 mu
Surayi Mulungu akuti:

) 11 (
Tidawagonthetsa makutu awo, (ndikugona kosamva nako
kanthu) kwa zaka zambirimbiri m'phanga.
Mndime ya 25 mu Surayi Mulungu akutiwuza nambala ya zaka
zomwe iwo adakhala ali chigonere mphangamo:

. ) 25 (
Ndipo adakhala m'phanga lawolo (ali mtulo) zaka
mazanaatatu (300) ndikuonjezera zisanu ndi zinayi (9).
Adali chigonere kwa zaka 309, koma pamene Mulungu
adawadzutsa, iwo adawona ngati agona tsiku limodzi kapena
gawo chabe la tsiku, mu ndime 19 Mulungu akunena kuti:

... ) 19 (
Ndipo momwemonso tidawaukitsa kuti afunsane pakati pawo
(zanthawi imene akhala alichigonere). Adanena wonena mwa
iwo: "Kodi mwakhala nthawi yotani muli mtulo?" Adati,
"Takhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku." (ena) adati:
"Mbuye wanu akudziwa kwambiri za nyengo imene mwakhala.
Alemekezeke Mulungu! Amene adapanga nthawi yokwana
zaka 309 kukhala yochepa kwambiri ngati tsiku limodzi lokha,


38
kapena maola ochepa chabe kwa Eni Phanga (Ashaabul
Kahf).
Mu Surah 2 (Al Baqara) ndime 259, Mulungu akufotokoza za
munthu yemwe adali ndi bulu wake komanso chakudya cha pa
ulendo, ndipo pamene amadutsa pa mudzi wina umene anthu
ake adamwalira ndipo udagumuka-gumuka,iye adadzifunsa
yekha kuti Mulungu adzawudzutsa bwanji mudziwu ndi anthu
ake?

>

) 259 (
Kapena ngati fanizo la uja amene adadutsa pafupi ndi mudzi
umene madenga ndi zipupa zake zidaphwasuka (udaferatu)
adati: "Kodi Mulungu adzaukitsa chotani mudzi uwu pambuyo
pakufa kwake?" Ndipo Mulungu adampatsa imfa kwanthawi
yokwana zaka zana limodzi (100), kenako adamuukitsa
namufunsa: "Kodi wakhala nyengo yotani?" Adati: "Ndakhala
nthawi yatsiku limodzi, kapena theka latsiku." (Mulungu) adati:
"Koma wakhala zaka zana limodzi, ndipo ona chakudya chako
ndi zakumwa zako, sizidaonongeke (sizidavunde). Ndipo
yang'ana bulu wako (ali mafupa okhaokha oyoyoka);ndi kuti
ukhale chisonyezo kwa anthu, (nchifukwa chake takuukitsa ku


39
imfa). Ndipo yang'ana mafupa(abulu wako) momwe
tingawaukitsire, kenako nkumaaveka minofu." choncho pamene
zidazindikirika (kwa iye, woukitsidwayo), adati: "Ndikudziwa
kuti Mulungu Ngokhoza chirichonse."
Poyankha funso la munthuyu, Mulungu adamuchotsa mzimu
1

ndipo adali chimwalilire kwa zaka zana limodzi (100),
zachidziwikire kuti thupi lake lidali litasanduka dothi.
Atawukitsidwa ndikufunsidwa za nthawi yomwe wakhala ali
chimwalilire, iye adati wakhala tsiku limodzi kapena gawo la
tsiku. Pamene adayangana chakudya chake adachipeza kuti
chili bwino bwino, sichidawole chifukwa chakuti chakudyacho
sichidakhale nawo zaka 100. Pamene adayangana bulu wake
adapeza mafupa okha okha kusonyeza kuti buluyo adakhala
zaka 100 zimene iye adali chimwalilire. Mulungu ndiwakutha
kupanga nthawi imodzi kukhala zaka 100 ngati momwe
adachitira kwa buluyo komanso nthawi yomweyo kukhala tsiku
limodzi ngati momwe adachitira ku chakudya cha munthuyu.

1
Sheikh Khalid Ibrahim potanthauzira ndime imeneyi akuti Ndipo Mulungu
adampatsa imfa sadagwiritse ntchito mau oti adamupha chifukwa kupha
ndikulichita thupi chinachake kufikira kufa, monga kumenya kapena kuvulaza mpaka
kufa, kapena kumudyetsa munthu mankhwala ngati poisoni mpaka kufa, zonsezi
umalichita thupi kenaka nzimu umachoka, timati: waphedwa, poisoni wamupha ndi
zina zotero, kumeneko kumatchedwa kupha, pa chiarabu amati

Qatala.
Pamene Mulungu akamakamba za Iye kuchotsa moyo mwa munthu kapena china
chirichonse amati

Amaata chifukwa Amaata ndikuchotsa mzimu popanda


kuchita chirichonse ku thupi, amene angathe zimenezo ndi Mulungu Yekha, pamene
anthu amangolimbana ndi thupi pofuna kuchotsa moyo wa munthu. Chifukwa choti
mau oti: Amaata kuchichewa kulibe, Sheikhewa adamasulira kuti: Adampatsa imfa.


40
Choncho tikamva kuti tsiku la chiweruzo ndilalitali ngati zaka
50000, zisatikayikitse. Tikamvanso kuti tsikuli likatalika
molingana ndi ntchito za anthu tisakayikirenso chifukwa Allah
wationetsa kale kuti Iye ndiwakutha chirichonse.
Mu umoyo wathu watsiku ndi tsiku, zimachitikanso kuti tsiku
lomwelo kwa wina limaoneka kutalika chifukwa cha ziphinjo
zimene munthu akukumana nazo, komanso limaoneka kufupika
kwa amene ali pachisangalalo patsikulo.
Dini
Mau oti Dini, ambiri timagwiritsa ntchito pafupifupi tsiku
lirilonse pofuna kunena za Dini yathu ya chisilamu.
Tikamawerenga ndime imeneyi kumapetoko kulinso mau
amenewa:

Maaliki yawmid-din. Mauwa ndi


amodzi koma ali ndi matanthauza angapo, amatanthauza
Chipembedzo, Chikhulupiliro komanso Chiwerengero ndi
Malipiro. Mu Surah 3 (Aali Imran) ndime 19 mau amenewa
atchulidwanso kutanthauza Chipembedzo:

... ) 19 (
Innad-dina inda-llahil islam
Ndithudi, chipembedzo (choona) kwa Mulungu ndi Chisilamu
Ndime zomwe mau amenewa atchulidwa potanthauza
chipembedzo zilipo zambiri.


41
Mu Surah 2 (Al Baqarah) ndime 256, mau oti Din
atchulidwanso potanthauza Chikhulupiliro kapena kuti kulowa
mchipembedzo:

. )... 256 (
Palibe kukakamiza (munthu kulowa) M'chipembedzo
1

Mu ndime imene tiriyi mau oti Din sakutanthauza chipembedzo,
sitinganene kuti: Maaliki yawmiddin Mwini tsiku la
chipembedzo. Koma akutanthauza Malipiro. Tikawerenga
Surah 51 (Adh Dhaariyaat) ndime 6 tipeza kuti mau amenewa
agwiritsidwa ntchito ndipo akutanthauza kuti Malipiro:

) 6 (
Ndipo, ndithu, malipiro (pa zochita zanu) adzapezekadi.

1
Tipezerepo mwayi, ndime imeneyi ena samayimvetsetsa bwino; amatanthauzira
molakwika kuti: Mchipembedzo mulibe kukakamizana, choncho munthu akhoza
kupanga chimene akufuna kapena kusapanga chimene sakufuna, akhoza kusiya
kupemphera, osavala Hijaab chifukwa palibe kukakamizana, kumeneko ndikumva
molakwika. Odana ndi Chisilamu amapezeranso mwayi ndipo amafunsa kuti ngati
mchipembedzo mulibe kukakamizana nanga ndi chifukwa chiani munthu akatuluka
Chisilamu amaphedwa, kumeneko sikukakamizana? Tiwauze anthu ngati amenewa
kuti ndimeyi ikutanthauza kulowa mchisilamu samakakamizana, koma ukalowa
ndiye kuti ukuvomereza malamulo ake onse, choncho udzayenera kutsatira, ngati
waphwanya lamulo udzayenera kupatsidwa chilango. Tiwachenjeze achinyamata
amene akuphunzira chiarabu kuti kudziwa chiarabu sindiye kuti ungamve
matanthauzo a Quran. Sheikh Khalid Ibrahim (Mulungu awalipire zabwino)
atanthauzira ndime imeneyi momveka bwino, sadanene kuti: Mulibe
kukakamizana mchipembedzo ngati momwe chiarabucho chikumvekera, koma
anena kuti: Palibe kukakamiza (munthu kulowa) M'chipembedzo.


42
Mu Surah 24 (An Nur) ndime 25:

) 25 (
Tsiku limenelo Mulungu adzawapatsa malipiro awo a
choonadi, ndipo adzadziwa kuti Mulungu ndiye Mwini kulipira
kwachoonadi koonekera poyera.
Ndi ndime zina zambiri. Choncho kuwawerengera anthu ntchito
zawo ndikuwapatsa malipiro awo ndiye chiweruzocho.Maaliki
yawmiddin: Mwini tsiku la chiweruzo.
Tsiku limeneri limatchuka ndi dzina loti: Tsiku la Qiyama,
kutanthauza kuti tsiku lodzuka mmanda ndikuyima:

) 68 (
Kenako lidzaimbidwa (Lipenga)kachiwiri; pamenepo (onse)
adzauka; adzakhala akuyang'ana (modabwa: 'Nchiyani
chachitika!). [Quran 39 (Az Zumar) kumapeto kwa ndime 68]
Lidatchulidwa kuti Tsiku la Qiyama mu Quran kokwana
makumi asanu ndi limodzi (60). Limatchedwanso kuti: Tsiku
Lomaliza ndipo lidatchulidwa kuti Tsiku Lomaliza mu Quran
kosachepera makumi awiri (20) ndi maina ena ambiri, koma
lidatchulidwa mu Quran kuti: Tsiku Lachiweruzo kokwana
khumi (10). Zikadatheka Mulungu kunena kuti: Mwini tsiku la
Qiyama, koma Mulungu mu Surah yoyambayi wagwiritsa
ntchito dzina loti: Tsiku la chiweruzo (Malipiro), chifukwa
dzinali likutenga zonse zochitika patsikuli. Kulandira malipiro


43
ndiye kuti padzafunika kuti anthu awuke mmanda ndi kuyima,
kuweruzidwa kenako kupatsidwa malipiro awo, Jannah kapena
Moto. Pamene dzina loti: Tsiku la Qiyama (lowuka mmanda
ndi kuyima) likungotchula chabe zouka mmanda, silikutchula
zochitika zonse. Tsiku lomaliza silikutchula chochitika
chirichonse, choncho mu Surah yoyamba zidayenera kugwiritsa
ntchito dzina lomwe likukamba za zochitika zonse za tsikuli,
uko ndiye kuzama kwa mawu a Mulungu.
*******


44
NDIME 5
(Ndime Yachisanu)

. ) 5 (
Iyyaka nabudu wa Iyyaka nastain
(5) Inu nokha tikukupembedzani, ndiponso Inu nokha
tikukupemphani chithandizo.
Quran ndi mawu a Mulungu, ndipo akulankhula apa ndi
Mulungu, akutilankhula ife okhulupilira, koma Allah
samapempha kwa aliyense:

) 97 (
Ndithudi, Mulungu ndiwachikwanekwane pa zolengedwa
Zake.[Quran 3 (Aali Imran) ndime 97.
Kutanthauza kuti palibe chomwe chingamuthandize
muzolengedwa Zake zonse. Mulungu akamati: Inu nokha
tikukupemphani..., amene akupempha si Iye, koma kuti
Mulungu akutiphunzitsa ife momwe tingayambire zinthu zathu
kuti tidziyamba ndi Bismillah, tidzimutamanda ponena kuti
Alhamdulillah ndipo akuti tidzinena kuti: Inu nokha
tikukupembedzani ndiponso Inu nokha tikukupemphani
chithandizo. Mu ndime zotsatirazo akupitiriza kutiphunzitsa
momwe tingamupemphere chiwongoko ndipo akuti tidziti:
Tiongolereni kunjira yoongoka.



45
Iyyaka nabudu
Inu nokha tikukupembedzani
Iyyaka: Inu nokha Nabudu: Timakupembedzani, mau oti
Nabudu akuchokera ku mau oti: Ibaadah
(kupembedza/kugwadira) omwe akuchokera ku mau oti: Abdu
(kapolo). Timati: Abdullah (Kapolo Wa Mulungu), Abdul
Rahman, Abdul Jabbaar, Abdul Hamid ndi ena ambiri.
Kalekale, munthu akagwidwa ukapolo amakhala womvera
malamulo ndi wodzichepetsa pa maso pa bwana wake, wochita
chirichonse chomwe bwana wake walamula popanda kufunsa
chifukwa, ndipo kapolo akakanira bwana wake amapatsidwa
chilango, kumanidwa chakudya, kukwapulidwa ndi zina zotero.
Kuchita zinthu zimenezi, zomwe kapolo amachita kwa bwana
wake kumatchedwa Kupembedza. Choncho ife timatchedwa
kuti akapolo a Mulungu chifukwa cholinga chopezekera pa
dziko pano ndi kuti tidzimumvera Mulungu ndi kutsatira
malamulo Ake, kudzichepetsa pa maso pake, kuchita
chirichonse chomwe walamula, mmene Iye akufunira popanda
kufunsa chifukwa, zimenezi zikutchedwa kuti Kupembedza
ndipo akapolo opanda kutsatira zimenezi adzapatsidwanso
chilango:

) 56 (
Sindidalenge ziwanda (majini) ndi anthu koma kuti
adzindipembedza. [Quran: 51(Adh Dhariyat) ndime 56]


46
Chimenecho ndiye cholinga chomwe Mulungu adatilengera,
ndipo zinthu zina zonse zomwe timachita monga kugwira
ntchito, kudya, kugona ndizongothandizira kuti Ibaadayo ikhale
yosavuta. Mmalo mwake anthu atembenuza, akupanga
kusangalala, kusonkhanitsa chuma ndi zina zotero kukhala
cholinga chenicheni ndipo Ibaadah ndiyongothandizira pa
nthawi imene moyo wathina.
Kupembedza (Ibaadah) sikupemphera Swala kokha,
Kupembedza ndi: Kudzichepetsa, Kumvera malamulo a
Mulungu ndi Kugonjera mwa Iye. Kupembedza kuli mzinthu
zambiri, zomwe Mulungu amazikonda ndi kusangalala nazo
mzolankhula; monga kupanga ma Dhikr (kumukumbukira
Mulungu), kupanga Dua, kulankhula zoona ndi zabwino.
Kupembedza kulinso mzichitochito monga Kupemphera,
kupereka Zakah kapena Sadqah, kupanga Hajj, kuyendera
odwala, kukhala ndi anthu bwino ndi zina zotero.
Mu ndimeyi tikamati: Inu nokha tikukupembedzani
tikutanthauza kuti timachita zinthu zonsezi ndicholinga
chokusangalatsani Inu Mulungu, osati kuti anthu atione, atitame,
osatinso kuti tipeze phindu la padziko lokha. Tikaonetsetsa
tipeza kuti moyo wathu wonse wadzadza ndi Ibaadah koma
ambiri samachita ndicholinga chomusangalatsa Mulungu.
Wa iyyaka nastain
Ndiponso Inu nokha tikukupemphani chithandizo.
Tikunena kuti timapempha chithandizo kwa Mulungu Yekha,
pamenepa pakufunika timvetsetse bwino chifukwa wina akhoza


47
kumafunsa kuti kodi anthu sitimathandizana? Munthu nzako
sangakuthandize? Dokotala akationaona ndikuchira
sadatithandize? Nzako akakupempha kuti umuthandize ndi 500
kwacha, pamenepo sadapemphe chithandizo?
Ndi zoona kuti anthu timathandizana, nzako akhoza
kukuthandiza, dokotala amatithandiza ndiponso nzako atha
kukupempha chithandizo. Tinene kuti tikutsutsana ndi ndime
imeneyi yoti ndi Mulungu Yekha Yemwe timamupempha
chithandizo?
Choyamba tidziwe kuti chithandizo chonse chimachokera kwa
Mulungu, ndipo Mulungu adafuna kuti chithandizo chake pa
akopolo ake chidziwapeza kudzera mnjira zosiyanasiyana,
komanso akafuna amatha kuthandiza popanda kugwiritsa ntchito
njira zimenezi. Mwachitsanzo, mukapempha Mulungu kuti
akuthandizeni ndi chakudya, Mulungu samachitsitsa kuchokera
kumwamba kufikira pa khomo panu moonekera, koma
amakusonyezani ndikukufewetserani njira yopezera
chakudyacho.
Tikapita kwa dokotala ndikuchira, timati dokotala watithandiza,
koma chithandizocho chachokera kwa Mulungu, amene
watichiritsa ndi Mulungu ndipo dokotala ndi njira imene
Mulungu adafuna kuti atithandizire. Mukalima ndikudzala
mmunda wanu, kulima ndi kudzala, mbewu ndi nthaka zonsezo
ndi njira zimene Mulungu wafuna kukuthandizirani ndi
chakudya. Ukamupempha nzako kuti akuthandize ndi 500
kwacha, nzakoyo ndi njira imene Mulungu wakufewetsera


48
ndikukuthandizira. Choncho chithandizo chonse chimachokera
kwa Mulungu.
Tikamapempha chithandizo kwa munthu timayenera kudziwa
ndikukhulupilira kuti Wothandiza ndi Mulungu Yekha ndipo
munthuyo ndi njira chabe. Koma ukakhulupilira kuti iye
(munthu) ndi amene ali ndi mphamvu yokuthandiza, pamenepo
watsutsana ndi ndime imeneyi ndipo wamuphatikiza Allah ndi
zinthu zina (Shirk). Ukayika mlonda pa nyumba amene
amateteza ndi Mulungu ndipo mlondayo ndi njira imene
Mulungu akuperekera chitetezo Chake.
Ndiye tikamati Inu nokha tikukupemphani chithandizo
timatanthauza kuti, zonse timazisiya mmanja Mwanu chifukwa
Inu nokha ndi amene mumathandiza ndipo ife titenga njira
zomwe chithandizo chanu chimatifikira. Tilima ndi kudzala,
ndipo kudzera mu ulimiwo tithandizeni ndi chakudya. Kudzera
mwa dokotala tichiritseni ndi zina zotero.
*******


49
NDIME 6
(Ndime Yachisanu ndi chimodzi)

) 6 (
Ihdinas siraatal mustaqim
(6) Tiongolereni ku njira yoongoka
Tafotokoza za kupempha chithandizo mndime yapitayo ndipo
Mulungu mndime iyi akutibweretsera chinthu choyenera
kuyamba kupempha, chiongoko. Tonse timafuna kuti tidzalowe
ku Jannah, amenewo ndi mapeto a ulendo wa anthu ochita
zabwino, koma Allah mu Surah yoyambayi, pempho loyamba
kutiphunzitsa sadati: Tipatseni Jannah, koma wati: Tiongolereni
ku njira yoongoka. Chifukwa chakuti Jannah ndi mathero
pamene chiongoko ndi mayambiliro, Mulungu akatipatsa
chiongoko, zimene tizichita molingana ndi chiongokocho
zikatifikitsa ku mathero amene ali Jannah.
Tiongolereni mu ndimeyi ndi mawu osonyeza kupempha osati
kulamula. Bwana akanena kwa akapolo ake kuti: Limani
munda uwu limenelo limakhala lamulo kwa akapolo akewo,
pamene akapolo ake akanena kuti: Tipatseni makasu tilime
limenelo limakhala pempho kwa bwana wawoyo.
Chimodzimodzi, Mulungu akamati pangani izi, limakhala
lamulo, pamene ife akapolo Ake tikamati: Tipangireni izi
limakhala pempho kwa Mulungu wathu osati lamulo.


50
Chiongoko (Hidaayah) chili ndi matanthauzo awiri: Pali
Chiongoko, kumusonyeza munthu njira yoyenera.
Mwachitsanzo munthu wafika pa msewu womwe wagawikana
pawiri, sakudziwa kuti ndi nsewu uti umene ukamufikitse
kumene akupita, adzayenera kupeza munthu amene akudziwa,
amuuze kuti komwe akupitako atenge nsewu uwu ndipo
akatenga winawu asochera. Munthu ameneyu wamuongolera
pomusonyeza njira yoyenera ndi kumuchenjeza za njira inayo.
Imeneyo ndiye ntchito ya Atumiki komanso anthu amene atenga
mipando ya Atumiki (ma Sheikh), kuongolera anthu powauza
njira ya ku Jannah ndikuwachenjeza za njira yaku Moto.
Ndiye pali Chiongoko (Hidaayah) chomwe ndikuika madalitso
ndi Imaan mu mtima wa munthu kuti atsate ndikugwiritsa
ntchito njira yoongoka, mkulankhula kwina tingati, kutsekula
mtima wa munthu kuti akhale okhulupilira ndi wochita zabwino.
Amene amatsekula mtima wa munthu kuti Imaan imeneyi ilowe
ndi Mulungu Yekha. Ndichifukwa chake timapeza ndime ziwiri
kapena zingapo zagwiritsa ntchito mau amenewa oti: Chiongoko
(Hidaayah) mosiyana ndipo zimamveka ngati ndimezi
zikutsutsana. Anthu odana ndi chisilamu amatenga ndime
zimenezi ndikupezerapo mwayi wonena kuti Quran imadzitsutsa
yokha. Vuto ndi kusazindikira, ndimezi nazi:
Surah 42 (Ash Shura) kumapeto kwa ndime 52:

) 52 (
Ndithu iwe (Muhammad) ukuongolera kunjira yoongoka,


51
Mu ndimeyi Mulungu akumuuza Mtumiki (SAW) momveka
bwino kuti iye Mtumiki (SAW) akuwaongolera anthu ku njira
yoongoka. Pamene mu Surah 28 (Al Qasas) ndime 56, Mulungu
akuti:

) 56 (
Ndithu, iwe sungathe kumuongola amene ukumfuna, koma
Mulungu amamuongola amene wamfuna. Ndipo Iye akudziwa za
amene ali oongoka.
Kuchichewa tikutha kumva kusiyana kwa ndime zimenezi,
yoyambayo akuti Kuongolera yachiwiriyo akuti Kuongola.
Pamene kuchirabu agwiritsidwa ntchito mau amodzi. Choncho
ndimezi sizikutsutsana, mu ndime yoyambayo Mulungu
akumuuza Mtumiki (SAW) kuti iye akuwalozera anthu njira
yoyenera kutsata, njira yoongoka, pamene ndime yachiwiriyo
Mulungu akumuuza Mtumiki (SAW) kuti iye sangathe
kutsekula mtima wa munthu ndikumuyika Imaan ndi
chikhulupiliro kuti atsate njira yoongoka, zimenezo amachita
ndi Mulungu.
Quran ndi mawu a Mulungu ndipo sizingatheke kupezeka
kutsutsana, ngati mungapeze kutsutsana ndiye kuti penapake
simunapamvetse bwino choncho osafulumira kunena kuti Quran
ikudzitsutsa yokha, mmalo mwake afunseni amene
akuzindikira kuti akufotokozereni bwino.



52
Siraat (Njira)
Mu ndimeyi, Siraata ndi mawu amene atanthauzidwa kuti Njira
m'chichewa. Njira, ndi m'sewu kapena ndondomeko imene
munthu amatsata kuti athe kukwaniritsa kapena kukafika
kumene iye akupita. Zimakhala zovuta kuti munthu akafike
kumene iye akupita ngati sakutsatira njira yoyenera. Choncho,
mawu omaliza a ndime ino akufotokoza chizindikiro cha njira
yoyenera..
Mustaqeem (yowongoka)
Njira yowongoka ndi imene ili yosakhotakhota, ndipo ndi njira
imene imakhala yofupika kuposa njira yokhotakhota.
*******



53
NDIME 7
(Ndime Yachisanu ndi chiwiri)

) 7 (
Siraatalladhina anamta alayhim, ghayril magh-dhubi
alayhim waladh dhaallin
(7) Njirayaomwe mudawapatsa chisomo; osati ya amene
adakwiyiridwa (ndi Inu) osatinso ya omwe adasokera.
Ndime imeneyi ikupitiriza kufotokoza za njira yoongoka imene
yatchulidwa mndime yomwe yangothayo: Tiongolereni ku
njira yoongoka.
Akamati njira yoongoka mndimeyi akutanthauza chani?
Siraatalladhina anamta alayhim
Njira ya omwe mudawapatsa chisomo
Ndime imeneyi ikutiwuza kuti njira yoongokayi ndi yomwe
adatsata anthu omwe adapatsidwa chisomo ndi Mulungu. Kodi
omwe adapatsidwa chisomo ndi ndani, tiwadziwe kutinso
tidziwe njira imene iwo adatsata? Tikawerenga Quran tikupeza
Surah 4 (An Nisaa) ndime 69 yawatchula omwe adapatsidwa
chisomo:

) 69 (


54
Ndipo amene angamvere Mulungu ndi Mtumiki Wake, iwowo
ndi omwe adzakhale pamodzi ndi omwe Mulungu adawapatsa
chisomo (adawadalitsa), kuyambira Aneneri, Olungama, ma
Shahidi (asilamu ofela kunkhondo) ndi anthu abwino. Taonani
ubwino wokhala nawo pamodzi iwowo!
Ndimeyi yanena kuti amene adapatsidwa chisomo ndi
kuyambira: Aneneri, Olungama, ma Shahid ndi anthu abwino
(ochita zabwino). Chisomo (Nimah) chimatchedwanso kuti
mtendere, ndi chirichonse chabwino pa moyo wa munthu, kuona
ndi chisomo, kuyenda, kupuma, kukhala msilamu ndi chisomo,
kuti tiyambe kuwerenga chisomo sitingakwanitse. Mulungu mu
Surah 16 (An Nahl) ndime 18 akuti:

) 18 (
Ngati mutayesera kuwerengera mtendere wa Mulungu
simungathe kuuwerengera (wonse); ndithudi, Mulungu
ndiwokhululuka kwambiri, ndiwachisoni.
Mtendere umenewu tikuona kuti amapatsidwa anthu onse
okhulupilira ndi osakhulupilira omwe, tsopano ndimeyi ikuti
amene adapatsidwa chisomochi ndi Aneneri, Olungama ma
Shahid ndi ochita zabwino. Zikuonetsa kuti chisomo
chimenechi ndi cha mtundu wina osati chisomo chomwe
amapatsidwa anthu onse, monga maso, makutu ndi zina zotero.
Choncho ma sheikh ena amanena kuti chisomo chimenechi ndi:
Kusonyezedwa njira ya choona, ndikupatsidwa mtima wotha
kuyigwiritsa njira imeneyi (Imaan\Chikhulupiliro).


55
Amenewa ndi amene amatsata njira yoongoka choncho tikafuna
kudziwa kuti njira yoongoka ndi chani, tiwafunse amene
atchulidwa apawa. Mu Quran mneneri amene wafotokoza kuti
njira yoongoka ndi chani, ndi Mneneri Yesu (AS). Surah 3
(Aali Imran) ndime 51, Surah 19 (Maryam) ndime 36 komanso
Surah 43 (Az Zukhruf) ndime 64.

Surah 19 (Maryam) ndime 36:

) 36 (
(Yesu adati:) "Ndipo ndithu, Mulungu ndi Mbuye wanga
ndiponso Mbuye wanu.Choncho mpembedzeni; iyi njira
yolunjika (yokufikitsani ku mtendere.)
Yesu (AS) akuwauza anthu kuti kukhulupilira kuti Mbuye ndi
Mulungu, ine (Yesu) simbuye, Mbuye wanga ndi Mbuye wanu
ndi Mulungu, ndi kuti omupembedza ndi Mulungu osati ine
(Yesu), musapemphere mu dzina la ine ndipo pempherani
mdzina la Mulungu, imeneyi ndiye njira yoongoka. Mu ndime
zitatu zomwe zafotokoza kuti njira yoongoka ndi chani,
amalankhula ndi Yesu (AS). Ndipo Mulungu akuikira kumbuyo
mawu a Yesu oti kupembedza Mulungu Yekha ndiye njira
yoongoka mu Surah 36 (Yasin) ndime 60 ndi 61, Mulungu
akuti:

) 60 (

) 61 (


56
(60) Kodi sindidakulangizeni, E!inuana a Adamu kuti
musapembedze Satana; ndithu, iye ndi mdani woonekera kwa
inu. (61) Ndikuti ndipembedzeni Ine; imeneyi ndi njira yolunjika
(yoongoka).
Zili ngati kuti Yesu (AS) adadziwa kuti akadzachoka anthu
adzamutcha mwana wa Mulungu ndikumupembedza.
Pachifukwa chimenechi tikupeza kuti Yesu (AS) adalankhula ali
wakhanda ndipo mau oyamba kuwauza anthu adali oti: Ine
ndine kapolo wa Mulungu:

) 30 (
(Mwanayo) adanena: "Ine ndine kapolo wa
Mulungu.Wandipatsa Buku ndikundichita kukhala
Mneneri.Surah 19 (Maryam) ndime 30.
Zikadatheka kungonena kuti ine ndine Mtumiki wa Mulungu
ndi Mneneri Wake koma Yesu (AS) adayamba ndikuti ine
ndine kapolo wa Mulungu, chifukwa mawu amenewa
tikawamvetsetsa bwino tipeza kuti akutsutsa zoti Yesu (AS) ndi
mwana wa Mulungu. Palibe amene angamupange mwana wake
kukhala mgulu la akapolo ake omugwilira ntchito, choncho
ngati Yesu (AS) akuti ine ndine kapolo wa Mulungu sizotheka
kuti akhale mwana wa Mulungu. Akadangonena kuti ine ndine
Mtumiki ndi Mneneri wa Mulungu, zikadanenedwa kuti
ndizotheka mwana wako kukhala wotumikira.


57
Choncho mu ndimeyi tikamati Tiongolereni ku njira yoongoka.
Njira ya omwe adapatsidwa chisomo njira yake ndi:
Kupembedza Mulungu yekha.
Ghayril magh-dhubi alayhim
Osati ya amene adakwiyiridwa (ndi Inu)
Ndime 7 ikupitiriza kunena kuti njira yake osati ya omwe
adakwiyiridwa ndi Mulungu osatinso njira ya omwe adasochera.
Mabuku a Tafsir amatiuza kuti amene adakwiyiridwa ndi
Ayuda, kutengera ndime 60 mu Surah 5 (Al Maidah) yomwe
ikukamba za Ayuda motere:

) 60 (
Nena: "Kodi ndikuuzeni za uja amene ali ndimalipiro oipa kwa
Mulungu kuposa izi? Ndiomwe Mulungu wawatemberera ndi
kuwakwiira ndi kuwasandutsa ena kukhala anyani ndi nkhumba,
ndi opembeza Satana. Awo ndiwo okhala ndi malo oipa,
ndiponso osokera njira yowongoka."
Mulungu adawatembelera, kuwakwiyira ndi kuwasandutsa ena
mwa iwo anyani ndi nkhumba. Amene adasandutsidwa ena mwa
iwo kukhala anyani ndi Ayuda, umo ndi mmene ma Sheikh
ambiri amatiuzira. Tikufunika kumvetsetsa, sizikutanthauza kuti
Ayuda okha ndi amene adakwiyiridwa ndi Mulungu, komanso
Mulungu sadawakwiyire iwo pokhala kuti ndi Ayuda koma


58
chifukwa cha kukanira kwawo chilungamo akuchidziwa
komanso kupha Aneneri. Surah 2 (Al Baqarah) ndime 61,
kumapeto kwa ndime imeneyi Mulungu akuti:

) 61 (
Potero adapatsidwa kunyozeka ndi kusauka; nabwelera ndi
mkwiyo wa Mulungu. Zimenezo n'chifukwa chakuti iwo sadali
okhulupilira zisonyezo za Mulungu, ndikuti adali kupha
Aneneri a Mulungu popanda chifukwa. Zidali tero chifukwa cha
kunyoza kwawo, ndipo adali olumpha malire.
Choncho okwiyiridwa ndi Mulungu si Ayuda okha, koma
aliyense amene amachita zimene Ayuda adachita, kukanira
chilungamo akuchidziwa, kupha Aneneri ndi kudumpha malire
mkukanira kwawo.
Waladh-dhaallin
Osatinso ya omwe adasokera.
Mulungu mu ndimeyi akupitiriza kuti osatinso njira ya omwe
adasokera. Amene adasokera ndi Akhristu, kutengera Hadith:
Ibn Hatim adati: Ndidamufunsa Mtumiki (SAW) za mau a
Mulungu oti: {Osati (njira) ya omwe adakwiyiridwa} iye
(Mtumiki) adati: Anthu ake ndi Ayuda, {Osatinso ya omwe
adasokera} iye adati: Akhristu.


59
Kusochera ndikutenga njira yolakwika ndikumaganiza kuti
ikakufikitsa kumene ukufuna. Kusiyana kwa Ayuda ndi Akristu
ndikwakuti, Ayuda, amaidziwa njira yoongoka ndi yachoonadi,
koma amayibisa ndikumatsatira zawozawo. Pamene Akristu
samayidziwa njira yoongoka, safunanso kufufuza kuti athe
kuyipeza, mmalo mwake amatsatira njira yomwe iwo akuganiza
kuti ndiyoona ndikuti ikawafikitsa ku ufumu wa kumwamba,
umo ndi momwe adasochelera. Omwe adasokera si Akhristu
okha, koma aliyense amene samadziwa choona ndipo safuna
kuchidziwa koma kutsata njira yolakwika kumaganiza kuti
ndiye yoongoka, ndipo Akhristu ndi amene ali owoonekera.
*******
__________________
AMEEN


Ameen
Ndi Sunnah kwa amene wawerenga kapena kumvera Surat Al
Fatihah kunena kuti: Ameen.
Mawu oti: Ameen amatanthauza kuti: Ambuye pangani
kutanthauza kuti Ambuye Mulungu tipangireni zimene
takupemphanizi. Amatanthauzanso kuti: Ambuye yankhani
(pempho langa\lathu), tanthauzo lachiwirili ndi limene ma
Sheikh ambiri amasankha.


60
Ndime ziwiri zomaliza mu Surat Al Fatihah ndi Dua
(pempho): Tiongolereni ku njira yoongoka. Njira ya omwe
mudawapatsa chisomo; osati ya amene adakwiyiridwa (ndi
Inu) osatinso ya omwe adasokera. Ameen (Ambuye
tiyankheni pempho lathuli.)
Mau oti Ameen siochokera mu Quran, ndi mau a Jibril,
ndichifukwa chake samalembedwa limodzi ndi Surayi ngati
momwe Bismillah amalembedwera.
Pali ma Hadith ambiri omwe amatilimbikitsa kunena Ameen
tikawerenga Surat Al Fatihah ena mwa iwo ndi awa:
Abu Hurairah adati: Mtumiki (SAW) amati akawerenga:
{Ghayril magh-dhubi alayhim wala-dhaallin} amanena kuti:
Ameen.-Abu Daud-
Hadith ina ya Abu Hurairah, Mtumiki (SAW) adati: Imaam
akanena kuti Ameen inunso mudzinena Ameen chifukwa
ndithudi, amene Ameen wake afanane\atsatane ndi Ameen wa
Angelo, Mulungu amamukhululukira machimo ake onse
ammbuyo. -Bukhari, Muslim-
_________________________



61
MABUKU OMWE AMAONEDWA KWAMBIRI
POLEMBA BUKU LIMENERI:
1. Quran Ya Chichewa (Sheikh Khalid Ibrahim).
2. Tafsir Al Sharawiy (Sheikh Muhammad Mutawally Al-
Sharawiy).
3. Tafsir Al Wasit (Sheikh Muhammad Sayyid Tantawiy
Sheikhul Azhar).
4. Tafsir Ibn Kathir.
5. Tafsir Ibn Abbas.
6. Tafsir Ayaatil Ahkaam.
7. Fi Rihaabit Tafsir (Sheikh Abdul Hamid Kishk).
Kuphatikizapo ma buku ena omwe amaonedwa mwapatalipatali.

You might also like