Mpingo wa Katolika ya St Pius mu Archdiocese ya Blantyre.
Tikatengera mbiri, nthawi yomwe
Bungwe la CWO linabadwa inali nthawi ya Vatican Council 2. Tikumbukire kuti mpingo wa Katolika unayambitsidwa ndi Yesu Khristu amene anauza Petulo kuti chomwe udzamange padziko lapansi pano chidzamangidwa ndi kumwamba komwe choncho zochitika zonse zomwe zimachitika mimpingo amakwaniritsa zomwe Yesu mwini ana. Nthawi yomwe kumachitika Vatican Council 2 mpingo umatdogoleledwa ndi Papa Yohane 23 amene anatenga udido kuchokera kwa Papa Pio 12. Papa Yohane 23 atafika anawona kuti kamvetsedwe, kachitidwe ndi kayankhulidwe ka anthu ena mumpingo zimasokanizika, zia mwa izo zinali ziphunzitso monga chokuti Papa akayankhula wayankhula basi. Izi anthu ena samazimvetsa bwino choncho samazilandira bwino ndipo amazitenga mwachabe ndipo takula nazo. Mwachitsanzo Bishop akavala chipewa, kunyamula ndodo yake ndikukhala pampando, akayankhula ndiyekuti anthu amati Bishop wati... chimodzimodzi Papa akayankhula kumakhala kuti wamaliza ndipo chotsatira ndikumvera basi. Ndiye Papa Yohane 23 anaganizira kuti akati 'mpingo ndiyekuti sipapa ekha ayi komanso onse; mpingo ndife tonse, ndichifukwa chake mu mauthenga ake Papa Yohane 23 amalimbikitsa kuti aliyense atenge mbali poyendetsa mpingo ndipo gawo la anthu omwe nthawi imeneyo samatekeseka ndi zampingo anali amai, mwina chifukwa chakuti nthawiyo chikhalidwe chimawaonera pansi amai ndipo ngati follow up ya nsonkhano wa Vatican Council 2, Papa anayamba kuitanitsa misonkhano ya magulu a Akhristu eniake yosiyanasiyana yomwe imachitikira kumaiko osiyanasiyana kuphatikizapo ku Africa. Ndipo nsonkhano oyamba unachitikira ku Ghana ndipo wachiwiri unachitikira ku Zambia.
Mu chaka cha 1974, Bambo Allan
Chamgwera (omwe tsopano ndi Bishop opuma wa Zomba) anali bambo mfumu wa Parish ya St Pius ku Soche mu Archdiocese ya Blantyre. Iwowa adatumizidwa kukhakhala bambo mfumu oyamba wa Parish ya St Pius ndi Ambuye Tennison mu chaka cha 1965 koma panthawiyi bambo Chamgwera anali akukhala ku C.I Parish kaamba koti nyumba ya wansembe inali ikumangidwa ndipo chaka chomwecho Papa anasankha Ambuye chiwona kukhala Auxiliary Bishop wa Blantyre ndipo kenaka mu 1968 Ambuye Tennison anapuma udindo ndipo anasiyira Ambuye James Chiona ngati Bishop wa Blantyre.
Nthawi imeneyi, Bambo Allan
Chamgwera ali bambo mfumu wa Parish ya St Pius anayamba kumawerenga mozama mfundo za mu misonkhano ya Vatican Council 1 komanso 2 ndikumaona ndimomwe zinthu zimachitikira ku parish yawo. Ndipo iwo akuzukuta zolembalembazo kunapezeka kuti a episikopi a ku Malawi nawo anaganiza zotulutsa kalata/Pastoral letter yomwe anaitchula kuti Inunso "Pitani kumunda wanga". Mau oti Inunso pitani, akutanthauza kuti pali ena apita kale ndipo ena sanapite ndipo mau awa amatanthauzira kuti "Inunso" (amai) amene mukusalidwa ndipo simukutekeseka ndi zampingo mupite nanunso mukagwire nawo ntchito ya Mulungu. Ndipo kutanthauzira kwa kalata imeneyi ya 'Inunso pitani kumunda kwanga' ndi chiyambi cha bungwe la Amai mu Dayosezi ya Blantyre chifukwa Bambo Chamgwera anaitanitsa nsonkhano wa parish Council kuyambira pa 3 August mpaka pa 5 August 1974 ndicholinga chofuna kufotokozera kalata ya Inunso pitani kumunda wanga ndipo pamapeto pake akhristu anavomereza kuti amvetsa kalatayo. Pa nthawiyi akhristu eniake ku St Pius kuphatikizapo a bulazala omwe anali pa Pastoral experience nthawiyo Brother Benito Masuwa omwe pano ndi wansembe opuma. Potsatira nsonkhano uwu akhristu anafunsana kuti "Titani?"ndipo kuyambira nthawi imeneyo anthu anasankha kugwira ntchito kudzera mu mabungwe ndipo kunabadwa mabungwe osiyanasiyana pa parishiyo monga bungwe la ofalitsa uthenga, olalika, a kwaya komanso bungwe la amai. Pamene limayamba nthawi imeneyi Bungwe la amai linali ndi amai asanu.
Amai awa (Mai Kataika, Chifukwa,
Mai Mbenjere, Mai Mvumbe ndi Mai Ndovi) anai 'tamva zonse zomwe zakambidwa zokhudza kuitanidwa kwathu kuti tigwire ntchito mumpingo ndipo ife ngati amai, gawo lathu likhala kusesa mu chalichi, izi zinali choncho chifukwa kufikira nthawi imeneyi amene amasesa mu chalichi anali mnyamata otumikira kunyumba ya ansembe komanso asisitere basi. Komabe sipokhapo, amai analonjeza kuti kupatula kusesa mu chalichi, adzigwiranso ntchito zina monga kusamalira panja pa chalichi ndi ntchito zina ndipo amai asanu aja anayamba kugwira ntchitoyi.
Izi zikuchitika choncho, Ambuye
Chiona analandira uthenga wansonkhano wa amai omwe umayenera kukachitikira Lusaka m'dziko la Zambia ndipo atamvetsedwa kuti ku St Pius amai akumakumana kugwira ntchito ngati bungwe anapempha bambo mfumu bambo Chamgwera kuti apemphe mai mmodzi kukaimilira anzake ku nsonkhanowu ndipo mai Kataika amene panthawiyo amuna awo amagwira ku Air Malawi anadzipereka kukachita nawo nsonkhanowu pogwiritsa ntchito ndalama zawo. Iwo anapitadi ndipo atabwera uko anakapereka lipoti la ulendo wawo ndi za nsonkhano ku likulu lampingo ku Catholic Secretariat ndipo likulu lampingo litamva mfundo zakunsonkhanowo linayamba kuthandiza bungweli ndipo bungweli linayamba kukula.
Pamenepa, likulu lampingo
linapempha amai a ku St Pius kuti afalitse bungweli ku Dinale ya Blantyre ndipo izi zinapangitsa kuti amai ena a ku parish ya Limbe ayambe nawo. Izi zinapangitsa kuti Mai Bande a ku Limbe Cathedral parish omwe pa nthawiyi amagwira ntchito ku Moni Magazine nawo ayambe kutenga mbali pa kuyendetsa bungweli ndipo nsonkhano wachiwiri wa bungwe la amai omwe unakachitikiranso ku Lusaka ku Zambia anakaimilira ndi Mai Bande. Ichi chinali chiyambi cha kufalika kwa bungwe la amai la Catholic Women Organisation mu Archdiocese ya Blantyre.