You are on page 1of 1

YIMBA NDI MILOMO YAKOYI

(Victor Sodza)

1. Yimba chikondi cha Yesu Mbuyeyo

Anawombola’we ku zolemerazo

Ena sanazione zonse uzionazo

Yimbadi za Iyeyo ndi milomo yakoyi

2. Moyo wakupatsa wakusamalatu

E! Wakuvekadi iwe sinasowe izo’yi

Watedza iwenso pansi pa nthenga zake

Imbadi za iyeyo ndi milomo yako

3. Dzana suja unalira’we, Mayo!

Dzulo unalinso du! Pakukhumudwa iwe,

Yesu wakondwetsa’we ndipo wapatsa zonse

Yimbadi za Iyeyo ndi milomo yakoyi

You might also like