You are on page 1of 32

NA IMWE MUNGAKHALE

MNZAKE WA MULUNGU!

NKHANI ZA MKATI

PHUNZILO


Mulungu Akupemphani Kuti Mukhale Mnzake

Mulungu Ndiye Angakhale Mnzanu Wabwino Kwambili

Mufunikila Kuphunzila za Mulungu

Nanga Mungaphunzile Bwanji za Mulungu?

Anzake a Mulungu Adzakhala mu Paladaiso

Paladaiso Ili Pafupi!

Kutengapo Phunzilo pa Zimene Zinacitika Kumbuyo

Kodi Adani a Mulungu ni Andani?

Kodi Anzake a Mulungu ni Andani?

 Mmene Mungadziwile
Cipembedzo Coona

9
10

Kanani Cipembedzo Conama!

11

Kodi Munthu Akafa Cimacitika kwa Iye ni Ciyani?

12

Matsenga na Ufiti ni Vinthu Voipa

13

Anzake a Mulungu Amakana Kucita Voipa

14

Anzake a Mulungu Amacita Vinthu Vabwino

15

Onetsani Cikondi Canu kwa Mulungu

16

Kuti Musunge Ubwenzi, Mufunikila Kukhala Munthu Waubwenzi

17

Khalani Mnzake wa Mulungu Kwamuyaya!

18

2009
Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
Ofalitsa:
Printed by Watch Tower Bible and Tract Society of South Africa NPC
1 Robert Broom Drive East, Rangeview, Krugersdorp, 1739, R.S.A.
Kabuku kano kanapulintiwa mu June 2014
Colinga ca kabuku kano ni kuthandiza panchito yophunzitsa Baibo
imene icitika padziko lonse. Zopeleka zodzifunila ni zimene
zimathandiza kuti nchito imeneyi ipite patsogolo.
Mu kabuku kano talembamo Cinyanja camasiku ano cimene

anthu ambili amamvela mosavuta. Baibo imene tasewenzetsa ni


Revised Nyanja (Union) Version, kusiyapo ngati taonetsa ina. Mukaona NW,
ndiye kuti mau amenewo acokela mu Baibo ya New World
Translation of the Holy Scriptures. Koma tasintha sipelingi
kuti igwilizane na Cinyanja cimene talemba.
You Can Be Gods Friend!
Cinyanja ( gf-CIN)
Made in the Republic of South Africa
Kabuku kano anakapangila ku Republic of South Africa

 P H U N Z I LO 1 

MULUNGU AKUPEMPHANI KUTI MUKHALE MNZAKE


Mulungu afuna kuti imwe mukhale mnzake. Kodi munaganizapo kuti
imwe mungakhale mnzake wa Mulungu? Abulahamu, amene anakhalako kale kwambili, anali mnzake wa Mulungu. (Yakobo 2:23) Baibo imakamba za anthu ena amene anali anzake a Mulungu, ndipo Mulungu anawadalitsa kwambili. Masiku ano, padziko lonse lapansi, pali anthu amene
akhala anzake a Mulungu. Na imwe mungakhale mnzake wa Mulungu.
Mulungu angakhale mnzanu woposa mnzanu aliyense. Mulungu salephela kucita zimene amalonjeza kwa anzake okhulupilika. (Salmo 18:25) Kukhala
mnzake wa Mulungu nikwabwino kuposa kukhala
na cuma. Munthu wolemela akafa, anthu ena amatenga cuma cake. Koma cuma cimene anzake a Mulungu ali naco, palibe munthu amene angacitenge.
Mateyu 6:19.
Anthu ena angayese kukuletsani kuphunzila za
Mulungu. Ngakhale anzanu kapena acibanja angafune kukuletsani. (Mateyu 10:36, 37) Ngati ena akusekani kapena kukuopsani, mudzifunse kuti, Kodi
ine nifuna kukondweletsa ndanianthu kapena Mulungu? Ganizilani izi: Ngati munthu wina akuuzani
kuti muleke kudya, kodi mungaleke? Iyai. Mukaleka kudya mungafe. Koma Mulungu angakupatseni moyo wosatha! Conco, musavomele kuti aliyense
akuletseni kuphunzila za kukhala mnzake wa Mulungu.Yohane 17:3.

 P H U N Z I LO 2 

MULUNGU NDIYE ANGAKHALE MNZANU WABWINO KWAMBILI


Kukhala mnzake wa Mulungu ni cinthu cabwino kuposa ciliconse cimene mungakhale naco. Iye angakuphunzitseni mmene mungapezele cimwemwe na
cisungiko. Ndiponso adzakumasulani ku
ziphunzitso zonama na ku vocitacita voipa. Iye adzayamba kumvela mapemphelo
anu. Adzakuthandizani kukhala na mtendele wa mmaganizo na cidalilo mwa
iye. (Salmo 71:5; 73:28) Panthawi ya mavuto Mulungu adzakuthandizani. (Salmo
18:18) Ndiponso Mulungu akulonjezani
mphatso ya moyo wosatha.Aroma 6:23.
Mukakhala mnzake wa Mulungu, mabwenzi ake nawo adzakhala anzanu.
Ndipo iwo adzakhala monga abale na
alongo anu. Adzakondwela kukuphunzitsani za Mulungu ndipo adzakulimbikitsani.
Mulungu sitilingana naye. Pamene
mufuna kukhala mnzake wa Mulungu,
pali mfundo ina imene muyenela kuidziwa bwino. Mfundo imeneyo ni yakuti;
mukakhala mnzake wa Mulungu sindiye kuti mwalingana naye iyai. Iye wakhalapo kwa zaka zambili, ali na nzelu na mphamvu zambili kuposa ife. Iye
ndiye woyenela kutilamulila. Conco ngati tifuna kukhala mnzake wa Mulungu,
tifunikila kumumvela na kucita zimene
amatiuza. Tikacita zimenezo, zinthu zidzatiyendela bwino.Yesaya 48:18.
4

 P H U N Z I LO 3 

MUFUNIKILA KUPHUNZILA ZA MULUNGU


Kuti mukhale mnzake wa Mulungu, mufunikila kuphunzila za iye. Kodi anzanu dzina lanu

alidziwa, ndipo amalitomola? Inde. Naye Mu


lungu amafuna kuti dzina lake mulidziwe, ndi
kuti muzilitomola. Dzina lake ni Yehova. (Salmo 83:18; Mateyu 6:9) Ndiponso mufunikila

kudziwa zimene amafuna na zimene samafu


na. Mufunikanso kudziwa anzake na adani ake.

Koma kudziwa munthu kumatenga nthawi. Baibo imakamba kuti ni cinthu canzelu kupatula nthawi ya kuphunzila za Yehova.Aefeso 5:
15, 16.
Anzake a Mulungu amacita zimene zimamukondweletsa. Mwacitsanzo, tiyeni tikambe za

anzanu. Ngati mumawavuta na kucita zinthu zimene samafuna, kodi angapitilize kukhala anzanu? Kutalitali! Ni cimodzimodzi na Mulungu.
Ngati imwe mufuna kukhala mnzake, mufunikila kucita zimene iye amafuna.Yohane 4:24.
Kodi zipembedzo zonse zingakuthandizeni kukhala mnzake wa Mulungu? Iyai.
Yesu, amene ni mnzake wa Mulungu wapa
mtima, anaphunzitsa ponena za njila ziwili.
Ina niikulu ndipo ili ndi anthu ambili oyendamo. Njila imeneyo imapeleka ku cionongeko. Koma njila ina niingono ndipo anthu
oyendamo ni ocepa. Njila imeneyi imapeleka
ku moyo wosatha. Conco, ngati mufuna kukhala mnzake wa Mulungu, mufunikila kuphunzila mmene mungamulambilile mu njila yoyenela.Mateyu 7:13, 14.
5

 P H U N Z I LO 4 

NANGA MUNGAPHUNZILE BWANJI ZA MULUNGU?

Mungaphunzile za Mulungu mwa kuwelenga Baibo. Kale kwambili, Mulungu anasankha anthu ena kuti alembe maganizo ake.
Zimene analemba zimapanga buku lochedwa
kuti Baibo. Masiku ano timaphunzila za Mu
lungu mwa kuwelenga Baibo. Baibo imachedwanso kuti Mau a Mulungu cifukwa muli
mau a Yehova, kapena kuti uthenga wake. Tingakhulupilile zimene Baibo imakamba cifukwa Yehova sanganame. Mulungu sakhoza
kunama. (Ahebri 6:18) Mau a Mulungu ndiye
coonadi.Yohane 17:17.

Mulungu anatipatsa mphatso zamtengo


wapatali. Koma Baibo imaposa zonse. Baibo ili monga kalata imene tate walembela ana
ake okondedwa. Imatiuza kuti Mulungu analonjeza kuti adzasintha dziko lapansi kukhala
paladaiso, malo abwino okhalamo. Imatiuzanso zimene Mulungu anacitila ana ake okhulupilika kumbuyo, zimene amawacitila masiku
ano, ndiponso zimene adzawacitila mtsogolo.
Imatithandizanso mmene tingacitile na mavuto athu na mmene tingapezele cimwemwe.
2 Timoteo 3:16, 17.
6

A Mboni za Yehova ni anzake a Mulungu.


Iwo adzakuthandizani kuimvetsetsa Baibo.
Ngati mufuna kuphunzila Baibo, auzeni adzakuthandizani. Samalipilitsa ndalama. (Mateyu
10:8) Ndiponso, mungaziyenda kumisonkhano yawo. Amacitila misonkhano imeneyi ku
malo oitanidwa kuti Nyumba ya Ufumu. Mukayamba kuyendako ku misonkhano imeneyi,
mudzaphunzila zambili ponena za Mulungu,
panthawi ingono cabe.

Mungaphunzilenso za Mulungu ku zinthu


zimene anapanga. Mwacitsanzo, Baibo imakamba kuti: Mulungu adalenga kumwamba
ndi dziko lapansi. (Genesis 1:1) Pamene Yehova analenga kumwamba, anapanganso dzu
wa. Nanga zimenezi zimatiphunzitsa ciyani
ponena za Mulungu? Zimatiphunzitsa kuti Yehova ali na mphamvu zambili. Ni yekha cabe
angakwanitse kupanga cinthu camphamvu

monga dzuwa. Zimatiphunzitsanso kuti Yehova ali na nzelu. Takamba conco cifukwa sembe

analibe nzelu, sakanakwanitsa kupanga dzuwa


limene limatulutsa kutentha na kuwala, koma
silikutha kapena kuzima.
Zimene Mulungu analenga zimaonetsa kuti
amatikonda. Ganizilani zipatso zosiyanasiyana zimene zili padziko lapansi. Yehova akanafuna, sembe anatipatsa mtundu umodzi cabe
wa zipatso, kapena osatipatsa cipatso ciliconse.
Koma, anatipatsa zipatso zambili zosiyanasiyana mu maonekedwe, ukulu, na kukoma kwake.
Zimenezi zimaonetsa kuti Yehova ni Mulungu
wacikondi, wopatsa, woganizila ena komanso
wabwino mtima.Salmo 104:24.
7

 P H U N Z I LO 5 

ANZAKE A MULUNGU ADZAKHALA MU PALADAISO


Paladaiso idzakhala malo osiyana na dziko limene tikhalamo panthawi ino. Mulungu sanafune ngakhale pangono kuti padziko lapansi pakhale mavuto alionse na zinthu zocititsa cisoni.
Mtsogolo, Mulungu adzasintha dziko lapansi kukhala Paladaiso. Kodi Paladaiso idzakhala malo
abwanji? Tiyeni tione zimene Baibo ikamba:
Anthu abwino. Mu Paladaiso mudzakhala cabe
anzake a Mulungu. Adzayamba kucitilana zinthu
zabwino wina na mnzake. Pamoyo wawo adzatsatila njila za Mulungu zolungama.Miyambo 2:21.
Zakudya za mwana alilenji. Mu Paladaiso simudzakhala njala. Baibo imakamba kuti: Mdzikomo mudzakhala zinthu [kapena, zakudya] zoculuka.Salmo 72:16.
Manyumba abwino na nchito zokondweletsa.
Mu Paladaiso padziko lapansi, banja lililonse lidzakhala na nyumba yawoyawo. Munthu aliyense
adzacita nchito imene idzamukondweletsa.Yesaya 65:21-23.

Kudzakhala mtendele padziko lonse. Nkhondo


na kuphana kudzakhala kulibe. Mau a Mulungu
amakamba kuti: [Mulungu] aletsa nkhondo ku
malekezelo a dziko lapansi.Salmo 46:8, 9.
Umoyo wabwino. Baibo imalonjeza kuti: Ndipo
wokhalamo [mu Paladaiso] sadzanena, Ine ndidwala. (Yesaya 33:24) Ndiponso, sipadzakhala
munthu wolemala kapena wosaona kapena wosamva kapena wosakamba.Yesaya 35:5, 6.

Zowawa, cisoni na imfa zidzacoka. Mau a Mulungu amakamba kuti: Ndipo sipadzakhalanso
imfa; ndipo sipadzakhalanso malilo, kapena kuli
la, kapena cowawitsa; zoyambazo zapita.Cibvumbulutso 21:4.
Anthu oipa sadzakhalamo. Yehova analonjeza
kuti: Oipa . . . adzalikhidwa [kucotsedwa] mdziko, aciwembu adzazulidwamo.Miyambo 2:22.
Anthu adzakondana na kulemekezana. Sikudzakhala kucitilana zosalungama, kupondelezana, dyela, na kuzondana. Anthu adzakhala
ogwilizana, ndipo adzatsatila njila za Mulungu
zolungama.Yesaya 26:9.

 P H U N Z I LO 6 

PALADAISO ILI PAFUPI!


Voipa vamene vicitika padziko lapansi vionetsa kuti Paladaiso ili
pafupi. Baibo inakambilatu kuti pamene Paladaiso ili pafupi kubwela, padzakhala nthawi yovuta kwambili. Nthawi imeneyo ndiye ino!
Onani vinthu vina vamene Baibo inakambilatu kuti vidzacitika:
Nkhondo Zikuluzikulu. Mtundu umodzi
wa anthu udzaukilana ndi mtundu wina, ndi
ufumu ndi ufumu wina. (Mateyu 24:7) Ulosi umenewu wakwanilitsika. Kuyambila mu

caka ca 1914, kwacitika nkhondo ziwili za


padziko lonse na nkhondo zina zingonozingono zambili. Ndipo anthu mamiliyoni
ambili afa mnkhondo zimenezi.
Kuwanda kwa matenda. Padzakhala milili [matenda owanda] mmalo akuti akuti.
(Luka 21:11) Kodi zimenezi zacitika? Inde.
Matenda a kansa, matenda a mtima, cifuwa
ca TB, maleliya, AIDS, na matenda ena amapha anthu mamiliyoni ambili.
Njala. Padziko lonse lapansi pali anthu
ambili amene alibe cakudya cokwanila. Caka
ciliconse anthu mamiliyoni amafa na njala.

Cimeneci ni cina codziwila kuti Paladaiso ili


pafupi. Baibo imakamba kuti: Padzakhala
njala.Marko 13:8.

10

Zivomezi. Kudzakhala . . . zivomezi mmalo akuti akuti. (Mateyu


24:7) Nazo izi zacitika mnthawi yathu. Kuyambila mu 1914, zivomezi
zapha anthu opitilila miliyoni imodzi.
Anthu oipa. Anthu adzakhala okonda ndalama ndi odzikonda
okha. Adzakhala okonda zokondweletsa munthu, osati okonda Mulungu. Ana adzakhala osamvela akuwabala. (2 Timoteo 3:1-5) Kodi simuvomeleza
kuti masiku ano pali anthu ambili amene ali
conco? Iwo alibe ulemu kwa Mulungu, ndipo
amavutitsa aja amene amafuna kuphunzila
za Mulungu.
Kucita zaupandu. Kudzakhalanso kuculuka kwa kusaweluzika. (Mateyu 24:12) Ngakhale imwe mungavomeleze kuti masiku ano
zaupandu zimacitika kwambili kusiyana na

kale. Anthu kulikonse amaopa kuwabela, ku

wanama kapena kuwapweteka.


Zonse izi zionetsa kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Baibo imakamba kuti: Pakuona zinthu izi zilikucitika, zindikilani
kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. (Luka
21:31) Kodi Ufumu wa Mulungu ni ciyani? Ni boma yakumwamba imene idzabweletsa Paladaiso padziko lino lapansi. Ufumu
wa Mulungu ukabwela udzacotsapo maboma onse a anthu.Danieli 2:44.

11

 P H U N Z I LO 7 

KUTENGAPO PHUNZILO PA
ZIMENE ZINACITIKA KUMBUYO
Yehova sadzalola kuti anthu oipa akakhalemo mu Paladaiso cifukwa angaiwononge.
Anzake cabe a Mulungu ni amene adzakhalamo.
Nanga anthu oipa cidzawacitikila ni ciyani? Kuti

mudziwe, mvelani vimene vinacitika mu nthawi


ya Nowa. Papita zaka masauzande pamene iye
anakhalapo. Anali munthu wabwino wolimbikila kucita zimene Yehova anali kufuna. Koma
anthu ena padziko lapansi anali kucita vinthu
voipa. Conco, Yehova anauza Nowa kuti adzabweletsa cigumula ca madzi kuti aononge anthu
onse oipa. Kuti Nowa na banja lake asafe pacigumula cimeneco, Yehova anamuuza kupanga cingalawa copulumukilamo.Genesis 6:9-18.

Nowa na Banja lake anapanga cingalawa. Cigumula cikalibe kubwela, Nowa anacenjeza
anthu, koma iwo sanamumvele. Iwo anapitiliza kucita vinthu voipa. Pamene Nowa anatsili
za kupanga cingalawa, analowetsamo vinyama.
Ndiyeno, iye na banja lake anangena mu cingalawa. Pambuyo pake, Yehova anabweletsa cimvula cikulu. Cimvula cimeneco cinagwa kwa masiku 40 usana na usiku. Ndipo madzi amenewo
anaculuka na kudzala padziko lonse lapansi.
Genesis 7:7-12.
12

Anthu oipa aja onse anafa, koma Nowa na


banja lake anapulumuka. Pambuyo pakuti
Yehova awapulumutsa ku cigumula, anawabwezela padziko lapansi limene anayeletsa mwa kucotsapo anthu oipa. (Genesis 7:22, 23) Baibo
imakamba kuti mtsogolo Yehova adzaononganso anthu amene safuna kucita zinthu zabwino. Koma anthu abwino sadzawaononga. Iwo
adzakhala na moyo wosatha mu Paladaiso padziko lapansi.2 Petro 2:5, 6, 9.

Masiku ano anthu ambili amacita vinthu


voipa. Mu dziko muli mavuto ambili. Yehova
watumiza Mboni zake mobwelezabweleza kuti
zicenjeze anthu, koma anthu ambili safuna kumvela mau ake. Iwo safuna kuleka makhalidwe
awo oipa. Safuna kuti Mulungu aziwauza zimene zili zabwino na zoipa. Kodi ni ciyani cidzacitikila anthu amene ali conco? Kodi tsiku lina
adzasintha makhalidwe awo? Ambili sadzaleka.
Ndiye cifukwa cake nthawi ibwela pamene Mulungu adzaononga anthu onse oipa, cakuti sadzakhalaponso.Salmo 92:7.
Dziko lapansi silidzaonongedwa; koma
adzalipanga paladaiso. Anthu amene ni anzake a Mulungu adzakhala na moyo wosatha mu
Paladaiso padziko lapansi.Salmo 37:29.
13

 P H U N Z I LO 8 

KODI ADANI A MULUNGU NI ANDANI?


Satana Mdyelekezi ndiye mdani mkulu
wa Mulungu. Iye ni mngelo amene anapandukila Yehova. Ndipo Satana ameneyo apitiliza kutsutsa Mulungu na kucititsa
mavuto akulu kwa anthu. Satana ni woipa.
Ni wabodza ndipo amapha anthu.Yohane
8:44.
Angelo ena anagwilizana na Satana kupandukila Mulungu. Angelo amenewo Ba
ibo imawaitana kuti viwanda. Monga mme
ne Satana alili, vi wanda navo ni adani a
anthu. Vimakonda kuvutitsa anthu. (Mateyu 9:32, 33; 12:22) Koma Yehova adzaono
ngelatu Satana na viwanda vake. Iwo atsala na nthawi ingono cabe yovutitsa anthu.
Cibvumbulutso 12:12.
Ngati mufuna kukhala mnzake wa Mulungu, osacita zimene Satana amafuna kuti

mucite. Satana na viwanda vake amazondana na Yehova. Iwo ni adani a Mulungu, ndipo amafuna kuti na imwe mukhale mdani wa Mulungu. Conco, muyenela kusankha
amene mufuna kukondweletsaSatana kapena Yehova. Ngati mufuna moyo wosatha,
muyenela kucita zimene Mulungu amafuna. Satana ali na njila zambili zonamilamo anthu. Iye amapusitsa anthu ambili.Cibvumbulutso 12:9.

14

 P H U N Z I LO 9 

KODI ANZAKE A MULUNGU NI ANDANI?


Yesu Khristu ni Mwana wa Mulungu,
ndipo ni mnzake wapamtima. Poyamba, Yesu anali kumwamba monga
mngelo wamphamvu. (Yohane 17:5) Ndiyeno, anabwela kudzakhala munthu padziko lapansi, kudzaphunzitsa coonadi
ponena za Mulungu. (Yohane 18:37) Pambuyo pake, anataya moyo wake waumunthu kuti apulumutse anthu omvela Mulungu ku ucimo na imfa. (Aroma 6:23)
Panthawi ino, Yesu ni Mfumu ya Ufumu
wa Mulungu. Ufumu umenewo ni boma
imene idzabweletsa Paladaiso padziko lapansi pano.Cibvumbulutso 19:16.
Angelo nawo ni anzake a Mulungu. Angelo sanayambile moyo wawo padziko lapansi. Mulungu anawalengela kumwamba akalibe kupanga
dziko lapansi. (Yobu 38:4-7) Angelo aliko mamiliyoni ambili. (Danieli 7:10) Anzake a Mulungu akumwamba amenewa amafuna kuti anthu
aphunzile coonadi conena za Yehova.Cibvumbulutso 14:6, 7.
Mulungu ali na anzake ena padziko lapansi;
iye amawaitana kuti mboni zake. Mboni, ni
munthu amene mu khoti amanena zimene adzi
wa ponena za munthu kapena cinthu cina. A

Mboni za Yehova amauza anthu zimene adziwa


ponena za Yehova na cifunilo cake. (Yesaya 43:10)
Mofanana na angelo, a Mboni amafuna kukuthandizani kuti muphunzile coonadi conena za
Yehova. Afuna kuti na imwe mukhale mnzake wa
Mulungu.
15

 P H U N Z I LO 10 

MMENE MUNGADZIWILE CIPEMBEDZO COONA


Ngati mufuna kukhala mnzake wa Mulungu, mufunika kulambila mu cipembedzo cimene iye amavomeleza. Yesu anakamba kuti olambila oona adzalambila
Mulungu mogwilizana na coonadi. (Yohane 4:23, 24) Pali njila imodzi cabe yoyenela kulambilila Mulungu. (Aefeso 4:4-6) Cipembedzo coona cimapeleka ku moyo wosatha,
koma cipembedzo conama cimapeleka ku
imfa.Mateyu 7:13, 14.

Cipembedzo coona mungacidziwe mwa


kuona zocita za anthu ake. Cifukwa Yehova ni wabwino, nawo amene amamulambila mnjila yoyenela, ayenela kukhala anthu
abwino. Monga mmene mtengo wabwino wa
maolenji umabalila maolenji abwino, naco
cipembedzo coona cimakhala na anthu abwino.Mateyu 7:15-20.
Anzake a Yehova amalemekeza Baibo

kwambili. Amadziwa kuti Baibo inacokela


kwa Mulungu. Amalola mau a mBaibo kuwatsogolela mmoyo wawo. Mau a Mulungu

amawathandiza kudziwa mocitila na mavuto awo, ndipo amawathandiza kuphunzila za


Mulungu. (2 Timoteo 3:16) Ndipo iwo amacita zimene amalalikila.

16

Anzake a Yehova amakondana wina na


mnzake. Yesu anaonetsa cikondi kwa anthu
mwa kuwaphunzitsa za Mulungu, na kucilitsa odwala. Komanso, amene ali mu cipembezo coona amakondana wina na mnzake. Mofanana na Yesu, iwo samaona anthu
osauka kapena a mtundu wina kukhala apa

nsi. Yesu anakamba kuti anthu adzawadziwa


ophunzila ake cifukwa ca kukondana kwawo.
Yohane 13:35.
Anzake a Mulungu amalemekeza dzina la
Mulungu, lakuti Yehova. Ngati munthu

wina akana kusewenzetsa dzina lanu, kodi


angakhale mnzanu wazoona? Kutalitali!
Ngati tili na mnzathu timamutomola dzina lake, ndipo timakamba zabwino za iye
kwa ena. Conco anthu amene afuna kukha
la anzake a Mulungu afunika kusewenzetsa
dzina lake na kuuzako ena za iye. Ni zimene
Yehova afuna kuti tizicita.Mateyu 6:9; Aroma 10:13, 14.
Mofanana na Yesu, Anzake a Mulungu
amaphunzitsa ena za Ufumu wa Mulungu. Ufumu wa Mulungu ni boma yakumwamba imene idzabweletsa paladaiso padziko lapansi. Anzake a Mulungu amauzako
anthu ena za uthenga wabwino wa Ufumu
wa Mulungu.Mateyu 24:14.
A Mboni za Yehova amalimbikila kukhala
anzake a Mulungu. Amalemekeza Baibo na

kukondana wina na mnzake. Amasewenzetsa


dzina la Mulungu na kulilemekeza, komanso
amaphunzitsa ena za Ufumu wake. A Mboni
za Yehova padziko lonse lapansi amalambila
mu cipembedzo coona.
17

 P H U N Z I LO 11 

KANANI CIPEMBEDZO CONAMA!

Satana na viwanda vake safuna kuti imwe muzitumikila Mulungu. Iwo amafuna kuti acotse munthu aliyense ku mbali ya Mulungu ngati
angakwanitse. Kodi amayesa kucita zimenezi kupitila mu njila za bwanji? Imodzi mwa njila zimenezo ni cipembedzo conama. (2 Akorinto 11:1315) Cipembedzo ciliconse cimene cimaphunzitsa
zimene sizicokela mu Baibo ni conama. Cipembedzo conama cili monga ndalama yabodzangakhale kuti ingaoneke monga ni yazoona, imakhala ilibe nchito. Ingakubweletseleni mavuto akulu.

Mabodza a cipembedzo sangakondweletse Yehova, Mulungu wa coonadi. Pamene Yesu anali padziko lapansi, panali anthu ena acipembedzo amene anafuna kumupha. Anali kuona kuti
cipembedzo cawo ndiye cinali coona. Iwo anakamba kuti: Tili naye tate mmodzi ndiye Mulungu. Kodi Yesu anavomeleza zimenezo? Kutalitali! Koma iye anawauza kuti: Inu muli ocokela
mwa atate wanu Mdyelekezi. (Yohane 8:41, 44)
Anthu ambili masiku ano amaganiza kuti amalambila Mulungu, koma kwenikweni amatumikila

Satana na viwanda vake!1 Akorinto 10:20.


18

Monga mmene mtengo umene uli na matenda umabalila


zipatso zoipa, cipembedzo conama cimakhala na anthu
ocita voipa. Padziko lapansi pali mavuto ambili cifukwa ca
vinthu voipa vimene anthu amacita. Pali uhule, kumenyana, kuba, kupondelezana, kuphana, na kugona akazi mokakamiza. Ambili amene amacita vinthu ivi ali na cipembezo cawo, koma cipembedzo cawo siciwalimbikitsa
kucita zinthu zabwino. Kuti akhale anzake a Mulungu afunikila kuleka kucita voipa.Mateyu 7:17, 18.
Cipembedzo conama cimaphunzitsa anthu kupemphela ku mafano. Mulungu amaletsa kupemphela ku mafano. Ndipo zimenezi ni zomveka. Mwacitsanzo, kodi mungamve bwanji ngati munthu wina,
mmalo mokamba na imwe, amakamba cabe na cithunzithunzi kapena cipikica canu? Kodi mungakambe
kuti munthu ameneyo ni mnzanu wazoona? Iyai. Conco, Yehova amafuna kuti anthu azikamba naye, osati
kukamba na cifanizilo copanga kapena cipikica cimene cilibe moyo.Eksodo 20:4, 5.
Cipembedzo conama cimaphunzitsa kuti si kulakwa kupha anthu pankhondo. Yesu anakamba kuti
anzake a Mulungu adzakhala okondana pakati pawo.
Ife sitingaphe anthu amene timakonda. (Yohane
13:35) Ngakhale kupha anthu oipa ni kulakwa. Pamene adani a Yesu anabwela kuti amumange, iye sanalole kuti ophunzila ake amenyane nawo kuti amucinjilize.Mateyu 26:51, 52.
Cipembedzo conama cimaphunzitsa kuti anthu
oipa adzapsa mmulilo ku helo. Koma Baibo imaphunzitsa kuti ucimo umapeleka ku imfa. (Aroma
6:23) Yehova ni Mulungu wacikondi. Nanga Mulungu wacikondi angaoche anthu mmoto kwamuyaya?
Iyai, sangacite zimenezo. Mu Paladaiso mudzakhala
cipembedzo cimodzi cabe, cimene Yehova amavomeleza. (Cibvumbulutso 15:4) Mulungu adzaononga vipembedzo vonse vimene vimaphunzitsa mabodza a Satana.
19

 P H U N Z I LO 12 

KODI MUNTHU AKAFA CIMACITIKA KWA IYE NI CIYANI?


Munthu akafa ndiye kuti alibe moyo. Imfa ili monga tulo tukulu, kapena
kuti tulo tofa nato. (Yohane 11:11-14) Anthu akufa sangamve, sangaone, sangakambe, kapena kuganiza ciliconse. (Mlaliki 9:5, 10) Cipembedzo conama cimaphunzitsa kuti anthu akafa amayenda ku dziko la mizimu kukakhala pamodzi
na mizimu ya makolo awo. Koma Baibo siiphunzitsa zimenezi.
Anthu amene anafa sangatithandize pa ci
liconse, ndipo sangatiukile ciwanda. Anthu
ambili amakonda kucita miyambo na kupeleka nsembe zimene amakhulupilila kuti zimakondweletsa anthu amene anafa. Zimenezi Mulungu sakondwela nazo cifukwa ni mabodza a
Satana Mdyelekezi. Sizingakondweletse ngakhale
akufa cifukwa alibe moyo. Sitiyenela kuopa kapena kulambila anthu amene anafa. Tifunikila kulambila Mulungu yekha cabe.Mateyu 4:10.
Anthu amene anafa adzauka. Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kuti akakhale na moyo mu
paladaiso padziko lapansi. Zimenezi zidzacitika mtsogolo. (Yohane 5:28, 29; Macitidwe 24:15)
Kwa Mulungu, ni cosavuta kuukitsa anthu akufa, monga mmene cilili cosavuta kwa imwe kuutsa munthu amene ali mu tulo.Marko 5:22, 23,
41, 42.
Maganizo akuti anthu ife sitimafelatu ni mabodza amene Satana Mdyelekezi amafalitsa.

Satana na viwanda vake amapangitsa anthu kuganiza kuti mizimu ya anthu amene anafa ili na
moyo. Amakamba kuti mizimu imeneyo ni imene imadwalitsa anthu na kubweletsa mavuto ena.
Nthawi zina Satana amanama anthu kupitila
mmaloto na masomphenya oona vinthu. Yehova
amawazonda anthu amene amayesa kukamba na
anthu amene anafa.Deuteronomo 18:10-12.

 P H U N Z I LO 13 

MATSENGA NA UFITI NI VINTHU VOIPA


Satana amafuna kuti muzicita vamatsenga.
Anthu ambili amapeleka nsembe ku mizimu
ya akufa kuti iziwachinjiliza. Amacita zimenezi cifukwa amaopa mphamvu za mizimu yoipa. Amavala mphete (malingi) zamatsenga kapena mabango (makhoza). Amamwa kapena
kudzola mankhwala amene amaganiza kuti ali
na mphamvu zowachinjiliza. Ena amabisa mankhwala mu nyumba kapena kukumbila pansi kuti achinjilize nyumba yawo, kapena kuti

kuitsilikila. Palinso ena amene amasewenzetsa


mankhwala cifukwa amakhulupilila kuti adzawapatsa mwayi pa bizinesi, pamayeso, kapena
ofunila mkazi kapena mwamuna.

Njila yabwino kwambili yodzichinjiliza


kwa Satana ni kukhala mnzake wa Yehova.
Yehova na angelo ake ni amphamvu kwambili

kuposa Satana na viwanda vake. (Yakobo 2:19;


Cibvumbulutso 12:9) Yehova ni wokonzeke
la kusewenzetsa mphamvu zake kuti achinjili
ze anthu amene ni anzake. Amenewa ni anthu
amene ali okhulupilika kwa iye na mtima wonse.2 Mbiri 16:9.
Mau a Mulungu amakamba kuti: Musamacita nyanga kapena kuombeza. Yehova
amazonda zamatsenga, ufiti, kapena kuombeza. Zimenezi amazizonda cifukwa munthu
amene amacita zinthu zimenezi amayamba
kulamulilidwa na Satana Mdyelekezi.Levitiko 19:26.
21

 P H U N Z I LO 14 

ANZAKE A MULUNGU AMAKANA KUCITA VOIPA


Satana amanyengelela anthu kuti azicita
vinthu voipa. Munthu amene amafuna kukhala mnzake wa Mulungu, naye afunika kuzonda vimene Mulungu amazonda. (Salmo
97:10) Onani vinthu vina voipa vimene anzake a Mulungu amakana kucita:
Macimo a zogonana. Usacite cigololo. (Eksodo 20:14) Nako kugonana mukalibe kukwatilana ni
kulakwa.1 Akorinto 6:18.

Kuledzela kapena kukolewa.

Oledzela, . . . sadzalowa Ufumu


wa Mulungu.1 Akorinto 6:10.

Kupha munthu, Kucotsa mimba.


Usaphe.Eksodo 20:13.

Kuba. Usabe.Eksodo 20:15.

Kunama. Yehova amazonda munthu wa lilime lonama.Miyambo 6:17.


22

Ciwawa na kukalipa kopitilila. Yehova . . .


amuda woipa ndi iye wakukonda ciwawa. (Salmo 11:5) Nchito za thupi, . . . [ziphatikizapo]
kupsa mtima.Agalatiya 5:19, 20.
Njuga. Muleke kuyanjana ndi aliyense . . . waumbombo.1 Akorinto 5:11, NW.
Kuzondana cifukwa cosiyana khungu
(nkhanda) kapena kusiyana mitundu. Kondanani nao adani anu, ndi kupemphelela iwo
akuzunza inu.Mateyu 5:43, 44.
Zimene Mulungu amatiuza zimatipindulitsa. Nthawi zina cimavuta kukana voipa. Koma
Yehova na Mboni zake angakuthandizeni kukana kucita voipa vimene Mulungu samafuna.
Yesaya 48:17; Afilipi 4:13; Ahebri 10:24, 25.

23

 P H U N Z I LO 15 

ANZAKE A MULUNGU AMACITA VINTHU VABWINO


Ngati muli na mnzanu amene mumakonda
na kumulemekeza, mumayesa kukhala monga iye. Baibo imakamba kuti: Yehova ndiye
wabwino ndi wolunjika mtima. (Salmo 25:8)
Kuti tikhale mnzake wa Mulungu, tifunikila kukhala anthu abwino ndi a mtima wolungama. Baibo imakambanso kuti: Khalani
akutsanza a Mulungu; monga ana okondedwa
ndipo yendani mcikondi. (Aefeso 5:1, 2) Onani mmene mungacitile zimenezi:
Muzithandiza ena. Ticitile onse cokoma.
Agalatiya 6:10.
Khalani wolimbikila panchito. Wakubayo
asabenso; koma makamaka agwilitse nchito,
nagwile nchito yokoma ndi manja ake.Aefeso 4:28.
Khalani munthu waukhondo ndi wamakhalidwe abwino. Tizikonzele tokha kuleka
codetsa conse ca thupi ndi ca mzimu, ndi kutsiliza ciyelo mkuopa Mulungu.2 Akorinto
7:1.

24

Muzikondana na kupatsana ulemu


na onse a mbanja mwanu. Yense
akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; . . . ndipo mkaziyo akumbukile kuti aziopa mwamuna.
Ananu, mvelani akukubalani.Aefeso
5:336:1.

Kondani anthu ena. Tikondane


wina ndi mnzake: cifukwa kuti cikondi cicokela kwa Mulungu.1 Yohane 4:7.
Muzimvela malamulo a dziko.
Anthu onse amvele maulamulilo aakulu [boma]; . . . Pelekani kwa anthu
onse mangawa awo; msonkho kwa eni
ake a msonkho.Aroma 13:1, 7.

25

 P H U N Z I LO 16 

ONETSANI CIKONDI CANU KWA MULUNGU


Kuti ubwenzi wanu na munthu wina upitilize, mufunikila kumakambitsana. Mumamumvela, nayenso amakumvelani. Ndiponso,
mumauzako anthu ena zinthu zabwino ponena za iye. Ni cimodzimodzi na kukhala mnzake wa Mulungu. Onani zimene Baibo imakamba pankhani imeneyi:
Muzikamba na Yehova mpemphelo nthawi zonse. Limbikani cilimbikile mkupemphela.Aroma 12:12.

Muziwelenga Mau a Mulungu, Baibo. Lemba lililonse adaliuzila Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzelo,
cilangizo ca mcilungamo.2 Timoteo 3:16.
Muziphunzitsa ena za Mulungu. Cifukwa
cake mukani, phunzitsani anthu a mitundu
yonse, . . . asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulilani inu.Mateyu 28:19, 20.

26

NYUMBA YA UFUMU ya Mboni za Yehova

Khalani mnzawo wa aja amene ni anzake a Mulungu. Ukayenda ndi anzelu udzakhala wanzelu.Miyambo 13:20.
Muzipezeka kumisonkhano ku Nyumba
ya Ufumu. Tiyeni tiganizilane wina ndi
mnzake, kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi
nchito zabwino.Ahebri 10:24, NW.
Muzithandiza panchito ya Ufumu na zopeleka zanu. Yense acite monga atsimikiza
mtima, si mwa cisoni kapena mokakamiza,
pakuti Mulungu akonda opeleka mokondwelela.2 Akorinto 9:7.

27

 P H U N Z I LO 17 

KUTI MUSUNGE UBWENZI, MUFUNIKILA


KUKHALA MUNTHU WAUBWENZI
Kuti ubwenzi upitilize payenela kukhala cikondi. Mukaphunzila zambili ponena za Yehova, cikondi canu kwa iye cidzakula kwambili. Ndipo cikondi canu pa iye cikakula, cifuno
canu comutumikila naco cidzakula. Zimenezi zidzakuthandizani kukhala wophunzila wa Yesu

Khristu. (Mateyu 28:19) Mukalowa mu gulu la


Mboni za Yehova, limene ni banja lacimwemwe,
mudzakhala mnzake wa Mulungu kwamuyaya.

Kodi mufunika kucita ciyani kuti mulowe mu


banja limeneli?
Mufunika kuonetsa cikondi canu kwa Mulungu mwa kusunga malamulo ake. Ici ndi cikondi ca Mulungu, kuti tisunge malamulo ake;
ndipo malamulo ake sali olemetsa.1 Yohane
5:3.
Muzicita zimene mumaphunzila. Yesu
anasimba nthano ina imene imaonetsa zimenezi. Munthu wocenjela anamanga nyumba yake pa cimwala kapena kuti thanthwe.
Koma munthu wopusa anamanga nyumba
yake pamcenga. Pamene cimvula camphepo
cinabwela, nyumba imene anamanga pacimwala siinagwe. Koma nyumba imene anamanga pamcenga inagwa kugwelatu. Ndiyeno, Yesu anakamba kuti anthu amene
amamvela, na kucita zimene amawaphunzitsa, ali monga munthu wocenjela uja,
amene anamanga nyumba yake pacimwala.
Koma awo amene amamvela cabe zimene iye
amaphunzitsa koma sazicita, ali monga munthu wopusa uja, amene anamanga nyumba
yake pamcenga. Kodi imwe mufuna kukhala monga munthu uti?Mateyu 7:24-27.
28

Kudzipeleka. Kudzipeleka kumatanthauza kumuuza Yehova mpemphelo kuti mufuna kucita


cifunilo cake kwamuyaya. Kucita cifunilo ca Mulungu kumaonetsa kuti ndimwe wophunzila wa
Yesu Khristu.Mateyu 11:29.
Ubatizo. Ubatizidwe ndi kusamba kucotsa macimo ako, nuitane pa dzina lake.Macitidwe
22:16.
Tumikilani Mulungu na mtima wonse. Ciliconse mukacicita, gwilani nchito mocokela mumtima, monga kwa Ambuye [Yehova, NW], osati
kwa anthu ayi.Akolose 3:23.

29

 P H U N Z I LO 18 

KHALANI MNZAKE WA MULUNGU KWAMUYAYA!


Kuti mupeze mnzanu wapamtima mufunika kulimbikila, ndipo kuti ubwenzi
wanu ukhalitse mufunikanso kulimbikila. Ngati mulimbikila kukhala mzake
wa Mulungu, mudzapeza madalitso ambili. Yesu anauza anthu amene anakhulupilila mwa iye kuti: Coonadi cidzakumasulani.
(Yohane 8:32) Kodi zimenezi zitanthauza ciyani?
Coonadi cingakumasuleni panthawi ino.
Cingakumasuleni ku viphunzitso vonama
na mabodza amene Satana amafalitsa. Mungakhalenso osiyana na anthu ambili ame
ne sadziwa Yehova. Anthu amenewo alibe
ciyembekezo. (Aroma 8:22) Anzake a Mulungu anamasuka ngakhale ku mantha akuopa imfa.Ahebri 2:14, 15.
Mungapeze ufulu mu dziko la Mulungu
latsopano. Ha, ati kukondweletsa ufulu
umene uli mtsogolo! Mu Paladaiso padziko
lapansi simudzakhala nkhondo, matenda,
kuphana, na vinthu vina voipa. Simudzakhalanso kusauka kapena njala. Mudzakhala mulibe kukalamba kapena kufa. Ndipo
simudzakhala mantha, kapena kupondelezana, ngakhale zosalungama zilizonse. Kunena
za Mulungu, Baibo imakamba kuti: Muolo
wetsa [kufewetsa] dzanja lanu, nimukwanilitsa zamoyo zonse cokhumba cawo.Salmo 145:16.

Anzake a Mulungu adzakhala na moyo


wosatha. Moyo wosatha ni mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu adzapatsa anthu onse amene akulimbikila kukhala anzake. (Aroma 6:23) Ha, ganizani
cabe zimene mungakwanitse kucita mukakhala na moyo wosatha!
Mudzakhala na nthawi yokwanila kucita zinthu zambili. Mwina mungafune
kuphunzila kuliza cida coimbila nyimbo.
Kapena mungafune kuphunzila kujambula zithunzithunzi kapena kukhala
kalipentala. Mungafunenso kuphunzila
za zinyama na zomela. Kapena mungafune kuyenda kumalo osiyanasiyana kukaona malo na anthu. Mukadzakhala na
moyo wosatha, mudzakwanitsa kucita zinthu zonse zimenezi.
Mudzakhala na nthawi yokwanila yopanga mabwenzi ambili. Mukadzakha
la na moyo wosatha mudzadziwana na
anthu ena ambili amene ni anzake a Mu
lungu. Mudzadziwa maluso awo na makhalidwe awo abwino, ndipo na imwe
adzakhala anzanu. Adzakukondani, ndipo na imwe mudzawakonda. (1 Akorinto
13:8) Mukadzakhala na moyo wosatha,
mudzakala na nthawi yokwanila yopanga
ubwenzi na munthu aliyense padziko lapansi! Koma copambana vonse ni cakuti,
ubwenzi wanu na Mulungu udzalimbilalimbila mkupita kwa zaka. Tikufunilani
ubwenzi wamuyaya na Mulungu!

31


Kodi mufuna kudziwa zambili?

gf-CIN
140704

Dziwitsani Mboni za Yehova pa www.jw.org.

You might also like