You are on page 1of 22

Love is a Verb (KUKONDA PAKUCHITA)

ULALIKI OYAMBA
MUCHIKONDI MULI KUDZIPELEKA 2corinthians 8:9
Kodi munayamba mwamvapo za mfumu ina yomwe inagwa mchikondi ndi kamtsikana kena,
kokhulupilika komwe kamakhala m‟mudzi wina mu mzinda omwe mfumuyi imalamulira
Mfumuyi imadziwika wambiri ndi khalidwe lopanda chifundo kwa anthu ake, iye samafuna kumva
zamunthu ndipo pakapezeka otsutsana naye iye amayesetsa kuti amuchititse manyazi pompopompo
koma ngakhale zinali chomcho mtsikanayi anamupangitsa kuti ayambe kudzichepetsa, khalidwe
la mfumuyi linayamba kusintha chifukwa cha chikondi chomwe anali nacho pa mchikanayi

Tsiku lina mfumuyi inaganiza zomuuza mtsikanayi kuti amamukonda, anamutengera ku nyumba yake
yachifumu, kumuveka zovala zabwino ndi mphete, zibangiri zokongola kwambiri, iye amkaganizira kuti
momwe wangoteromo ndiye kuti mtsikanayu sakananso kuti akhale wachikondi wake. Angandikane
bwanji anadzifunsa? Koma m‟mene amati adzimuuza za kukhosi kwake anadzifusanso, Koma
angandikonde? m‟maganizo ake anazindikira kuti kumutengera ku nyumba ya chifumu, komanso
kumuveka zovala zokongola sizingapangitse kuti iye mkuvomera, ndiye mfumu inaganiza zopita kumudzi
kwa mtiskanayi ndi magalimoto, antchito achifumu kuti zikamukope, ndipo iye adzakopeka ndikukhala
mkazi wa mfumu komabe anadzifusanso, koma adzandikonda?

Mapeto ake mfumuyi inaganiza njira ina, imene anadzipanga kukhala osauka nakhala ngati munthu
wamba ofana ndi mtsikanayi kuti mwina afanane mu chikhalidwe, madyedwe ngakhale m‟mavalidwe,
anavala ngati opempha, kusiya ufumu cholinga choti mtsikanayi akopeke naye osati chifukwa cha chuma
ndi ulemelro womwe ali nawo, koma ndi chikondi chenicheni

Okondedwa achinyamata, nthanoyi ikutionetsera kuya kwa chilingamo, kuti chikondi chimafunika
kudzipeleka, kukonda kweni kweni kumachokera mum‟tima osati chufuka cha chuma ayi

Kukula mu Uzimu
Yesu anasiya ulemelero ndi cholinga chakuti ife tidzakhale ulemelero ndikurandira moyo wosatha
2 akorinto 8:9
Chikondi chakuya cha Yesu chikutitengera ku choonadi m‟magawo awiri

1 MFUMU YATHU INALI YOLEMERA


Forbes magazine mu chaka cha 2022 anthu onse achuma analipo 2,668 kuphatikiza chuma
chawo chinali 12 trillion dollars ( $12,700,000,000 Nanga wolemera kwambiri ndani padziko
lapansi? Ellon Musk mwini wake wa magalimoto aTesla komanso amene anapanga space x
company yomwe anayambilira kupita ku mwezi
Anthu ena omwe ali ndi chuma chambiri padziko lapansi
1 Jeff Bezos mweni wake wa amazon $171 billion
2 Warren Buffet $118 billion
3 Forbes magazine $ 129 billion

Ngakahale kuti anthu onsewa ali ndi chuma chambiri koma sichingafanane ndi chuma choposa chomwe
Ambuye wathu Yesu khristu ali nacho, Yesu ndi mwini zonse ndi wolenga ndipo ulemelero wonse ndi
wake: Akorose 1:16

2 MFUMU YATHU INAKHALA YOSAUKA


Bungwe lina la ku Australia lomwe limawona za mtendere pa dziko lapansi linapanga kafukufuku
ndipo anapeza kuti mwa anthu 100 osaukitsitsa pa dziko lapansi ndi amene;

1 Oyamba anali othawa nkhondo wa ku sudani Mary Myaluak mai wa mwana m‟modzi
amene amakhala ndi ana asanu ku malo osungira anthu othawa kwawo
2 Wachiwiri anali Prem Bahadur Lama wa zaka 45 ochokera ku Nepalese amagwira ntchito
maola khumi tsiku liri lonse kunyamula Dengu la miyara yomwe amakagulitsa $4 amakhala
mu kanyumba udzu ndi mkazi wake ndi ana atatu iyeyu chuma chomwe angaloze
m‟nyumbamo inali watch ya pankono, zovala ndi dengu la miyara

Kungoganizira zomwe anzathu akudutsamo masiku ano, ndi zinthu zomvetsa chisoni, koma taganizirani
Mfumu ya mafumu Yesu anali wosauka kuposa anthu onsewa, Yesu anali osauka motani?
Afillipi 2:5-8

Tiwasamalire osowa, amasiye, okalamba, am‟ndende monga ife tikafunira kuthandizidwa titakumana
ndi mavuto onga amene anzathu akukumana nawo
Yesu anasiya ulemelero, kudzakhala kapolo nadzichepetsa yekha nakhala onga ife, anali odzichepetsa
anaopa lamulo la Mulungu anasinthanitsa ulemelero ndi imfa, natifera ife pa mtanda.

Mathero
Chikondi chakuya ndicho chinamupangitsa Yesu kufa pa mtanda
Yesu ndi bwenzi lathu
Anafa kuti inu ndi ine tipeze ndendere ndi moyo wosatha
Chifukwa chakuti anakhala osauka kuti tipeze moyo wosatha lero amene tamulandira iye ndife wolemera
chifukwa tili nawo moyo wosatha

Kodi ife tikuti bwanji poganizira chikondi chakuya chotere?\


Yankho labwino ndikungodzipeleka m‟manja wa Yesu kuti alamulire miyoyo yathu nthawi zonse
Tikumbulire kuti chikondi chenicheni chimafunika kudzipeleka mwathunthu , chifukwa cha zomwe Yesu
wapanga m‟mowo wathu ife tikungoyenera kulapa machimo athu ndikudzipeleka m‟manja mwake
Chikondi chake mchakuya, chomka muyaya

AMEN
Love is a Verb (KUKONDA PAKUCHITA)

ULALIKI WACHIWIRI
Mukukonda muli kuyamika Luka 7:36-50
Tangoganizirani kuti madzidzidzi mwagwera m‟nyanja, koma inuyo simudziwa kusambira ndipo
mwayamba kumira, koma wina wakuonani mukuvutika ndi madzi ndipo wakuponyerani, choti
mugwire kuti muyandame, musamire chopulumukirapochi chaponyedwa kutsogolo kwanu
musanayambe kumwa madzi mwachigwira ndipo mwayandama, osamiranso anthu opulumutsa afika
kukupulumutsani kumka kumtunda, mwasanza ena amadzi pang‟ono omwe munamwa, anthu
akuunjikirani, kukondwera kuti mwapulumuka, pamene tsopano moyo wabwelera mukulankhula mau;
munaona m‟mene ndinawakhira choyandamitsa chija ife simasewera!
Munaona m‟mene ndinachimamatira muja
Munaona kuti thupi langa linagomamatira ndendende chopulumukirapo choyandama chija, ife ndi amuna

Iyi ndi nkhani yomwe ili mu bukhu la (John Z‟s Grace addition) mocking bird 2012
Limene linalembedwa kutengera zolembera za Rod Rosenbladt

Nzochititsa mantha ndi zomvetsa chisoni kuti ambiri a ife lero tikapulumuka pa ngozi kapena pa vuto
lina, timaona ngati ndi mzeru zathu zapangitsa kuti tipulumuke, ena timaona kuti ndi mzeru za anzathu
zapangitsa kuti tipulumuke, komanso mwina tapulumuka chifukwa tinamvera zomwe otithandiza
amanena kuti tazitsatira bwino lomwe mchifukwa chake mwina tapulumuka,
sitimaganiza kuti alipo wina woposa amene watipulumutsa koma ife timakweza anthu, kukhala opambana
pachipulumutso chathu kuiwala Mulungu monga wopulumutsa koposa
Tingathe kuwathokoza, mwinanso kuwaitanira ku nyumba kwathu ndikudya nawo limodzi, koma kuiwala
kuthokoza Mulungu ndi pemphero ngakhalenso ndi zothokoza
Kuyamika ndi chinthu chimodzi chimaonetsera uyamika ndipo chimayenera kupezeka mwa ana a
Mulungu, chimenechi ndi chimene chingatisiyanitse ndi dziko lapansi
(William Mc adavid ethan Richardson, Paul Zahl.Law & Gospel Mockingbird Ministries, 2015, 73)

Kukula
Luke 7:36-50
Kuthokoza Mulungu chifukwa cha moyo, mabanja, ndimadalitso ambiri omwe watipatsa komanso,
kukhala okhulupilika ndi kuyamika makhalidwe ena a ana a Mulungu
Mfundo zoti tione
Simon anali m‟pharisi
Simon anakonzera Yesu phwando
Simon anali Mpharisi otsatira malamulo a chiyuda ndipo a Pharisi nthawi zambiri amadzitenga monga
anthu oyera koposa anthu ena onse
Pambali posunga malamulo a Mulungu, a Pharisi anadzipangiranso malamulo ena owonjezera
mwachitsanzo lamululo la Eksodo 20:8-11 lokhudza sabata iwo analipangira malamulo ena owonjezera
Simon anali wolemekezeka ndi omveka. Koma ndichifukwa chani anamuitanira Yesu kunyumba
kwake?
Simon anakonza phwando osati pachifukwa chothokoza kuti wachiritsidwa ku khate lake, kuyamika
Mulungu pa zomwe wachita pa banja lake, koma kuti adzionetsere kuti iye ndi wachuma, Mateyu 26:6
komanso kuti zimangoyenera kutiro ndipo amaona ngati phwando lake lingalipire zomwe Yesu
anamuchitira, kusayamika ndi kusavomereza kwa Simon

Mosiyana ndi Simon mai wina yemwe sanaitanidwe ku phwando, koma yemwe amadziwa zomwe Yesu
wachita pa moyo wake anaganiza zopita ndi mphatso kwa Yesu
Mai ameneyu anali ndani?
Anyamata ndi asungwana pamakhala zokamba zambiri zokhudzana ndi nkhani imeneyi ngakhale zili
chomcho chachidziwikire ndi chakuti maiyu anali wochimwa
Ena amaganiza kuti anali Maria wa Magadala mlongo wake wa Lazaro ndi Malita yemwe anaphwanyira
mafuta onunkhila pa mapazi a Yesu nalira, napukuta misonzi yake kupuputa ndi tsitsi lake yemwe
anapsyopsyona mapazi aYesu Luka 7:38

Luka 7:39
Luka 7:40-43
Maria anali atapelekedwa kwa Yesu monga ochimwa ndipo amayenera kugendedwa kuti afe Yesu anali
atangomukhululukira kumene;

1 Yesu anamuona maria monga mwana wake


2 Yesu anamuona Maria monga mwana yemwe amasoweka chikondi
3 Yesu anamuona Maria monga mwana yemwe amasowa kulandiridwa ndi kukhululukidwa
4 Monga wina aliyense wa ife tinali otayika koma Yesu anatilandira monga ana ake tinakali
chichimwire iye anatifera

Achinyamata chikondi chidzitipangitsa kukhala oyamika pa zomwe Mulungu wachita pa moyo wathu
Moyo wathu mwina wakhala otayika, chifukwa chotsatira zomwe anzathu amachita kumwa
mowa,zibwenzi kusakonda kupita ku kachisi la sabata ndi zina, koma Yesu akutiitanabe kuti bwera
mwanga wanga ndinakufera
Maria anasiya moyo wake otayika ife lero Yesu akutiitana kuti tibwelere kwa Iye, amatikonda ndipo
akudikira kuti ife tibwerere kwa Iye ndipo adzatikhululukira, ndikukhalanso ana ake
Masalmo 103:1-5
Tidzakhutitsidwa ndikukhala ndi moyo wa muyaya tikabwera monga m‟mene tilili kwa Yesu ndipo Iye
adzakhala Tate wathu ndikutipulumutsa

AMEN
To Love is to forgive
(KUKONDA NDIKUKHULULUKA) Yohane 21:15-17

ULALIKI WACHITATU
Bill Buckner anali munthu woyamba wosewera mpira yemwe anasewera mipikisano ikulu ikulu kwa
zaka 22 ndipo anamwalila mu chaka cha 2019 alindi zaka 69.

Udali mpikisano wa chaka cha 1986, umene red sox umkatsogola 3-2 mu mpikisano ndipo umkatsogola
5-2 kwa timu ya new york mets mu mphindi ten zosatsala; padali patangotsala mphindi zitatu kuti awine
masewelowa. Koma mphindi teni zitafika pakati osewela mookie Wilson wa timu ya mets, adaponya
mpira kwa buckner omwe adauphonya numudusa pakati pa miyendo yake ndipo udatuluka

A team ya mets anachinya chigoli kuti apambane mpikisano umenewu ndipo anapambana. Kulakwisa
komwe anapanga buckner zinampangitsa kukhala chimodzi cholakwika chachikulu mu mbiri
yazamasewerowa. Atasiya kusewela maselowa, anachokako ku dela la Boston kupita ku Idaho malingana
ndi mkwiyo wa anthu omuzungila omwe amaonesara.

Chidani cha anthu aku boston ndi bucker chidapitilira kwa zaka zochuluka. Koma zinthu zidayamba
kusitha mmene osewera a timu ya redsox anawina mpikisano wa dziko lapansi mu chaka cha 2004 ndi
2007. Mphanvu yokhululuka idaonekera mu chaka cha 2008, pamene bucker anabwelela mu nzindawu
wa fenway park kukaponya mpira oyamba kutsegulira masewelowa; kumeneku adalandira ulemu, anthu
atayima kwa mphindi ziwiri ndipo adalira.( kelvin mercer. Osewela wakale wa MLB bill buckner
anamwalira, “atamulandi Yesu monga Mbuye ndi mpulumutsi wa moyo wake‟‟‟ (malemba azamasewero
28-55-19).

KUKULA MU UZIMU
Monga m‟mene bill buckner anachitira, ophunzira wa Yesu, Petro nayenso monga m‟modzi
Amaene anachitiridwa zozizwa , ndi Yesu
Kupha nsomba zambiri atakahala usiku onse opanda nsomba. Kwa zaka zitatu ndi theka, Petro anali
ophunzira wa Yesu ndipo adachitira umboni za zozizwa anachita Ambuye. Ndipo anali munthu m‟modzi
yemwe anachita zozizwa zina atatumidwa ndi Yesu. Zinanenedwa, tsiku lina usiku, atapita kowedza
nsomba osapezako, Ambuye anafika panyanja panaili iwo nanena “kankhira bwato lako kwa kuya, ndipo
ponya makoka ako kuti ugwile nsomba.” (Luka 5:4.) ndipo nkhaniyi idapitilira, anachita motero
ndikugwira nsomba zambiri pofikana ma koka adayamba kungambika.” Powona zozizwazi Petro,
adagwada pamaso pa Yesu nanena, “ambuye, musabwele chifupi ndi ine! Ndine munthu ochimwa.”‟

Ndipo pachochitika china, Petro adala pa Nyanja ya galileya ndi ophunzila onse pamene mafunde
anaomba omwe anafuna kuononga bwato lawo, koma pakati pa mafunde Yesu anawafikila, ophunzila ali
ndi matha, Yesu anayenda pa Nyanjakulondora ophunzira. Pamene ophunzila anawona munthu
akuyenda panyanja pomwe panali mafunde anali ndi mantha and anaganiza kuti ndi mzukwa ndipo
analira mowopa. Koma yesu anawalimbikitsa nanena mawu, “musadandaule! Ndine Yesu. Musaope. Iyi
ndi nthawi yomwe Petro anati, “Ambuye, ngatidi muli inu, ndiuzeni ndibwele kwainu pamadzi.” Yesu
anayakha kuti abwere ndipo Petro anayenda pa nyanja yamafunde ya galileya.

Mateyu analembanso chochitika china cha Petro ndi Yesu:

Ndipo Yesu anafusa, koma munena kuti ndine yani?

Simon Petro nayakha, ndinu Mesiya, mwana wa Mulungu wamoyo

Yesu namuuza: Simoni mwana wa Yona, ndiwe odalitsidwa! Sudazindikile izi mwaiwe wekha.
Akuonesela izi ndi Ambuye anga wakumwamba. Ndipo ndikutcha Petro, kutathauza “thanthwe.”
Ndipo pa nthatwe Ili ndizamanga mpingo ndipo imfa sizakhala ndi mphanvu pa ichi. (Mateyu
16:15-18)

Titha tonse kuvomeleza kuti Petro anali munthu ofunikila pa ophunzila a Yesu, koma pa nthawi yopanga
chisankho, iye adalakwa chithu chachikulu. asadapachikidwe pa mtanda, Yesu adayakhula ophunzila ake
nati, “ pofika usiku wa lero lomwe, nonse muzandikana…” ndipo pa mawu awa onse adayang‟anana.
Ndipo Petro adati,” angakhale ena akukaneni, ine sindizakukanani!” Mateyu 26:31,31

Petulo adakakamila mobwelenza kuti sadzamakana ambuye ake! Komabe, patapita mawola,
sadangomukana kokha, koma anatembelela ndikulumbila kuti samamudziwa yesu. Mateyu 26:70-74)

Inde, Petro adamukana Phunzitsi wake. Adamukana pamene amayenela kumuteteza. Adamukana ndithu
yemwe adamuyitana ndikupanga zozizwa zambiri mmoyo mwake. Pakuchita kulakwikaku, Petro
anadzimvera chisoni kuti zomwe Ambuye ananena zachitika, anachititsidwa manyazi. Ndipo mukuganiza
chidachitika chotsatila ndi chani?

Mmene chilli chodziwika, Ambuye wathu anapachikidwa. Nthupi lake lidalowa mmanda, ndipo pa tsiku
lachitatu adawuka. Ndipo atawuka anaKumana ndi Petro kachikena, pamalo omwewo a zaka za mbuyo
adachitila umboni pa chozizwa adachita Yesu. Tiyeni tiwelenge momwe adachezera ambuye ndi Petro

Ngati mukufuna kudziwa, welengani bukhu la Yohane21:


Mmene Yesu ndi ophunzila ake adamaliza kudya, adawafunsa, “ simoni mwana wa Yona, kodi
umandikonda kuposa andikondela enawa?”
Simoni Petro nayakha, “inde, ambuye, mudziwa ndimakukondani!”

“Dyetsa ana akhosa zanga”,

Yesu nafunsanso kachiwiri, “simon mwana wa Yona, kodi umandikonda ?

Simoni Petro nayakha, “inde, ambuye, ndimakukondani!”

Weta mkhosa zanga,”


Yesu nafunsanso kachitatu, “simon mwana wa Yona, kodi umandikonda ?
Petro adanva kuwawa chifukwa Yesu adamufunsa katatu ngati iye amamukonda, ndipo anayakha kwa
Yesu, “Ambuye, mudziwa chilichonse. Mudziwa ndikukondani.”

Yesu nayakha, “dyetsa nkhosa zanga. (Yohane 21:15-17)

MATHELO
PetRO, ngati bill buckner, adachita kulakwika kwakukulu komwe kudalemedwa mu mbiri, koma
adalandila chisomo chokhululukidwa. Achinyamata , nkhani ya Petro ikutiphunzisa za chikondi
ndikukhululuka. Mutha kuona kuti Yesu anamukhululukila Petro posaona kulakwa ndikulephera kwake.
Ndipo adamukhululukila chifukwa amamukonda. Nanu mkutheka mwalakwa chachikulu, koma mmene
Yesu anamukhululukila Petro, akulitsa kukhululuka kwake kwa inu.
Mbali ina, nkhaniyi ikutiphunzisa ife kukhululuka, mmene Yesu anachitira. Mulungu anampasa Petro
mwayi wachiwiri posaona kulakwa kwake. Chomwechonso, inu ndi ine tikhale ololera kukhululuka. Lero
ndikukuyitanilani kulandila chikhululuko, komanso kuchipeleka, osayiwala kuti chikondi
ndikukhululuka,

KUZIYANGANILA NDI MAFUNSO

1. Kodi bill buckner angafanane bwanji ndi nkhani ya Petro?


2. Tikuphunzirapo chani pa nkhani ziwirizi?
3. Tafotokozani mu mau anu chifukwa chani chikondi ndikukhululuka?

AMEN
To Love is to Trust (KUKONDA NDIKUKHULUPILIRA)
ULALIKI WACHINAYI

Kodi munamvapo za nkhani ina ya munthu amene anawoloka miagara falls poyenda pakachingwe?
Atawagomesa anthu ndi chibwana chake choyenda pakachigwe, anawafunsa, ndiangati amene
mukuganiza angawoloke pakachingwe kameneka potsatira zomwe munthuyi wachita kodi ulendo uno
atatenga wilibala munthu atakhalamo?
Anthu anawomba mmanja, wina aliyense anali ndichikhulupiliro choti atha kukwanisa, oyenda
pakachingwe uja anawonjezela, ndi ndani mwainu akufuna kukhala okwela nane wilibala?‟‟
Padakhala chete. Chigulu cha anthu chidasiyana maganizo pakati pakukhulupilira ndi chikhulupiliro!
Chidali chithu chimodzi choti akhulupilire kuti wilibala ithadi kuwoloka pachingwecho, koma kuika
munthu mu wilibala ndikudusa naye pakachingwe zidali zithu zovuta ndikovuta kuzikhulupilira.

KUKULA MU UZIMU
Tikukumana ndichomwe chikutchedwa “ mazunzo opanda kuzikhulupilira padziko”. Molingana ndi
zolemba la bukhu la Washington post mu chaka cha 2015. Osakhulupilira munthu, ndi chithu chofunika
kwambiri. Kafukufuku anapanga a sukulu yaza ndale ku Harvard university, imanena kuti mwa anthu a
zaka 18 mpaka 29 palibe kusoweka kokhulupilana ku boma, mabwalo akulu a Milandu ndi kowulutsila
nkhani. Ndipo adapiliza kunena kuti mmadera mwathu chikhulupiliro mmalo otumikila dziko, chachepa
kapena chalowelatu pasi.” Ndichifukwa chiyani chakutaya chikhulupilirochi? Pali kumvetsedwa kuti
chitetezo cha anthu chidatha.” Olemba bukhuli akukhulupilira kuti “ chipongwe chapa sept. 11,2001,
chidationesela ndi mphanvu ndi mowopseza kuti anthu omwe anakhulupilidwa kuteteza anthu sangathe
kutelo.” Chikhulupiliro choti ndiotetezedwa isanachitike ngoziyi chidasowa.

Mau a Mulungu amakamba za chikulupiliro mwa Mulungu. Ndizithu zopatsa chidwi kudziwa kuti pali
mawu atatu amene amafotokoza ubwenzi odalilana omwe ulipo pakati pa akhristu ndi Mulungu:
zikhulupiliro ndi chikhulupiliro. Koma ndi mau achikhulupiliro omwe amafotokoza bwino za mau
amulungu, odalira kwa Mulungu. Mwachisanzo, pamene mawu okhulupilira amaoneka mmalemba, atha
kuloweredwa mmalo ndi mawu oti chikhulupilo. Mau aMulungu akuti, “khulupilirani mwa Ambuye Yesu
khristu ndipo muzapulumutsidwa.” Machitidwe 16 :31, NKJV) komanso vesili litha kuwelengedwanso
motere, “ndichikhulupiliro mwa Ambuye Yesu khristu ndipo muzapulumutsidwa”.

Kukhulupilira ndi chani ndipo nkofunika motani? Pa Merriam-webster.com akutathauzila mau oti
chikhulupiliro ngati:” munthu or chithu chodalilika .” bukhu la Mulungu pa Ahebri 11: likuti,: koma
opanda Chikhulupiliro sukangatheke kumungasangalatsa Mulungu. tikuyenera ku khulupilira Mulungu
kuti ndiowona ndipo amapeleka mphoto kwa onse omusaka Iye.

Pano mutha kusikhasikha: zimatathauzanji ku khulupilira mulungu? Zimangotathauza kuti kukhala


ndichiyembekezo chathu kuti ndiye Yemwe anati Ndiye, komanso amachita chomwe wanena.
Mu bukhu la Mulungu timapeza nkhani za anthu omwe anapeleka chikhulupilo chawo chonse kwa
Mulungu. Nkhani imodzi ina inalembedwa pa Mateyu 8:5-13.ndipo vesili limanena kuti wamkulu wa
nkhondo wachiroma anapita kwa Yesu, nayamba kupepha: Mulungu, wantchito wanga alikunyumba mu
ululu ndipo sangathe kuyenda.” (Versi 6)
Powona ndikukhuzika muMtima wa munthu wakhondoti, Yesu anayakha: ndipita ndikukamuchilisa.”
Apa ndipomwe nsilikaliyu anaonesa kukhulupilira kwakukulu komwe sikudaonekepo. “Mulungu ,
sindine olungama kwatuthu kuti mukathe kufika kunyumba kwanga. Ingonenani mau, ndipo wantchito
wanga achila.” (Verse 8). Atamva izi, Yesu anazizwa nanena, “ ndinena ndi inu nonse a Israyeli
sindidapeze munthu wachikhulupiliro chotere! (verse 10)

Nsilikali wachiroma adakhulupirila mawu amphanvu a Yesu ndipo posaona adakhulupilira mawu a
mphunzisi adali amphanvu kukachita zoziswa. Chinanso chofanana chidachitikanso ndi msilikali
adathamangisa ndikugwira bulu wa alexander waulemelero. Mmene adabweletsa chinyamachi kwa
wamkulu wawo, alexander adamuthokoza ponena , “zikomo.”
Ndimau amodzi nsilikaliyu adakwezedwa udindo, mmene wamkuluyu adayakhula, ndipo nsilikaliyu
adakhulupilira: adazionesela yekha kwa mkulu wa nkhondo, nasakha chovala cha nkhondo chatsopano
navala; adapita kwa ogona akulu akhondo nasakha malo ake ogona; adapita ku malo odyera nakadya
nawo.

Adakhulupilira chifukwa cha wamkulu wawo wankhomo adanena. Okondedwa anyamata, ndidakakonda
tidakakhala ndi kuzidalira komwe akhondowa anali nako ndikukhulupilira mau a Mulungu kuti alindi
mphanvu yaikulu. Ichi ndichifukwa chomwe chiliri chofunika mmene Mulungu akuti tidzuke, tichite
motelo; akanena watikhululukila, tizimasule pakulakwa kwathu. Akatiuza chomwe tili, tikhulupilire,
akanena tapulumutsidwa, tichose mantha athu. Ndipo akanena wapeleka kwa ife, tisiye kudandaula. (max
lucado. He still removes stones, editorial Caribe, Nashville, tn;1994,p.117)

MATHELO
Komabe, sitingathe kukhulupilira Mulungu mwatuthu ngati sitimukonda. Pamene tikonda Mulungu
tikuyenela kumukhulupilanso. Kupita kukhala m‟manja a Mulungu nkofunika kwambiri, Mawu a
Yohane akuti, “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu
Khrustu amene munamumtuma.” (Yohane 17:3)

Kukhulupilira ndi zotsatira za chikondi ndipo chikondi chikula mwa ubwenzi ndi Mulungu. ngati ukufuna
chikhulupiliro chikule mwa Mulungu, ukuyenela kukhazikitsa ubwenzi ndi Mulungu. ukuyenela
kuyakhula naye mu pemphero ndiku mvetsela tsiku liri lonse mawu ake powelenga mau ake; ichi ndi
chokhacho ungakulitse chikondi chaku pa Mulungu ndipo potelo muzabwela ndikukhulupilira umulungu
wake ndi mawu ake.

KUYANG’ANILA, MAFUNSO

1. Kodi chikhulupiro ndi chani komanso ndichofunika bwanji?


2. Ndichifukwa chani kupanda kusakhulupilira sikumukondweletsa Mulungu?
3. Chimatathauza chani kukhulupira Mulungu ndipo mumamanga bwanji ubwenzi olimba
wachikhulupiliro ndi Ambuye?

AMEN
To Love is to Obey (KUKONDA NDIKUNVELA)

ULALIKI WACHISANU
Kodi mukuziwa kuti panali nthawi yomwe dziko la America lidalibe malamulo oteteza ana mmipando ndi
kuika zozitetezela mma galimoto? Zomvesa chisoni, ana ochuluka omwe sanakhale mmipando kapena
kuyika lamba wozitetezela okakhala mgalimoto anamwalira pa ngozi zagalimoto. Lero, malamulo
akuletsa ana kuyenda mu galimoto iliyonse osamanga lamba molondola komanso oyikidwa bwino.
Komanso azimayi akuyenela kuyika mmpando wa mwana akamachoka kuchipatala, kupita ku nyumba.
Pa zonse zowonesa chikondi cha munthu, palibe chikondi choyera komanso chokongola kuposa chikondi
cha bambo ndi mwana wake. Komabe, chitetezo chamwana chilli pachiopsezo, chimaonesa kuti chikondi
chokha sichokwanila. makolo sithawi zonse angakwanise kuchita chilichose kwa ana awo choncho
pakuyenela kukhala lamulo kapena mulingo powonesesa chikondi chawo chisachepere pachikondi
chowona.
Mulungu amaziwa chomwecho ndichikondi chowona komanso kuzipeleka kwa iye ndi anthu ena.
Amadziwa kuti siokwanila, tikuyenera malamulo komanso malire, munjila ya malamulo nkhumi omwe
amatithandiza kukonda mwathunthu Mulungu ndi anthu.

KUKULA MU UZIMU
Chikondi chizakhala choyanjanisidwa ndikumvela, ndipo pamene zilizoona kuti kumvela kutha kukhala
opanda chikondi, sipangakhale chikondi opanda kumvela. Bukhu la marko likukamba zankhani ina
yomwe inafotokoza za chilungamo cheni cheni.
Panali nyamata wolemela kwambiri ndipo anadza kwa Yesu, mozichepesa adagwa pamapazi a Yesu
ndikufunsa, “ mphunzitsi, ndingatani kuti ndipeze moyo wosatha?” ili ndifunso lofunika pa moyo
wamunthu ndipo pachifukwa ichi, tiima ka mphindi kuonetsela kuchepa koma chilungamo chofunika.
Nyamatayu adamufikila Yesu pamene amafuna kudziwa za chipulumutso chosatha; malingana
ndichikhulupiliro chawo, chipulumutso chidali chotsatila cha kugwira ntchito ndikulimbikila. Kwa iyeyu,
moyo osatha adali malipilo ochoka kwa Mulungu chifukwa chakumvela. Zosakhalabwino, Anyamata
ambiri adapitiliza kukhulupilira bodzali! (Malaki 10:17-22)
Kodi tidapulumutsidwilanji? Mau aMulungu akutiphunzitsa moyo wosatha sukwanilisidwa ndi maganizo
athu ; koma timapasidwa ngati mphanso. Paulo akutiuza pa Aefeso 2:8,9 Pakuti muli opulumutsidwa ndi
chisomo chakuchita mwa chikhulupiliro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chiri mphatso ya Mulungu.”

Abale anzanga, chipulumutso chimatengela zimene Mulungu wachita kwa ife, osati chomwe tachita kwa
iye; nyamata olemelayu amafuna kusitha mmene amayang‟anila chipulumutso. Ngati tikufuna moyo
wosatha, tikuyenela kuphunziraso ndi Yesu Iye ndi mphunzitsi widabwitsa!
Ku tsogolera anthu olemera, munjira yachowonadi, Yesu anayakha funso lake, nanena, “ukudziwa
malamulo. „usaphe. Khala okhulupilika mu banja. Usabe. Usakambe mabodza za ena. Usaname.
Lemekeza atate ako ndi amako.”

Pamene nyamata wolemelayu atanva yakho lafunsoli anadupha ndi chimwemwe chosefuka nanena,
“mphunzitsi, zonsezo ndakhala ndikusunga pa unyamata wanga.‟‟ Koma zitatelo, “ Yesu,
anamuyang‟ana, namukonda nanena naye, “ukusoweka chithu chimodzi: pita, kagulise zonse ulinazo ndi
kupeleke kwa osauka, ndipo uzakhala chuma kumwamba; ndipo bwera, nunditsate.”

Mutha kumasikhasikha: chachitika ndichani? Zikutheka bwanji nyamatayi yemwe adamvela malamulo
adapelewela zina? Chimasoweka ndi chani? Amasoweka chithu chofunika kwambiri!

Pa nkhaniyi nyamata olemelayu, ellen white adalemba….


Nkhristu adadziwa mtima wa nyamatayu. Koma chithu chimodzi chimasoweka, ndipo chidali chofunika
kwambiri. Ndimafunika chikondi chamulungu mu mtima mwanga. Pa chithu ichi chokha, ngati
sichipelekedwa, chidakatayitsa moyo wake; zidakalowetsa chinyengo ku umoyo wake. Posekelela ichi,
kukula mtima kudakakula. Koma kuti alandilechikondi chamulungu, amayenela kuonetsanso chikondi
chachikulu kwa iye mwini ndi anzake omwe. (E.G de white. The desire of Ages, p.478)

Chomwe nyamatayu adasoweka chidali chikondi chamulungu! Adasoweka kumvetsetsa kuti kumvela
sikumasayanisidwa ndi chikondi! Ndimakhala ndikumva achinyamata ambiri akunena, “ ndine munthu
wabwino ndipo ndichithu chofunika kwambiri.” Koma ndizoona? Taganizani mzimayi, wamasiye wa
mwana mmodzi yekha. Mmayiyu akuphunzitsa mwana momwe akuyenela kukhalila moyo wake: kunena
zoona nthawi zonse, kulimbikila ndikuthandiza anthu osauka. Amapeza ndalama yochepa, koma
pazomwezo amasunga nkukwanitsa kumutumiza ku sukulu. Taganizani atamaliza sukulu, osafuna
kulankhula mai ake mwina ntahwi zina mwapatalipatali; mwa kanthawi aziwatumizila kadi ya
khrisimisi, koma osawayankha ndi telephone kapena kalata. Koma amalonjeza kuti dzakhala momwe
adamuphunzitsira mai ake kukhala: wonena zoona, wolimbikila ndi opeleka.

Kodi mutha kunena kuti izi zidali zololedwa? Ayi ndithu. Anzanga, sizokwanila kutsata kokha malamulo,
ndikofunika kukhala ndiubwenzi okonda ndi Mulungu, kusamalira makolo, amasiye, odwara ndi ena

MATHELO
Chinachitika ndi chani kwa nyamata wathu mu nkhaniyi? Ndingakondwe kuti m‟nyamata uyu
adamutsatila Yesu! Komabe, nkhaniyi yatha ponena kuti: anakhudzika ndimauwa, adachoka
okhumudwa, chifukwa adali ndi ziwanda zambiri.

Okondedwa abale ndi alongo, patha kukhala kumvela opanda chikondi- potengesa pankhani ya nyamata
olemelayi- koma sipangakhale chikondi opanda kumvela. Kukonda ndikumvela. Pamene Yesu
anafusidwa za lamulo lofunika kwambiri pamalamulo khumi, mosindika adati, “kunda Ambuye Mulungu
wako ndi mtima wako onse, mzeru zako zonse ndi moyo wako wonse.38 ili ndilo lochoyamba
ndilofunika pa malamulo a Mulungu.” (Mateyu 22:37-38)
Anzanga, chikondi chikhale choyambilira pakumvera, poti malemba akuti, “chikondi ndikukwanilitsa
chilamulo.”
KUYANG’ANILA NDI MAFUNSO

1. Kodi chifukwa chani kunanenedwa kuti sipangakhale kumvela opanda chikondi, koma
sipangakhale chikondi opanda kumvela?

2. Kodi malemba akutiuza chifukwa chani tidapulumutsidwa nanga nyamata amayenera kuchita
chani uti apulumutsidwe?

3. Kodi ndi lamulo liti liri lofunika kwambiri pa malamulo khumi komanso chifukwa chani?

AMEN
To Love is to worship (KUKONDA

NDIKUPEMBEDZA)

ULALIKI WACHISANU NDI CHIMODZI


(YOHANE 4:23)
Pa malonda ena apakanema, adawonetsa nyamata wina alimkati mosikhasikha kuti apilire kapena ayi
kupanga ukwati omwe achita kumukonzela. Mu dziko lake, ukwati opangilidwa chinali
chikhalidwe,komabe atakhalako ku America, adali asanachilandire kuchikhalidwechi, potengela adali
asanakumane ndi mkazi yemwe amafuna.
Zitatelo, atafika mzimayiyu ku bwalo la ndege, nyamatayu anadikilira momvera makolo ake, Maluwa ali
mmanja mwake ndi nkhope yosangalala, koma atamuona akulowa chilichonse chidasitha. Zidapezeka
adali mkazi wokongola; mosakhalitsa khope yake yosangalala idasitha. Maganizo okwatila mkaziyu
sichinalinso chithu chopasa matha koma chosangalatsa.

Chinasitha ndichani? Anali atamuona.


Okondedwa anzanga, timatha kutumikila mulungu chifukwa tachita kuuzidwa. Timakwawa mukachisi,
kuzikakamiza kutumikila, koma mitima yathu sili choncho. Tili ngati nyamatayu ku bwalo la ndege,
mokayika tagwira maluwo a Mulungu. timayesera kuyima muchiyelo chifukwa tikudziwa tikuyenera
kutelo, koma zimatilemera, sitimachita ndichimwemwe.
Izi zingasithe bwanji? Tione Mulungu.
Tikakhala ndimasomphenya omwe Mulungu ali, timakhala ndi mphamvu yokwanilitsa ntchito yake.
Tikayang‟ana za ukulu wake ndi kuyela kwake, kupembedza kumasiya kukhala kokakamiza.
Tikanvetsetsa za ukulu wachikondi chake, kutumikira ndikupembedza sikukhala ntchito koma
chimwemwe!

KUKULA MU UZIMU
Poyakhula zachikondi ngati ntchito, tisayang‟anile pansi nkhani yakupembedza, kukonda Mulungu ndi
kumupembedza zimayendera limodzi. Pano, patha kukhala ngati zingabweletse kukangana ndi
kusagwirizana kwamaganizo kuposa nkhani yakupembeza chifukwa, nthawi zambiri nkhani ya
kupembedza ikamakambidwa, anthu amapita ku nkhani ya nyimbo. Mu ulaliki wa Lero ndikuuzeni kuti
sitikambilana za nkhani yosathayi yozungulira kupembedza, koma tiyang‟ana mau amubukhu lopatulika
amane akuonetsa zotsatila za anthu okhulupilira opembedza muchoonadi.
Tiyika chidwi kwambiri pa mau abwino amu bukhu la Mateyu.

Tiyambe ndikuwelenga Mateyu 2:11-12: “ pamene amuna analowa mu nyumba nawona mwana ndi
maria, mai wake, anagwadwa pansi namupembedza iye. Adatulutsa mphatso zawo za golide,nawapatsa
iwo. Chotelo adawachenjeza m‟maloto nati asabwelere kwa Herodi, Ndipo iwo anadutsa njira ina
pobwelera kwawo.

Mafumu akummawa, amene anali owona za m‟mwamba ndi ophunzila achinenero, adabwera kuchokera
mdera lakutali ndicholinga chokapembedza mfumu yomwe yabadwa. Kodi Mungathe kulingalira nthawi
yomwe inadutsa paulendo wawo wokaona Yesu nakamulambira? Adali ololera kudutsa mu misewu
yovuta, ndikusintha kwa nyengo pokangopembeza Mulungu. ndipo m‟mene adamupeza, anagwa pamaso
pake napeleka mphatso zapamwamba. Chidawachitikila ndichani kenako? Nkhani imati atatha
kupembeza Mulungu” adachenjezedwa kuti asabwelere kwa Herodi ndipo anabwelera kwawo podutsa
njira ina.
Anzanga, posafuna kuonjezera zina mu bukhu lopatulika, titha kunena kuti wopembedza muchoona
adzabwelera kwawo pa njira ina. Mu mau ena, kusintha kwa njira ndi cholinga, kumachitika mu moyo
wathu wauzimu.

Mawu achiwiri a Mulungu okamba za zotsatira zopembeza moona akuoneka pa Mateyu 14:32-33.
Pamene Yesu ndi Petro anakwera mu bwato, namodwe anasiya. Anthu amene anali mu bwato
anamupembeza nati, “ ndinudi mwana wa Mulungu!” nkhaniyi imati, namondwe adafuna ku miza bwato
la ophunzila. mkati mwakuomba Mphepo Yesu anabwera akuyenda pamadzi, atamuona, ophunzirawa
adalira mokweza poganiza adali mzukwa, koma Yesu adayakhula nawo, nati, “ khalani olimba; ndine,
musaope.” (Mateyu 14:27) apa ndipamene Yesu anakwera mungarawa, ndipo moziziswa anamodwe
adasiya ndipo pa Nyanja padachita bata. Poyang‟ana mphanvu ya Mulungu, ophunzira, anagwa pamapazi
pake namupembeza, popeza adaona mphanvu ya Mulungu itagonjetsa namondwe. Anakumana ndi
mtendere opyola kumvetsetsa konse, kotero adapembeza Mulungu posiya zonse. Popeza adali pamapadzi
ndi wamkulu wawo padalibe chifukwa chowopa, kusatetezeka kudachoka.

Inde, okondedwa anzanga, tikachitira umboni za mphanvu ya Mulungu ndikumupembedza Iye, mantha
ndi kusowa kwa chitetezo m‟moyo mwathu kumachoka. Mtendere omwe umadzadza
ndikumvetsetsa,umadzadza mmitima mwathu ndi kuzidalira. Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza
ndani? (Aroma 8:31)

Verse lomaliza ndikufuna kugawana nanu likuchoka pa bukhu la Mateyu, mwadzidzizi yesu anakumana
nawo nawapasa moni. Ndipo anapita chifupi naye, nagwila mapazi ake namulambila iye. Mateyu 28:9

Tsiku lachisanu zisadachitike izi, Yesu atapachikidwa ndipo chikhulupiliro cha omutsatira chitachoka.
Kugwesedwa mphwayi, kugonja, kusapenyetsetsa kudawagwera kwa wina aliyense.ochepa okha
adayang‟anira pamapazi pa mtanda wa Yesu. Ambiri mwa iwo anathawa nawasiya Ambuye okha.
Ndikudandaula kwakukulu mwa ophunzira ndi amayi ena adaona momwe thupi la Mbuye wawo
lidatengedwera ku manda! Ndipo pa tsiku loyamba, litatha sabata, amayi olimba mtimawa adaganiza
zopita ku kumanda, koma chowazizimutsa: m‟manda mudalibe kanthu! Yesu wauka ndipo iye yekha
adapita nakakumana nawo nanena nawo: ndauka!

Ataona ambuye awo wauka, onse okhulupilira adapita pamapazi ake namulambira. Atagwada pamaziwo
kusazidalira ndikusapenyetsetsa kudatha. Ponyadira kuuka kwa Yesu Khristu, zobetchera anakumana
nazo zidasanduka kukhala chipambano.
MATHELO
Kodi chinachitika ndi chani kwa anzeru amkummawa, ophunzira ndi azimayi amene anapita ku manda
tsiku loyamba la pasabata anaona mphanvu ndi ulamuliro ndi ulemelero wa Yesu?
Mphamvu ya chigonjetso inaonekera mwa Yesu, kupembedza kumaonetsera m‟mene ife tiliri mu
chikhulupiliro chathu mwa Mulungu wathu
Tikayika chidwi pa umunthu mphanvu ndi ulamiliro wa Mulungu, mudzamukonda, ndikumpembedza
ndipo moyo wanu udzasinthika
Ralph waldo emerson adanena mawu odziwika, “ timakhala chomwe tikupembedza” mumawu ena,
chomwe timachipembedza chimatipanga kukhala chizindikilo chathu.
Ophunzira owona zakusitha kwa zinthu Charles Darwin ananena kamodzi muzolemba zake: “chithu
chimodzi chochititsa chidwi ndi ntchito yanga m‟moyo mwanga inali ntchito yaza science. Kuchokela
ku ntchitoyi” adaonjezela, “sindidakhalepo chilili,” popeza ndichithu chokhacho chimapandisa moyo
wanga kukhalika.
Kodi ndizosatila zotani za ntchito ya za science idalinazo pa moyo wa Darwin?
Atafika zaka 30 darwin adapitiliza kulemba, “ ndakatulo….. zidandimvetsa kukoma, ndi
ndidasangalatsidwa ndi shakespeare…koma pano, kwa zaka zambiri… ndapeza zosasangaratsa
kundifunisa kusaza… maganizo anga asanduka kukhala ngati chopanga chachitsulo chopangila malamulo
potorera zazikulu za zowona. Kutayika uku ndikutayika kwa chimwemwe…ndidasanduka duwa lofota pa
zonse zamoyo kupatulako za science ( chomwe adaona kuti chidali choyipa).

Pano tionenso moyo wa munthu wina wanzeru wachikoka, Jonathan Edwards. Ali ndi zaka 19, Edwards
analemba:
Iyeyu anapeleka moyo wake kwa Ambuye Yesu Khritsu, analankhura mau, ndasiya zonse ndasankha
kuyenda ndi Yesu moyo wanga wonse, kukhulupilira iye ndikuzipeleka kwathunthu kwa Iye.
Patapita nthawi mmoyo mwake, Edwards adaziyang‟anira momwe adapangira chisankho chake,
kupembeza inali mbali imodzi la khalidwe lake, patapita zaka: Mzimu wake unadzadza ndi chiyero,
kuwala ndi ntendere. Mu mau ena, zidasanduza mzimu wake kukhala munda wamaluwa okongola

Amuna awiri aluso. Mmodzi anakhala “duwa lofota” ndipo wina nakhala “munda wamaluwa”.
Kupembedza ndi Chithu chomwe adasankha, ndipo chidawapanga kukhala anthu osiyana pamapeto.

KUYANG’ANILA NDI MAFUNSO

1. Tinganene bwanji kuti munthu wopembedza muchoona amabwerera kwa Ambuye mu njira ina?
2. Chimachitika ndi chani tikachitiRa umboni mphamvu ya Mulungu mukupembeza Iye?
3. Tanenani mawu a bukhu lopatulika anakusangalasani amaonetsa zotsatira ku moyo wa anthu
okhulupilira opembeza zoona?

AMEN
To Love is to share (KUKONDA NDIKUGAWA)

ULALIKI WACHISANU NDI CHIWIRI


(2 AKORINTO 5:14)
Nkhani ina yodabwisa ndinamvapo ndi ya Desmond Doss yemwe anabadwa ku Virginia mu 1919 ku
banja lina logwira ntchito, Doss anatengedwa ku khala nsilikali wa nkhondo mu dziko la united states mu
nyengo ya nkhondo yachiwiri ya dziko lonse lapansi. Pachifukwa cha chikhuupiliro Mulungu adamuuza
kuti asazanyamule mfuti, iye adaphunzira kukhala dotolo.

Kodi mungaganizeko kupita ku nkhondo opanda mfuti? Doss‟s adasautsidwa ndikuchitiridwa nkhanza
ndi anzinzake koma kwa akulu ake, komabe sadaleke kuyima pachikhulupilo chake chosanyamula mfuti.

Komabe, chilichonse chidasitha mu april 1945 pamene gulu la Doss amamenya nkhondo ya Okinawa,
khondo ya mwazi yayikulu ku pacific. Pakati pomenyana, ma Japanese adayima njii pa malo awo;
kumapeto, a battalion a America anabwerera.

Pobwerera, Doss anaona matupi a gulu lake atayarana pa bwalo la nkhondo ndipo anazindikira, alipo
wina ovulala. Adatsalira mbuyo, posalingalira kuopsya kwake, nathamangira pa malo owopsyawo,
ananyamura asilikali ovulala pakatunda nawatsitsira kumalo otetezeka ndi chingwe chomwe adapanga.

Pa maola khumi ndi awiri, adadziwa kuti padalibenso ena ovulala pamalopo, atachoka pamalopo,
Desmond Doss adapulumusa moyo wa anthu makhumi seveni ndi asanu!
Pachithu chodabwisachi Doss adapasidwa mphoto ya congressional medal ya ulemelero. Zaka zitapita,
adafunsidwa kuti mphanvu zimene anachita usiku umenewu zidachokela kuti. Yankho lake lidali lochepa:
nthawi iliyonse akamaliza kukasiya munthu ku malo otetezeka, amapemphera, “ ambuye, ndithandizeni
ndipeze mmodzi wina.”

Okondedwa achinyamata, ngati Desmond Doss, tili pa nkhondo yomwe anthu ochuluka akuvutika
komanso akupita ku chionongeko. Ntchito yathu ndichani? Tigwire ntchito mosatopa ndikupemphera, “
Ambuye, ndithandizeni ndipeze m‟modzi wina oti ndi muuze za chikondi chanu.”

Chikondi pa mulungu ndi anzathu chititengele ife kukagawana nawo uthenga wachipulumuso

KUKULA MU UZIMU
Panthawi iyi, ndikufuna ndigawane nanu zitsanzo za anthu amene adakanika kukhala chete ndi chikondi
chawo, adaganiza kugawana ndi ena za uthenga wabwino wa Yesu; anthu ngati inu ndi ine.

Chitsanzo choyamba chikupezeka pa Marko 1:40-42. Bukhu lopatulika likutiuza kuti:


Mamuna wina odwala khunyu anabwera kwa Yesu nagwada. Iye anampepha Yesu, “ muli ndi mphanvu
yondichiritsa, ngati mungafune kutero.” Yesu anamva chisoni naye. Anayika dzanja lake pa iye nanena,
“ndikufuna” wachiritsidwa” pompo nkhunyu lonse lidachoka ndipo anakhala bwino.

Mmene tikuonera mu nthano imeneyi, mamuna odwala nkhunyu anabwera kwa Yesu. Tiyeni
tikumbukile, achinyamata,nkhunyu limatchedwanso kuti chala cha Mulungu mu nthawi ya Yesu.
Mukudziwa chifukwa chake? OphunzitsI ndi olemba, alfonso ropero, adanena kuti nkhunyu idali nthenga
yowawa ndi ndiyonyasa, imene idalibe mankhwala.
Inde, achinyamata, Bamboyi anadza kwa Yesu adayenera kumwalira; komabe, mau a Mulungu akuti
yesu anayakhula, ndipo nthupi lake lidayela. Odwalayu yemwe adasaukitsidwa ndi nthenda yowopsyayi
anapeza machilitso mwa Yesu. Chinachitika ndi chani kenako? Tione mmene nkhani idathera:

Ndipo adamuchiza namusiya namuwuza iye, ona, usakanene kwa anthu, kazionetse wekha kwa
ansembe, ndikupeleka choziyeretsera monga Mose analamulira, nukhala umboni kwa iwo. Ndipo
adapita, nayamba kulengeza nanena zachilungamo za Yesu.

Yesu atachenjeza munthuyu, adamuuza pita, nanena, “ usakauze anthu za izi. Pita kauze mkulu wa
mpingo kuti ulibwino. Niutenge mphatso ku kachisi monga mose analamulira, ndipo aliyense azaziwa
kuti wachilitsidwa.”

Ndipo iye adakamba kwambiri za izi nawauza anthu ambiri, nafika poti Yesu anavutika kuyenda
momasuka mu mzinda. Adaleka kuyenda mimzinda, koma anthu adabwelabe kwaiye kuchokera kuli
konse. (Maliko 1:43-45).
Pamene wakhunyuyu adalandira machilitso, chotsatira chomwe anachita chinali kukapelekera umboni wa
omuchilitsa. Sadakhale chete! Adakamba za mchilitsi wake.

Chitsanso chachiwiri ndikufuna kukuonetselani chikupezekanso mu buku la Marko. Nkhani ya munthu


wina otchedwa chikhamu chaku gadarene idanenedwa. Nkhaniyi imakamba kuti mu dera la Gadara
mudali munthu yemwe anali ndi ziwanda. onaninso (Mark 5:1-20).

Ndikwabwino kutathauzira mau oti chikhamu, zikutathauza ziwanda 6,700 mutha kuona munthuyu
mukhaniyi anali ndiziwanda zambiri

Tsiku lina Yesu anapita ku Nyanja ya Gerasa ndicholinga chopeleka mpumulo kwa munthu wina osauka.
Modabwitsa, Yesu adagonjetsa mphanvu ya satana namuombola ku singa zamdima. Chinachitika
ndichani chotsatira?

Tiyeni tione tonse mayakho mu Marko:

Pamene Yesu ankakwera bwato, munthu adamupepha kupita naye. Koma Yesu sadalore iye. Komabe,
anati kwa iye, pita kwanu kwa abale ako nuwauze zambiri zomwe Mulungu wakuchitira ndi umbwino
wakuchitira iwe. Ndipo mzibamboyu anapita ku dera loyandikana ndi madera khumi otchedwa Decapolis
nayamba kuuza aliyense za zomwe yesu wamuchitira. Aliyense yemwe adanva za zochitikazi adali
odabwitsika. (Maliko 5: 18-20)
Kodi mwaona? Pamene chikhamu chaku Gerasa anamasulidwa ndi mphanvu ya yesu ndipo sadathe
kukhala chete. Iye, ngati wakhate, anapita nayamba kugawana ndi ena za zabwino zoposa zomwe yesu
wachita mmoyo mwawo!

Chitsanzo chachitatu
Ndikufuna ndikuonetseni pa Yohane 4:8-10. Pa mau amenewa tiwelenga za mzimayi osautsika ndi
wamanyazi ndi zammbuyo mwake. Tsiku lina lotetha, Yesu adapita kukatunga madzi ndipo kumeneko,
chifukwa anali otopa ndikuyenda, anakhala pansi napuma. Mzimayi wachifundo anabwera kuzatunga
madzi ndipo Yesu adamufunsa, “ chonde munganditungileko madzi ndimwe?” iye, monga mkazi
wachifundo, pozindikila kuti adamufunsa adali mu yuda, anati kwa iye: kodi inu, okhala muyuda,
mundifusa za madzi okumwa? Apa ndipamene yesu amene analenga zonse zopeleka madzi nanena
kwaiye: “sudziwa chomwe Mulungu afuna apelike kwa iwe, ndipo suziwa amene wakupepha madzi.
Udakadziwa, unakandifunsa madzi opeleka.” Verse 10

Ndipo mkazi osautsidwayu anapepha madzi a moyo kwa Yesu! Pamenepo, pachitsimepo, adakumana ndi
mphamvu yakukhululukidwa ndi yachipulumutso. Chosatira chidali chani? John 4: 28-30 likunena kuti:

Mzimayiyu anasiya mtsuko wake wamadzi nathamanga kubwelera ku mzinda, nakanena kwa anthu,
“bwelani muzaone munthu amene wanena zonse zomwe ndakhala ndikuchita! Kodi atha kukhala
mpulumutsi?” aliyense mu mzinda adapita kukaona Yesu.

Nzimayi wachifundoyi ngati odwala nkhunyu ndi waziwanda waku Gerasa, sadakhale chete. Pamene
anakumana ndi mphanvu yokhululukidwa anapita ndikukachitira umboni wa mpulumutsi wawo.

MATHELO
Okondedwa achinyamata, mau a Mulungu akuti chikondi cha Mulungu chidzadze mwaife. Pamene
chikondi cha Mulungu chadzadza mwa ife, sitingakhale chete, chifukwa kukonda kumatipangitda
kulalikira mau a Mulungu welengani ( 2 Akorinto 5:14)

Yesu, anakwela kupita kumwamba ndipo adalandiridwa mwachimwemwe ndi angelo. Pamene angelo
adamukweza posangalalira za kupambana kwake, ndipo mmodzi mwa iwo anafika kwa Yesu nafusa
mafunso osatilawa:

Kodi mwakhonza zotani zopitiliza ntchito munayamba pa dziko lapansi?

Mosakayika, Yesu adati:

Ndasiya zonse mmanja mwa a neneri.


Akuyenera kutenga uthenga kukauza ena za Yesu mpaka onse azaziwa choonadi.

Ndipo ngelo anafunsanso:


Nanga atalephera, mulibe njira ina?
Ambuye adayakha:

Ndilibenso njira ina.


Oh, achinyamata! Palibenso njira ina. Njira ndi yokhayo yaife kukachitira umboni za Yesu pa zomwe
watichitira ife. Chikondi cha Mulungu ndi anzathu chititengere kukagawana ndi anzathu mawu a
chipulumutso.

KUYANG’ANILA NDI MAFUNSO

1. Ndichiphunzitso chanji taphunzira pa nthano ya desmond Doss malingana ndi ntchito yosamala
ovutika anzathu?
2. Kodi chikondi chomwe tili nacho pa Mulungu, chititengele kuti poganizira ntchito watipatsa?
3. Ndichifukwa chiyani tisakhale chete pamene chikondi cha Mulungu chadzadza mwa ife?

AMEN
To Love is to wait (KUKONDA NDIKUDIKILA)

ULALIKI WACHISANU NDI CHITATU


(2 TIMOTEO 4:6-7)
Olemba wina ndi olalika, Max lucado, akutiuza nkhani yosutha moyo, yomwe inachitika patatha
chivomelezi chinagwedeza Armenia mu 1989- kudali ku gwedeza koti mu mphindi zinayi tidatha
kuononga dzikoli lonse ndikupha anthu okwana 30,000. Pathata chivomerezi choopsachi, bamboo wina
adathamanga ku school kukapulumusa mwana wake. Atafika, anawona sikulu itagwa, atayamba
kuyang‟ana mkati mwa miyala ndi zokugwazo, adakumbukira zomwe anamulonjeza mwana wake: “olo
pangachitike chotani, ndidzakhara nawe kulikonse uli.”

Moyendesedwa ndi lonjezoli, adapeza kalasi ya mwana wake nayamba kuchosa zokugwazo; makolo ena
anabwera nayamba kuyang‟ana ana awonso. Ambiri amene anabwera pamalopo, powona kukula kwa
kuonongekako, adanena naye: “mwachedwa” mukudziwa amwalira, palibe chingachitike”. Wa police
wina adamulangiza kuti asiye kuyang‟ana.

Koma bamboyi sadagonje: maola asanu ndi atatu atadusa, kenako maola khumi asanu ndi chimodzi,
makumi awiri ndikomalizira maola makumi atatu asanu ndi chimodzi. Manja ake adavulala ndipo
mphamvu zake zidatha, koma adakanabe kugonja. Ndipo mphindi izi zitatha anali ndi nkhawa yayikulu,
adachotsa mbali ina ya nkhoma ndipo adamva mawu a mwana wake.

Ndipo anakuwa, “armman! Arm!” ndipo mau anayakha, bambo wanga ndili pano! Ndipo mwanayu
nayakhula mau amtengo wapatali: ndidawauza ana ena kuti asadandaule, kuti ngati inu muli moyo,
mudzabwera kutipulumutsa ife, ndipo pondipulumutsa ine, nawo azapulumutsidwa nawo chifucha
munalonjeza ine kuti, pachilichonse mudzakhala nane kulikonse.

KUKULA MUUZIMU
Anyamata ndi atsikana, lonjezo lomweli lomwe bamboyi anapeleka kwa mwana wake lidanenedwanso
ndi Yesu, ndipo adati…. Ndizabwelanso ndi kudzatenga inu kwa ine ndekha, kuti komwe kuli ineko,
mukakhale inunso.” Kubwelanso kwachiwiri kwa Yesu ndi chiyembekezo chodala kwa okhulupilira
ndipo ndikuuzeni kuti mumabuku onse a chipangana chakale ndi chatsopano adzadza ndimalonjezano
akubwelanso kachiwiri kwa Yesu. Mwachisanzo pali zolemba zochitira umboni 1845 muchipangano
chakale ndi ma buku okwana khumi asanu ndi awiri opelekera umboni. Za kebweranso kwa Yesu
(Yohane 41:3; Tito 2:13-14).

Tsono, pamalemba 260 mu mabuku a chipangano cha chipangano chatsopano, pali malembo 318 ochitira
umboni kwa kubweranso kachiwiri ka Yesu, chomwe chiri, imodzi mwa malembo 30; 23 mwamabuku
27 muchipangano chatsopano akutipitisa ku chochitika cha chikuluchi; ndipo pa ulosi ulionse wa Yesu
Khristu pakubwera koyamba pali thenga wakubwela kwake kachiwiri.

Kubwelanso kachiwiri kwa Yesu kudzakwanirisa maulosi amene anatsara. Pakubwela kwake koyamba,
Yesu adali kapolo wamsautso. Kubwelenso kachiwiri, Yesu adzakhala mfumu ya mafumu yogonjetsa pa
Yesu anafika modzichepetsa. Pakubwelanso kachiwiri, Yesu adzabwela ndi gulu lake la nkhondo ku
mwamba ndipo adzabwera ndi ulemelero wake wonse.
Mu zaka zambiri, akhristu akhala akudikilira kukwanilitsidwa kwa lonjezo lomwe Yesu anapeleka
lobwelanso mu ulemelero ndi ufumu. Mmodzi mwa okhulupilika amene anadikila kubwelanso kwa Yesu
Paulo. Kumapeto kwa utumiki ndi moyo wake, mtumiki wa Mulungu adalemba:

Pakuti ndili mkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi yakumasuka kwanga yafika, 7 ndarimana
nako kulimbana kwa bwino, ndatsiliza njirayo, ndasunga chukhulupiliro; 8 cotsalira wandiikira
ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, wpweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo
ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anaconda maonekedwe ake. (2 Timoteo
4:6-8)

Paulo adayang‟ana mwachikondi pakubwelanso kachiwiri kwa yesu. Pakuyamba kwa utumiki wake wa
moyo wauzimu, pamene Yesu anakumana naye pa ulendo wake waku Damasco, munthu wabwino
wamulunguyu adakhazikika kuyembekeza. Chilimbikitso chake chidafika polemba kwa okhulupilira aku
athesalonika: tewerenge zomwe analemba pa(1 athesalonika 4:13-18)

Kodi mwazindikilapo chilimbikitso chomwe Paulo anapeleka pakubwelanso kwa Ambuye? Iye
adakhulupilira kuti Yesu adzabwela Paulo alimoyo! Pa ichi adanena:… kwa amene angakhare ndi moyo
mpaka kubwela kwa Yesu…..! Komabe, nthawi inadusa ndipo mtumiki Paulo adapitiliza kulalika
ndikugwira ntchito mosatopa pachifukwa cha mau abwino. Pokupita kwa nthawi sizidamuchepetsere
chikhulupiliro . Ndipo adalembanso izi: Tiwerenge .(1 Akorinto 15:51-52).

Pokutha kwa zaka mtumiki Paulo sadataye chikhulupiliro! Pamene tsiku limadutsa. Chikondi pa
kubwelanso kachiwiri kwa nkhristu chidakula ndi kukula mu mtima mwake! Chiyembekezo chake
chidapitiliriza kukula ndi nthawi osazilala! Pakutha kwamasiku ake, malinga ndi imfa yake yosathawika,
ndi chikhulupiliro ndi kuzipeleka adanena:

7 Ndalimbana ndikulimbana kwabwino. Ndatsiliza njirayo ndasunga chikhululpiliro, chotsalira


wandiikira ine korona. Wa chilungamo, amene Ambuye woweruza wolungama, adzandipatsa ine
tsiku lijaro; ndipo sikwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene amakonda maonekedwe ache .
(2 timoteo 4:6-8)

MATHELO
Kodi ndichifukwa chani chikhulipiliro cha mtumiki Paulo pakubwelanso kachiwiri kwa Yesu chidakula
popita kwa nthawi? Chifukwa anakonda ndikuyang‟anira chitsogolo pakubwelanso ka chiwiri kwa Yesu.
Achinyamata, Omwe amakonda Yesu amadikira.
Kumukonda mulungu ndikudikila mokhulupilika pakubwelanso kwake mu ulemelero ndi ufumu.

Lero ndikuyitanira inu kudikila ndi chikondi pakubwera kwa Yesu. ndikuyitanira inu kupepha Mulungu
atikhonzetsere pa tsiku lomwe yesu adzaonekere mmitambo yakummwamba.
Mulungu atithandize kukhala ndi mtima wakukhala wantchito mzake wa Mulungu
munthu olemela Benneth adali nawo, pa nkhani yotsatilayi.

Jill jones adalemba za munthu wolemela olemba mapepala a nkhani ku America dzina lake James Gordon
Bennet. Mu 1835 Bennett adayambitsa pepela la nkhani yotchuka yotchedwa The New York Herald. Iye
adali ndi nyumba zomangidwa bwino ziwirii ku paris, ndi malo ku france ndi bwato yomwe imayenda
ku Europe; ndipo analitso ndi nyumba zitatu ku united states, ngakhale sadakhale mu dzikomo kwa dzaka
10, koma adali ndi ogwira ntchito ku nyumba ili yonse omwe amakhala okonzekera kubwera mwa
dzidzidzi kwa Bennett.

Jones adalemba:
Nyumba iliyonse idali ndi ofunikira onse ogwira ntchito, okhonzekela kutumikila Bennett atafika
pakhomopo mozizimutsa: zokumwa zimasanjidwa, moto otethetsa umakhala oyatsa, ndi zofunda
zimayalidwa usiku uliwonse.

Umu ndimmene tikuyenera kukhalira: pakudikila, ndikuyang‟anira kubweranso kwa Yesu, chifukwa pa
nthawi iliyonse im, ne sitikuyembekeza Ambuye yesu khristu adzabwera ndi mphanvu ndi ulemelelo!

KUYANG’ANILA NDI MAFUNSO

1. Ndichifuwa chani mu chipangano chakale ndi chatsopano chadzadza ndipangano akubwelanso


kachiwiri kwa Yesu nkhristu?
2. Kodi ndi mphunziro lanji pa nkhani ya mtumiki Paulo watengapo potengela kubwelanso kwa
Yesu? Fotokozani mu mau anu chifukwa chani kudanenedwa kuti yemwe akonda amadikira.
3. Kodi tichitenge bwanji pa longezo lakubwelanso kwa Yesu?

AMEN
MA ULALIKIWA ATANTHAUZIDWA MU CHICHEWA
NDI
Evangelist
Hxson Malunga 0999312257
LIMBE SDA CHURCH

You might also like