You are on page 1of 14

CHILI KUTI NDI

NDAKATULO ZINA

By Ridson Sambuka
CHILI KUTI

Chili kuti chija unkabdiwonetsa pachiyambi

Ndili wanthete ndi wa nyonga zake

Anga Ali njo wonga papaya

Achitsonzera akuchotsana zibwano

Ndikuthokoza patali ngati la m' nyezi

Lija lopanga ma ubwenzi ndi mbewu

Ndipo motsangalala zikuyimba pa iwo

Ndipo iwe unkatero pa ine

Ndati chili kuti chija unkandininkha matsiku azana aja

Ndipo timawu tanthetemya tinkatuluka pa iwe

Koma zonsezi kudali kuwukodola

Mtima wanga ku msampha

Womwe wandilatsa pamtima panga

Ndikuwononga mapapo anga

Koma zonsezi njoka yake ndi iwe?

Mkulingadi utayenda naye

Alidere ndazindikira.

Unkabwera ndi katundu osiyanasiyana


Ndicholinga choti undikokere ku gologota

Kwamazunzo azawoneni

Wandisenzetsa mtanda pano ndisaname

Wandisiya ndikuzunzika ndi iti

Tomwe tawononga m'thupi mwanga

Ndidali mtengo wa malambe ine

Koma lero ndine munthu womvetsa chisoni

Ngakhale kamphepo kakunditika

Pano moyo wanga uli pamoto

Ndikuti chili kuti chija unkandininkha

Tikafatsa poduka mphepo

Timawu tokodola moyo unkandininkha

Wakumtima wako unkakamba kuti ndine

Koma lero ndayimbira mfiti m'manja

Wandigwiritsa fuwa la Moto iwe

Ndakhulupilira ndiwedi khang'a

Chilombi chotheratu

Ndiwe mfiti yayikazi

Kundisiya ndekha ije munthu wamayi

Moyo wanga utawunyenya mtizidutswa

Wandisiyira tiwanati

Kitisamalira ndekha ndekha


Komatu unkabdiwonetsa pachiyambi

Kuti limodzi tizakhala ndithu

Lero ndiwe kukutchayira lamya sukuyankha

Wapeza tiyendayenda

Tikakuboola mthumba uzandifuna

Koma uyende bwino

Ndi mtima wako wa mkhiziwo

Chili kuti?

2. ANKATERO NDANI?

Ankatero ndani kuti sizizatero

Chimwemwe kudzadza tsaya chonchi lero

Kunyadiratu wanga ulemerero

Ambiri amati ndi nkhambankamwa

Koma lero ndizoonadi

Ndipo awo achita tsembwe

Asowa mtengo wogwira

Ndipo awuma mate mkamwa

Poti yawo ayitayira pachabe

Ndinkawona ngati ndikuchedwa

Komano pano ndazindikira

Kuti ukadekha ankhono maso umawona

Ndikumaseka chikhakhali
Ndikakumbuka zomwe awo ankayankhula

Kuyiwala kuti kunena kwa ndithendithe

Anazitengera Nanthambwe

Komano zonsezi zandikokera kudoko

Lozaza ndi mtendere ndi chikondi

Chisatha kwamuyaya

Komano ndikuti ndi yani ankatero aja

Lero okha opanda mnyanga akupukutsa

Kuwusowa wamumtima mtendere

Diso lofiira kundiwonetsera

Mumtima mwawo kutentha ngati makala amoto

Chifukwa Cha yanga mphoto

Akuyetsera kundikoretsa chona

Poti makutu awo agontha

Pomva zomwe zandichitikira

Ndatitu ankakamba aja alikuti?

Nanga akamba chiyani lero?

Poti ndamupeza wanga wakumphasa

Yemwe walasa mtima wanga

Ndipo ndi yemwenso wandikodolera ku dziko lachikondi

Lomwe ndinkalilakalaka pa moyo wanga


3. ANGA

Mozyolika nkhope chisoti ndavula

Ngakhale abemberezi ena

Sakumvetsa zomwe andichitira

Ndipo ageya zochuluka kwambiri

Zokhudza ine ndi anga

Komano ngati Tsokonombwe tayenda

Mpaka kufika pomwe tili

Mwakhala mukuyankhula mwathamu

Kuyiwala anazitengera Nanthambwe

Alowa m'chala mwawatchula

Chonsecho limodzi mukayenda

Kumudziwadi fisi sikubadwa kale

Komano kuyenda usiku anzanga

Anga anzanga ndumawapatsa ulemu

Yathukuta losamba agwira

Wefuwefu kukonza langa

Kuwopa ndingazachite tsembwe pa mawa

Angatu abale andithandiza

Kundininkha ondithandiza ndithu


Konza kapansi kuti

Kam'mwamba katsike

Anga abale anzanga

Ndikukanika kusimba

Ndipo mukamandiwona lero chonchi

Sichunanso ayi anzanga

Komano zonsezitu ndi anga

Omwe asintha moyo wanga.

4. TSOGOLO

Mwapang'onopang'ono ulendiwu ndayenda

Poti tsokonombwe adatha mtunda ndikudumpha

Ankandipatsa othandiza ndithu

Koma chifukwa Cha ukhutukumve wanga

Kumbali ndinkangowatayira

Poti sindinkalingalira kuti zizatero

Koma lero Bondo ndikunong'oneza

Inki kwakanthawi ndidayimwa anthuni

Ndipo ndi chimwemwe ndinkayembekezera labwino

Ndipo awo ondimwetsawo

Adayigwira yawo ntchito ndithu

Koma mphulumpulu zanga


Zandilephetetsa khumbo langa

Zachisoni lero ndikubuula ngati fisi ogwera m'mbuna

Lero thukuta ndangokhetsera pachabe

Ndimkalimbana ndi am'maanja awo

Omwe ndinkakumana nawo

Ankandinyengeza nditochepa

Tomwe ankandipatsa

Chifukwa sindinkadziwa

Kuti ndikuwononga langa kutere

Lero yalekaleka ndidayipeza

Mwachangu pamoyo wanga

Lero wakuda galu sakuchoka

Pakhomo panga

Ngati kapilipili moyo wanga ukuwawatsa

Kusowa mtengo wogwira

Pano ndikusamala ndekha uyu Ali m'manjayi

Zonsezitu ndikugontha m'khutu kwanga.


5. ALI PAFUPI

Mwanyozedwa kwakanthawi ndithu

Moyikhetsera thukuta mwayigwira

Mwazunzika anthuni

Kuyigwira ntchito molimbika

Poti kanthu ndi khama

Phwiti adakwatira njiwa.

Waminga nsewu mwapondadi ndithu

Mikwingwirima yosaneneka

Mphenvu mdyera kunthiko mwanenedwa

Mokwanira mwapilira ndithu

Kuzitonzo zonse zomwe mwalandira

Moleza mtima mwakhala nawo ndithu

Poti ukadekha woyera mkanda umavala

Nyangwita lanu thupi mwakoleka

Wopha nyerere mwayenda

Kunyozedwa kosaneneka m'njiramu

Wobooka mthumba ndiye dzina lanu

Mwagwiritsidwa yopanda malipiro anthuni

Kumapiri akutali mwakatuta nkhuni


Inki mwaimwa mozunzika nthuni

Mukafika nawo kuti mwanenedwa

Achikondi akuninkhani okulimbikitsani ndithu

Ndipo mwa mvano wamavu mwawagwiritsa ntchito

Ngakhale ena mwa inu ankanyozera

Paja zengerezu adalida kwawukwawu

Koma limbani mtima anthuni.

6. CHIKONDI

Ndikakhala duu!

Kulingalira za iwe

Ubongo wanga ukumafa bwazi

Ndikumasowa mtendere

Kupukutsa opanda nyanga

Chifukwa Chosakumvetsetsa

Ndiwe yani?

Ndati wadulutsa mutu wazizwa

Mikoko yogona

Wabweretsa chisoni, chisangalalo

Ngakhalenso chidani
Wabweretsa pamodzi anthu osiyanasiyana

Alowa mchala ngakhalenso makhumutcha

Mbambadi! Ndisaname

Wandigonthetsa m'khutu

Ndiwe yani?

Ukakhala pakati pa anthu awiri

Zimavuta kuwalekanitsa

Amalumikizana m' kulimba ndi

Ngati Pali ulimbo

Ngakhale ena atayetsera kutero

Yawo awiriwa mitima

Imakhala dyokodyoko

Kulingalira kuwona winayo

Ndiwe yani?

Ndagwidwa njakata

Maka ndikamanva za iwe

Ana , achinyamata , ngakhalenso achikulire

Pakati pawo umapezeka

Umafika mosadzindikirika

Ndipo yosiyana mitima umayikokera pamodzi

Ndiwe yani?
7. NDIKADADZIWA

Ndikadadziwa sindinkalingalira chonchi

Changa chonse sinkanachisanula

Ndikadangokhala chete!

Osalingalira za iwe

Poti ndawuma nawe mate mkamwa

Ndikakhala Phee!

Chikumbumtima chikumandigwira

Chifukwa Cha zonukha zako

Zomwe ndagontha nawo m'khutu

Ndikadadziwa kuti udzidzatero

Ulendo wako mbambao!

Ndikadawudulira panjira

Wandikhumudwitsa ndisaname

Ndipo ndakhunzika koopsa

Poti sindidayembekezere kusunga chilombo

Ndiwe otani

Kuchita zosemphana ndi chikhalidwe

Ndati ndikadadziwa
Yanga sindikadayitayira pa iwe

Poti sindidayembekezere madzi amphusi

Ndipo ndikulakalaka

Nditangokusiya pa mtsika

Mwina chipsinjochi mkulekana nawo

Aaaa! Ndisaname

Ndathedwa nawe nzeru

Pena ndikumadzifunsa

Mafunso osowekera mayankho

Koma ndiwe mwana wangadi

Ndipo ndikumasowa mtendere mumtima

Ndikumachita tsembwe pamaso panzanga

Ndikumadziyimba mlandu wawukulu

Maka ndikamanva anthu akukamba za iwe

Ndikumasowa chokamba

Choyankhula chikumagwera mmimba

Koma ndikadadziwa

Sukadafika msinkhu uliwo.

You might also like