You are on page 1of 6

Zilengezo Ndiponso Zofunika Kukumbukira

August 2023

ZOPITA KWA AKULU


1. Chikumbutso cha 2024: Pokonzekera chikumbutso cha 2024, zingachite bwino
kwambiri kuti muonenso malangizo amene ali m’buku la Wetani mutu 20 ndime 6 ndi 8,
posankha m’bale woti adzakambe nkhani komanso nthawi yochitira mwambowu.

2. Nkhani Yapadera ya 2024: Nkhani yapadera ya 2024 idzakambidwa mlungu wa March


11, 2024. Nkhaniyi ili ndi mutu wakuti, “Kugonjetsa Imfa, mwa Kuukitsa Akufa!”. Mipingo
imene idzakhale ndi mlungu wapadera kapena msonkhano wadera, mlungu woyambira
March 11, ndiye kuti nkhani yapadera ingadzakambidwe mlungu wa March 4. Ngati mpingo
udzakhale ndi mlungu wapadera komanso msonkhano wadera pa wiki imeneyo ndiye kuti
nkhani ya onse idzakambidwe mlungu woyambira February 26.

3. Bungwe la akulu lililonse lingasankhe kuti mkulu wa mumpingomo kapena mlendo


wochokera mpingo wina adzakambe nkhani yapaderayi. Nkhani yojambula yomwe
idzapezeke pa JW Stream ingadzagwiritsidwe ntchito ndi ofalitsa komanso anthu achidwi
amene sadzakwanitsa kulumikizidwa ku nkhani yokambidwa ku Nyumba ya Ufumu. Autilaini
ya nkhani yapaderayi ya chaka cha 2023 (S-123-23), pamodzi ndi zinthunzi, vidiyo komanso
zinthu zonse zomwe zidzagwiritsidwe ntchito pa nkhaniyi, ziyamba kupezeka pa JW Hub
posachedwapa.

4. Nkhani ya Onse Na 132: Autilaini ya nkhani yapadera ya 2024 idzakhala ya nkhani ya


onse nambala 132 koma yokonzedwanso. Yomwe ili ndi mutu wakuti “Kugonjetsa Imfa, mwa
Kuukitsa Akufa!” Simukuyenera kupatsa munthu wina kuti akambe autilaini imeneyi
kuyambira pa September 1, 2023. M’tsogolomu, autilaini ya nkhani ya onse nambala 132
idzalowedwa m’malo ndi autilaini ya nkhani yapadera ya 2024.

5. Malangizo Othandiza Amayi Oyembekezera (S-407) Komanso Mfundo Zofunika


Kukumbukira Tikafunika Thandizo la Opaleshoni Kapena la Matenda a Khansa (S-
401): Fomu ya Malangizo Othandiza Amayi Oyembekezera yokonzedwanso yayamba
kupezeka pa JW Hub. (sfl mutu. 11 ndime 2) Kuwonjezera pamenepo, fomu yatsopano
yotchedwa Mfundo Zofunika Kukumbukira Tikafunika Thandizo la Opaleshoni Kapena la
Matenda a Khansa yaikidwanso pa JW Hub. Chonde, muzipereka malangizo amenewa kwa
ofalitsa mukangodziwa kuti akufunikira thandizo la opaleshoni kapena la matenda a khansa.
M’malangizo amenewa, muli mfundo zina zimene zingakhale zothandiza pa zokambirana
za wodwalayo ndi dokotala komanso ndi zothandiza wodwala kulumikizana ndi abale a
m’Dipatimenti Yolankhula ndi a Chipatala kuti amvetse mfundo zina, komanso kulandira
thandizo ngati pangafunike kutero.

6. Ntchito yokonzetsa zinthu pa Nyumba ya Ufumu, komanso kuona kuchuluka kwa


ndalama zimene bungwe la akulu likuona kuti ndi zoyenera kusunga: Kuti mukhale ndi
ndalama zokwanira pa mpingo wanu zosamalira zowonongedwa pa mpingo komanso pa
Nyumba ya Ufumu, mabungwe a akulu komanso makomiti oyang’anira Nyumba ya Ufumu
ayenera kukhazikitsa ndalama zimene akuona kuti ndi zoyenera kusunga. (Malangizo a
Kayendetsedwe ka Ndalama za Mpingo [S-27b], ndi. 8; [S-27c], ndi. 9; Malangizo a
Kayendetsedwe ka Ndalama za Komiti Yoyang’anira Nyumba ya Ufumu [S-42b], ndi. 10; [S-
42c], par. 11.) Kuti mudziwe ndalama zomwe mungamasunge, chitani zotsatirazi:

S-147-23.08-CN
(1) Kuti mudziwe ndalama zomwe mungamasunge, phatikizani "Ndalama zonse
zogwiritsidwa ntchito" [e] zomwe zimalembedwa pa fomu ya Lipoti la Pamwezi
Losonyeza Mmene Ndalama za Mpingo Zayendera (S-30) za miyezi 12 yomwe
yapita. (Musaphatikize ndalama zomwe mwalemba mu Lipoti la Pamwezi Losonyeza
Mmene Ndalama za Mpingo Zayendera zomwe ndi ndalama (1) zomwe mpingo
unagamula kuti ziperekedwe ku ofesi ya nthambi kuti zithandize pa ntchito ya padziko
lonse poona kuti ndalama zonse zimene mpingo ulinazo zachuluka kuposa ndalama
zimene bungwe la akulu likuona kuti ndi zoyenera kusunga, (2) zolipilira ntchito
yokonzanso Nyumba ya Ufumu kapena kukonza zinthu zina zomwe ndalama yake
inachita kutumizidwa kuchokera ku ofesi ya nthambi) Mogwirizana ndi Wetani, mutu
10 komanso Malangizo a Kayendetsedwe ka Ndalama za Mpingo (S-27), ndalama
zowonongedwazo zingaphatikize:
• Ndalama zogwiritsidwa ntchito pa nthawi imene woyang’anira dera
akuchezera mpingo, Ndalamazo zingaphatikizepo zimene anagulira
chakudya, mapepala olembapo zinthu, ndalama zimene anagwiritsa ntchito
poyendera ndiponso ndalama zimene anagwiritsa ntchito pa zinthu zina
zochepa zaumwini.
• Kubwezera ndalama za thiransipoti zimene okamba nkhani amene amabwera
ku mpingo wanu agwiritsa ntchito (kuphatikizapo ndalama za thiransipoti
zimene abale amene achita kutumizidwa ndi ofesi ya nthambi).
• kusindikiza mawu pa mapepala oitanira anthu ku misonkhano, kugula zinthu
zogwiritsa ntchito pamene mpingo ukupanga ulaliki wa m’malo opezeka anthu
ambiri.
• Ngati Nyumba ya Ufumuyo imagwiritsidwa ntchito ndi mpingo umodzi wokha:
Ndalama zowonongedwa pokonzetsa Nyumba ya Ufumu: (1) ndalama
zolipilira madzi, magetsi, intanet kapena zonse zowonongedwa pogwiritsa
ntchito kapena kukonzetsanso Nyumba ya Ufumu, (2) ndalama zimene
wophunzitsa anthu kasamaliridwe ka Nyumba ya Ufumu amagwiritsa ntchito
popita ndi kubwera ku mpingo, monga ndalama zoyendera ndi zogwiritsa
ntchito potumiza ndi kulandira makalata (3) ndalama zowonongedwa
pogwiritsa ntchito komanso kukonza nyumba zina zimene zili pa Nyumba ya
Ufumu.
• Ngati Nyumba ya Ufumuyo imagwiritsidwa ntchito ndi mipingo yoposa iwiri,
amene amalipira zinthu zowonongwedwa pa Nyumba ya Ufumu ndi komiti
yoyang’anira Nyumba ya Ufumu.
• Chigamulo cha ndalama zotumizidwa ku ofesi ya nthambi ku ntchito ya pa
dziko lonse.
(2) Gawani mtengo wa ndalama zonse zowonongedwa zomwe mwaphatikiza ndipo
gawani ndi 12. Mtengo umene mupezewo ukuimira avireji ya ndalama
zowonongedwa mwezi ndi mwezi.
(3) Mungasankhe kuwirikiza kawiri kapena katatu (mtengo wa avireji ya mwezi ndi mwezi
yomwe mwapezayo) kuti muone ndalama zomwe mukufunika kumasunga.
Mwachitsanzo:
Chitani izi poyamba: Ndalama zonse zowonongedwa pa miyezi 12: 12,000
Chitani izi kachiwiri: Gawani mtengowo ndi 12: 1,000
Pomaliza: Wirikizani katatu, izi ndi ndalama zomwe mungamasunge: 3,000

S-147-23.08-CN
7. Nchifukwa chiyani ndi zofunika kukhazikitsa ndalama zofunika kumasunga? (1)
zimathandiza kudziwa ngati mpingo kapena komiti yoyang’anira Nyumba ya Ufumu
ikuyenera kulipira ntchito yokonzetsanso pa Nyumba ya Uufmu kapena ngati ndalamazo
ziyenera kuchokera ku ofesi ya nthambi. (sfl, mu. 21, ndi. 9) (2) kukhazikitsa mtengo wa
ndalama zomwe mpingo ukuyenera kumasunga zimathandiza kuti akulu apange chigamulo
cholondola cha ndalama zomwe angamatumize mwezi ndi mwezi ku ntchito ya pa dziko
lonse ku ofesi ya nthambi. Ngati mpingo sungakwanitse kulipira zonse zowonogedwa pa
ntchito yokonzetsa pa Nyumba ya Ufumu, komanso kulipira zinthu zina za mwezi ndi mwezi
komanso zowonongedwa pa nthawi ya kuchezeredwa ndi woyang’anira dera, zingafunike
kuti akulu akonzetse chigamulo cha zopereka ku ntchito ya pa dziko lonse . — Malangizo a
Kayendetsedwe ka Ndalama za Mpingo (S-27) ndi. 19.

8. Chigamulo cha Ndalama Zimene Zimaperekedwa Mwezi ndi Mwezi Pothandiza


Ntchito Yapadziko Lonse: Chigamulo cha ndalama zimene zimaperekedwa mwezi ndi
mwezi chomwe chatchulidwa mu zilengezo zopita kumipingo zikutengera zimene ofesi ya
nthambi inaona kuti wofalitsa aliyense angakwanitse kumapereka mwezi ndi mwezi.
Tsamba lomwe lili pa JW Hub likusonyeza zopereka zimene ofalitsa angapereke mwezi ndi
mwezi ndipo mungapezeponso linki ya chilengezo chino ndipo zingathandize kuti mudziwe
chigamulo chimene mungamapereke mwezi ndi mwezi. Mungachite taimusi chiwerengero
cha ofalitsa amene amalalikira, ndi ndalama zimene wofalitsa angakwanitse kupereka
mwezi ndi mwezi zimene ofesi ya nthambi inasonyeza pa JW Hub. Bungwe la akulu
likuyenera kuganizira zimene mpingo ukukwanitsa kuchita zokhudza kupereka ndalama
mwachitsanzo, ndalama yopita ku Komiti Yosamalira pa Nyumba ya Ufumu. Kenako
n’kuona ngati mpingo ungakwanitse kupereka ndalama imene mukupeza pambuyo
popanga taimusi kapenanso ngati pangafunike kuwonjezera. Ngati zitaoneka kuti kupereka
ndalamayi kungakhale mtolo wolemetsa kwa abale ndi alongo, mungachite bwino kusankha
ndalama yocheperako kuti muzitumiza ku ofesi ya nthambi. Kuchuluka kwa ndalama zimene
bungwe la akulu lingagwirizane kuti ziziperekedwa, mungadzadziwitse mpingo kuti
uvomereze ngati zili zololeka kumapereka ndalamazo. Dziwani kuti chigamulo cha ndalama
zimene mpingo ungavomereze chiyenera kumaperekedwa mwezi ndi mwezi osati
kudzapereka zonse pamodzi kumapeto kwa chaka chautumiki.—Onani mawu akumapeto
mu fomu ya Malangizo a Kayendetsedwe ka Ndalama za Mpingo (S-27) kuti akuthandizeni
kudziwa mawu amene mungalembe okhudza chigamulo

9. Pulogalamu ya Mwezi ndi Mwezi ya JW Broadcasting: Takonda kukumbutsa akulu za


malangizo a buku la Wetani mutu 21 ndime 41: “Ngati pa Nyumba ya Ufumuyo
pamasonkhana mipingo ingapo, zingakhale bwino kuti anthu a m’mipingo yonseyo amene
alibe intaneti azionerera pulogalamuyi pa nthawi imodzi yomwe Nyumba ya Ufumuyo
sigwiritsidwa ntchito. Popeza kuonerera pulogalamuyi si mbali ya misonkhano ya mpingo,
palibe chifukwa chotsegulira kapena kutsekera ndi pemphero. Anthu ochotsedwa kapena
odzilekanitsa nawonso angathe kubwera pa Nyumba ya Ufumu kudzaonerera nawo
pulogalamuyi. Anthu onse amene angabwere kudzaonerera pulogalamuyi akuyenera
kuvala mofanana ndi mmene amavalira kumisonkhano ya mpingo”. Kungakhale kusonyeza
chikondi kugwiritsira ntchito makonzedwe amenewa, ngakhale patakhala kuti ndi anthu
ochepa chabe amene sangathe kuonera kunyumba zawo. Woyang’anira magulu akhoza
kufunsa ofalitsa ngati angakonde kuonera pulogalamu mwezi uliwonse kenako akhoza
kudziwitsa bungwe la akulu za mayankho awo.

10. Lipoti la Mmene Mpingo Ukuyendera (S-10): Tikukumbutsa akulu kuti adzatumize
fomu ya Lipoti la Mmene Mpingo Ukuyendera (S-10) la chaka cha utumiki cha 2023
pasanadutse pa September 20, pogwiritsa ntchito webusaiti ya JW Hub. Mipingo imene ilibe

S-147-23.08-CN
maakaunti ikhoza kupempha woyang’anira dera wawo kuti adzathandize kutumiza lipoti
lawo, kapena ingatumize pogwiritsa ntchito SMS ku nambala iyi: 84 102 0030.

11. Kuchitira Lipoti Ngozi pa Nyumba ya Ufumu Komanso Malo ena Ochititira Zinthu
Zauzimu: Tikukumbutsa akulu onse kufunika kwa kufufuza mosamala zimene zachititsa
ngozi pamene akudzaza molondola fomu ya Lipoti Lonena za Mavuto a Mwadzidzidzi (TO-
5) nthawi zonse pamene pachitika ngozi pa malo aliwonse olambirira. Cholinga cha kufufuza
zomwe zachititsa ngozi komanso kudzaza fomuyi ndi chofuna kuteteza onse osonkhana
komanso kupeza njira yakuti ngozi ya mtundu umenewo isadzachitike mtsogolo. Pa
chifukwa chimenechi, tikupempha akulu onse kuti nthawi zonse aziona malangizo komanso
mavidiyo amene akupezeka pa JW Hub kuti aone mmene angafufuzire moyenerera zomwe
zachititsa ngozi. Pambuyo pake dzazani fomu ya TO-5 ndipo tumizani ku Setor de Gestão
de Risco ku nthambi, pambuyo pa ngoziyo. Mungapeze malangizo a mmene mungafufuzire
zomwe zachitisa ngozi komanso kudzaza fomu ya TO-5 pa JW Hub popita pa:

• MADOKYUMENTI/ Mavidiyo
• Mmene mungafufuzire pakagwa mavuto a mwadzidzidzi
• Mmene mugalembere Lipoti Lonena za Mavuto a Mwadzidzidzi (TO-5)
• MADOKYUMENTI/ Mafomu
• Instruções para Preencher o Relatório de Incidente de Risco (TO-5i)
Chipwitikizi

ZOPITA KU MAKOMITI A UTUMIKI WA MPINGO


1. Ntchito Yapadera Padziko Lonse M’mwezi wa September 2023: Chonde, ganizirani
zokhudza njira zimene mpingo wanu ungadzachite kuti udzakwanitse kulalikira anthu ambiri
pa ntchito yapadera imene tidzagwire m’mwezi wa September.
ZOPITA KWA OGWIRIZANITSA MABUNGWE A AKULU
1. Zilengezo Zopita Kumipingo: Onetsetsani kuti zilengezo zopita kumipingo
zalengezedwa pa msonkhano wotsatira wa mkati mwa mlungu ndipo kenako zikaikidwe pa
bolodi la mpingo kwa mwezi wathunthu.

2. Chigamulo cha Ndalama Zimene Zimaperekedwa Mwezi ndi Mwezi Pothandiza


Ntchito Yapadziko Lonse: Ngati bungwe la akulu lagwirizana kuti pakhale chigamulo cha
ndalama zimene zingamaperekedwe mwezi ndi mwezi, mogwirizana ndi chilengezo chopita
ku mabungwe a akulu, ndiye kuti chilengezocho chidzaperekedwe pa nthawi imene
mukulengeza zilengezo zopita kumpingo. Kapena mungadzadziwitse mpingo kuti
chigamulo chidzaperekedwa mlungu wotsatira.

ZOPITA KWA ALEMBI


1. Chigamulo cha Ndalama Zimene Zimaperekedwa Mwezi ndi Mwezi Pothandiza
Ntchito Yapadziko Lonse: Pambuyo poti chigamulo chomwe chafotokozedwa mu
zilengezo zopita kwa akulu chavomerezedwa ndi mpingo, chonde onetsetsani kuti
chigamulocho chaperekedwa kwa mtumiki woona za ndalama. Ndalama zimene
zizitumizidwa mwezi uliwonse, zizisonyezedwa pa Fomu Yosonyeza Ndalama Zotumizidwa
(TO-62) yomwe ili pa JW Hub, pa nzera wolembedwa kuti, “Zothandizira pa Ntchito
Yapadziko Lonse (Zimene munagwirizana.)”
ZOPITA KWA OYANG’ANIRA UTUMIKI
1. Ntchito Yapadera Padziko Lonse M’mwezi wa September, 2023: Chilengezo
chokhudza zomwe mpingo wakonza mmene ntchitoyi yapaderayi idzagwiridwire, chiyenera
S-147-23.08-CN
kudzaperekedwa pamisonkhano yamkati mwa wiki, pa wiki yoyambira August 21, 2023, pa
nkhani yakuti, “Ntchito Yapadera Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu September!”

2. Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso cha 2024 Ndiponso Nkhani Yapadera:


Pokonzekera ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso cha 2024 ndi nkhani yapadera, mpingo
uliwonse utumize mapempho awo pofika pa Lolemba, September 18, 2023, ndipo
mungagwiritse ntchito nambala iyi 7964 kapena chizindikiro ichi mi24. Ngati mpingo wanu
uli ndi ofalitsa amene anali m’kagulu kapena timagulu timene tinkasamalidwa ndi mipingo
ina, mukuyenera kuphatikizaponso chiwerengero cha ofalitsa amenewa.

KWA WOYANG’ANIRA KAGULU KA UTUMIKI WAKUMUNDA


1. Makalasi a kuwerenga: Mu chaka chautumiki cha 2024, woyang’anira madera akhala
akulimbikitsa makalasi a kuwerenga. Pamene mukukonzekera kuchezeredwa ndi
woyang’anira dera, ganizirani za zomwe mungachite pothandiza ena kuphunzira kuwerenga
molondola mu gulu lanu. Kuti mudziwe bwino luso la kuwerenga funsani mwachinsinsi mitu
ya mabanja kapena pamene mukugwira ntchito yolalikira limodzi ndi abale mu utumiki
wakumunda. Woyang’anira dera adzakufunsani kuti mumupatse ziwerengero zotsatirazi:

• Ndi anthu angati amene sadziwa kuwerenga m’chinenero cha mpingo kapena
zofalitsa zogwiritsidwa ntchito pa misonkhano ya mpingo. Phatikizani ofalitsa, ana
amene amapita ku sukulu komanso onse amene amapezeka pa misonkhano ya
mpingo mokhazikika.

• Ndi anthu angati omwe akufunika kukulitsa luso lawo la kuwerenga.


Phatikizani ofalitsa, ana amene amapita ku sukulu komanso onse amene
amapezeka pa misonkhano ya mpingo mokhazikika. Phatikizani amene
amavutika kuwerenga, ‘kuwerenga momveka bwino komanso mosalakwitsa.’,
‘kutchula mawu alionse molondola’, kapena “kuwerenga mogwira mtima”. —
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso, phunziro 5; Pindulani, tsamba 26,
ndime 2.

KWA WOYANG’ANIRA UTUMIKI NDI MAGULU A CHINENERO CHAMANJA


1. Baibulo la Dziko Latsopano mu Chinenero Chamanja cha Moçambique: Mothandi-
zidwa ndi m’bale amene amapanga apudeti JW Box, chonde tsimikizani kuti wapanga
apudeti JW Box ndipo ndi zotheka kupeza buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu komanso
zofalitsa zina mu njira zamakono.

KWA WOYANG’ANIRA KAGULU KA UTUMIKI WAKUMUNDA KU MIPINGO NDI


MAGULU A CHINENERO CHAMANJA

1. Baibulo la Dziko Latsopano mu Chinenero Chamanja cha Moçambique: Onetsetsa-


ni kuti ofalitsa onse mu kagulu kanu akudziwa za zofalitsa zatsopano ndipo thandizani
amene akufuna zofalitsazi kuti akhale nazo.

S-147-23.08-CN
Zilengezo Ndiponso Zofunika Kukumbukira
August 2023

ZOPITA KUMIPINGO
1. Ntchito Yapadera Padziko Lonse M’mwezi wa September 2023: Monga m’mene
chilengezo cha m’buyomu chinanenera, m’mwezi wa September 2023, tidzakhala ndi
ntchito yapadera padziko lonse yogawira magazini a Nsanja ya Olonda Na. 2 2020, ya mutu
wakuti; “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? Ofalitsa amene akufuna kudzachita upainiya
othandiza m’mwezi wa September 2023 ali ndi mwayi wodzachita upainiya wa maola 15
kapena 30. Mipingo idzapindula kwambiri ngati akulu adzakhale patsogolo kuchita khama
pa ntchito imeneyi. —Aheb. 13:7.

2. Chikumbutso cha 2024: Lamlungu pa March 24, 2024, tidzachita mwambo wa


Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. (Luka 22:19) Pa mlungu umeneyi, sitidzakhala ndi
misonkhano ya kumapeto kwa mlungu. Kuwonjezera pamenepo, dziwani kuti Chikumbutso
cha chaka cha 2025 chidzachitika pa Loweruka, April 12, 2025. Ndipo Chikumbutso cha
chaka cha 2026 chidzachitika pa Lachinayi, April 2, 2026.

3. Nkhani Yapadera ya 2024: Pofuna kuti tidzayembekezere ndi chidwi Chikumbutso cha
2024, nkhani yapadera idzakambidwa mlungu woyambira March 11, 2024. Mipingo yomwe
idzakhale ndi msonkhano wadera kapena mlungu wapadera, pa wiki yoyambira March 11,
ndiye kuti nkhani yapadera idzakambidwa kutatsala mlungu umodzi.

4. Chigamulo cha Mwezi ndi Mwezi Chothandiza pa Ntchito Yapadziko Lonse: M’chaka
cha utumiki chikubwerachi, chigamulo chidzaperekedwa ku mpingo chokhudza ndalama
zimene zingamaperekedwe pothandiza pa ntchito ya padziko lonse. Ofesi ya nthambi
imagwiritsa ntchito ndalamazi pothandiza pa zinthu zosiyanasiyana zomwe zimathandiza
mipingo. Zinthu zake ndi monga, kukonzanso komanso kumanga Nyumba za Ufumu, Malo
a Misonkhano, kuthandiza pa zinthu zadzidzidzi zomwe zingachitike pa nyumba za gulu la
Mulungu kuphatikizapo ngozi za m’chilengedwe, ngozi za moto, kubedwa kwa zinthu,
kuwonongedwa kwa katundu wa gulu ndi anthu achiwawa komanso kuthandiza mipingo pa
zinthu zamakono komanso zinthu zina zofanana ndi zimenezi. Ndalamayi imagwiritsi-
dwanso ntchito pothandizira mayendedwe a abale amene akuchita utumiki wa nthawi zonse
amene akufuna kukachita nawo msonkhano wamayiko. [Ngati bungwe la akulu lagwirizana
kuti pakhale chigamulo cha ndalama zimene zingamaperekedwe, mogwirizana ndi
chilengezo chopita ku mabungwe a akulu, ndiye kuti chilengezocho chikuyenera
kulengezedwa panopa. Kapena mungadziwitse mpingo kuti chigamulo chidzaperekedwa
wiki yotsatira.]

5. Baibulo La Dziko Latsopano mu Chinenero Chamanja cha Moçambique: Monga


mbali yotulutsa pang’onopang’ono Baibulo la Dziko Latsopano mu Chinenero Chamanja
cha Moçambique, ndife osangalala kukudziwitsani kuti vidiyo ya Uthenga Wabwino wa
Mateyu tsopano ukupezeka pa JW Libray Sign Language komanso pa jw.org. kuyambira
tsopano buku latsopanoli liyenera kugwiritsiridwa ntchito pa misonkhano yampingo
komanso mu utumiki wakumunda. Tikupezerapo mwayi oyamikira zopereka zanu zaufulu
za ntchito ya padziko lonse zimene mukupereka mowolowa manja pothandiza ena
kuphunzira Baibulo.

S-147-23.08-CN

You might also like