You are on page 1of 2

LIPOTI LA WOYANG’ANIRA DERA ATACHEZERA MPINGO

Nambala ya mpingo: 3228 Madeti amene mwachezera mpingo: MAY 09-14 2023
Dzina la mpingo: DWAMBAZI Mzinda: PAKATI Pulovinsi/boma: NKHOTAKOTA

Woyang’anira dera: LYNOCIE NASHO (SCO) Nambala ya dera: NB-5

Fotokozani mwachidule mzimu wa mpingowo ndiponso malangizo amene mwapereka kapena mmene mwaulimbikitsira:

Talimbikitsidwa kwambiri ndi changu chimene abale ndi alongo ochuluka omwe ndi okalamba anali kusonyeza potumikira Yehova pa mlungu
wonse'Tinalinso ndi nthawi yodziwana bwino ndi abale ndi alongo apabanja ngakhalenso omwe sali pabanja mwakutiitanira chakudya
chamasana ndi chamadzulo kunyumba kwawo.Ofalitsa ambiri amapereka malipoti awo mokhazikika mwezi uliwonse.Ofalitsa ampingowu
amakonda kwambiri misonkhano yakumapeto kwa mlungu . Ndi akulu takambirana kwambiri mfundo za od 7:14-17 ndicholinga chothandiza
ofalitsa kuzindikira ubwino wa misonkhano yamkati mwa mlungu ,yomwe inakonzedwa pofuna kulimbitsachikhulupiliro chathu ndi kukhala
atumiki oyrerera kugwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa mogwira mtima. Ndachita zimenezi chifukwa average ya misonkhano yamkati
mwamlungu ndichotsika.Ndawalimbikitsanso kutsatira njira zaukhondo kuti kuti nkhosa za Mulungu zizikhala zotetezeka ku majeremusi
akamachoka kuchimbudzi mwakusamba m'manja ndi sopo.Izi zilichoncho chifukwa sakhala ndi madzi komanso sopo nthawi ya misonkhano.
Ngakhale kuti akulu onse anayi ali ndi akaunti, awiri samakwanitsa kulowa pa akaunti chifukwa cha ukalamba. g 12/8/2003 (sopo)
(Lipotili litumizidwe ku ofesi ya nthambi mwamsanga. Wogwirizanitsa ntchito za akulu mumusiyire kope la lipotili n’cholinga choti akulu onse aliwerenge
komanso adzalikambirane pa msonkhano wawo wotsatira umene umachitika pakatha miyezi itatu.) S-303-CN 8/14

You might also like