You are on page 1of 3

Expressive arts mayeso a chigawo chachitatu

Malangizo:

 Yankhani mafunso onse


 Pepalali lili ndi magawo awiri A ndi B
 Tsatilani malangizo pa gawo lililonse

Gawo A: Multiple choice

Zunguzani yankho lolondola

1. Tchulani chochitika chimodzi m’madera anu


a. Mganda
b. Maliyeliye
c. Chinamwali

2. Kodi zochitika m’madera anu zimachitika nthawi yanji?


a. Tisanakolole
b. Zinja
c. Tikamaliza kukolola mbewu

3. Tchulani udindo umodzi opeza m’dera lanu


a. Kukhala fisi
b. Kukhala onyamula tomato
c. Kukhala mphunzitsi

4. Kodi zidole zimakongolesedwa ndi chani?


a. Madzi
b. Udongo
c. Utoto

5. Nenani chithu chimodzi chomwe chingapangidwe kuchokera mawaya


a. Chipande
b. Mpoto
c. Galimoto
6. Tchulani masewero amachita ana ku mudzi
a. Jingo
b. Kusewera
c. Zamakiki

7. Tchulani zipangizo zopangira zidole


a. Dongo
b. Mawaya
c. Mapetsi

8. Tchulani magule amakolo


a. Mganda
b. Amapiyano
c. Zeze ndi nyimbo yakusangalala

9. Kodi amasogolera zochitika ku chalichi ndi ndani


a. Abusa ndi wa Msembe
b. Amfumu
c. Aphunzitsi
10. Kodi chidole cha mbuzi tingagwiritse ntchito chipangizo chanji
a. Dongo
b. Madzi
c. chingwe

Gawo B: MAFUNSO OYANKHA NOKHA


50 malikisi

malangizo

Yankhani mafunso awa mumalo omwe adulidwa nzeru kunsi kwa mfunso lina lililonse

11. Tchulani zithu ziwiri zomwe zingalepheretse kupanga zaluso (5 malikisi)


12. Fotokozani zipangizo ziwiri zopangira zidole (5 malikisi)

Werengani nkhani iyi ndipo muyakhe mafunso ali munsiwa:

Tsiku lina Tadala amapita ku sukulu. Panjira adakumana ndi bamboo wina yemwe adanyamula
thumba la Makala logulitsa. Tadala adali ataphunzira ku sukulu kufunika kosamala zithu
zachilengedwe.
Tadala adalingalira zochita kuti mchitidwe wowotcha Makala uthe. Adakumbukira zomwe
akuphunzitsi ake ankanena kuti mitengo ikatha m’dziko, mvula imavuta komanso makhwala
azitsamba amasowa.
13. Tchulani zithu zomwe mungachite pochepetsa mchitidwe odula mitengo (5 malikisi)
14. Kodi mitengo ikatha zimabweretsa mavuto anji (tchulani fundo ziwiri kuchokera mu nkhaniyi) (5
malikisi)
15. Tchulani zithu ziwiri zogwiritsa ntchito pakhomo (5 malikisi)
16. Jambulani chikwangwani cha pa mseu chimodzi (20 malikisi)
17. Kodi owoloka mseu timayenera kuti titani (5 malikisi)

You might also like